North America Adzakhala ndi Misonkhano ya Mitundu Yonse ya 1998
Monga mwa chilengezo choperekedwa pa Loŵeruka, October 5, 1996, pamsonkhano wapachaka wa Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, Bungwe Lolamulira likulinganiza kukhala ndi misonkhano ya mitundu yonse mu 1998. Limodzi ndi misonkhano yachigawo ya nthaŵi zonse, kudzakhala misonkhano ya mitundu yonse ingapo ku North America limodzinso ndi mu Afirika, Asia, Europe, Latin America, m’dera la Caribbean, ndi South Pacific.
Ingapo ya misonkhano yapadera imeneyi idzachitikira ku North America, ndipo nthumwi zochokera kumbali zonse za dziko lapansi zidzaitanidwa. Ndiponso, tingayembekezere kukhala ndi amishonale pamisonkhano ya mitundu yonse imeneyi. Amishonale ndi ena omwe akhala mu utumiki wapadera kumaiko akutali kwa zaka zosachepera zitatu ndipo ali ndi ziyeneretso adzaitanidwa kukapezeka pa umodzi wa misonkhano imeneyi ku dziko lakwawo kapena lapafupi ndi kwawo.
Tidzakudziŵitsani ponena za madeti, malo, ziyeneretso za nthumwi, zofunika kwa nthumwi za kwina, ndi zina zofunika. Mwaŵi udzaperekedwa kwa nthumwi zingapo za ku United States wokapezeka pamisonkhano ya mitundu yonse m’maiko ena. Ofalitsa ofuna kudzalembetsa kukhala pakati pa nthumwi zosankhidwa angayambe kusunga ndalama kuti akapezeke pazochitika zapadera zimenezi. Nthambi idzadziŵitsa mipingo za mzinda wa msonkhano wa mitundu yonse kumene ofalitsa adzaitanidwa. Adzauzidwa za madeti ndi makonzedwe omwe akupangidwa osankhira nthumwi.