‘Mangirirani Nyumba Yanu’
1 Mosakayika, moyo wa banja ukunyonyotsoka m’fuko lililonse kuzungulira dziko lonse lapansi. Dziko la Satana likumwerekera m’chinyengo ndi chisembwere. (1 Yoh. 5:19) Zimenezi zikugogomezera kufunika kwa ‘kumangirira nyumba yathu’ mofulumira ndi kuphunzitsa ena mmene angamangirenso zawo.—Miy. 24:3, 27.
2 Mapulinsipulo a Baibulo Nchitetezo: Chinsinsi cha chimwemwe chenicheni cha banja chimapezeka mwa kugwiritsira ntchito mapulinsipulo a Baibulo. Choonadi champhamvu chimenechi chimapindulitsa aliyense m’banja m’mbali zonse za moyo. Banja limene limawagwiritsira ntchito lidzakhala lachimwemwe ndipo lidzakhala ndi mtendere wa Mulungu.—Yerekezerani ndi Yesaya 32:17, 18.
3 Mapulinsipulo amene angatithandize kumanga nyumba zathu alongosoledwa mwachidule m’buku latsopano lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. Mutu uliwonse umatha ndi bokosi lophunzitsa limene limagogomezera mapulinsipulo amene a m’banja afunikira kukumbukira. Ochuluka a mabokosi ameneŵa amayamba ndi funso lakuti, “Kodi mapulinsipulo a Baibulo awa angatithandize motani . . . ?” Zimenezi zimasonyeza maganizo a Mulungu kotero kuti tikhale ndi maganizo ake pankhani imene tikukambitsirana.—Yes. 48:17.
4 Lidziŵeni bwino bukulo. Phunzirani kupeza mapulinsipulo amene angakhale othandiza pamene mavuto osiyanasiyana abuka. Bukulo lili ndi nkhani zonga izi: zimene munthu ayenera kufuna mwa munthu amene akufuna kukwatirana naye (mutu 2), makiyi ofunika amene amatsegula khomo la chimwemwe chokhalitsa cha mu ukwati (mutu 3), mmene makolo angalerere achinyamata awo kukhala achikulire athayo ndi oopa Mulungu (mutu 6), mmene mungatetezerere banja ku zisonkhezero zowononga (mutu 8), mapulinsipulo othandiza mabanja a kholo limodzi kupambana (mutu 9), thandizo lauzimu ku mabanja osautsidwa ndi uchidakwa ndi chiwawa (mutu 12), zimene mungachite ngati zomangira za ukwati zili pafupi kuduka (mutu 13), zimene mungachite kuti mulemekeze makolo okalamba (mutu 15), ndi mmene munthu angamangire mtsogolo mokhalitsa mwa banja lake (mutu 16).
5 Ligwiritsireni Ntchito Mokwanira Buku Latsopanoli: Ngati simunaliphunzire kale pamodzi monga banja buku la Chimwemwe cha Banja, bwanji osatero? Ndiponso, nthaŵi zonse banja lanu likakumana ndi mavuto kapena zothetsa nzeru zatsopano, pendani mitu m’bukuli imene imanena za zimenezo, ndipo mwapemphero lingalirani mmene mungagwiritsire ntchito uphunguwo. Ndiponso, m’March, dzigaŵireni nthaŵi yaikulu ya utumiki wakumunda kuti mukayese kugaŵira Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja kwa anthu ambiri ndithu.
6 Mabanja amene amadzipereka mwaumulungu adzalimbitsidwa ndi kumangiriridwa mwauzimu ndipo adzakhala okonzekera bwino kulimbana ndi ziukiro za Satana. (1 Tim. 4:7, 8; 1 Pet. 5:8, 9) Tikuthokoza chotani nanga kuti tili ndi malangizo aumulungu ochokera kwa Myambitsi wa banja!