Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/97 tsamba 7-8
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
km 3/97 tsamba 7-8

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu March: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. April ndi May: Makope a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mu utumiki wa mkati mwa mlungu ndi m’gawo lofoledwa kaŵirikaŵiri, mungagwiritsire ntchito brosha lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? June: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Sumikani maganizo pa kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba.

◼ Woyang’anira wotsogoza kapena wina wosankhidwa ndi iye ayenera kuŵerengera maakaunti a mpingo pa March 1 kapena mwamsanga ndithu pambuyo pake. Mutachita zimenezi perekani chilengezo ku mpingo.

◼ Nkhani yapoyera yapadera ya m’nyengo ya Chikumbutso chaka chino idzaperekedwa pa Sande, April 6 m’mipingo yambiri. Nkhaniyo ili ndi mutu wakuti “Khalani Oyera pa Zodetsa za Dziko.” Tonsefe tiyenera kupezekapo, ndipo tiyenera kuthandiza okondwerera amene anabwera ku Chikumbutso kuti adzapezekepo pankhaniyi. Zimene tidzamva ndithudi zidzatichititsa kutsimikizanso mtima za kukondweretsa Mulungu.

◼ Kuti tipindule ndi maphunziro a mpingo m’buku la Munthu Wamkulu, chonde ŵerengani zitsogozo zabwino kopambana zopezeka patsamba 1 la Utumiki Wathu Waufumu wa September 1992. Nkhaniyo imafotokoza mmene tingakonzekerere phunziro lililonse ndi kachitidwe ka Phunziro la Buku la Mpingo. Ochititsa maphunziro ndi onse opezekapo adzapindula mwa kupenda chidziŵitsochi.

◼ M’chitaganya chilichonse, panthaŵi zosiyanasiyana pachaka, pamakhala maholide akudziko pamene ana samapita kusukulu ndi pamene kumakhala nthaŵi yopuma pantchito yakuthupi. Ameneŵa amapereka mpata wabwino kwambiri woti mpingo ukhale ndi phande lowonjezereka mu utumiki wakumunda. Akulu ayenera kudziŵiratu pamene mpata umenewu udzaoneka ndi kudziŵitsa mpingo pasadakhale za makonzedwe amene akupangidwa kaamba ka umboni wa kagulu panthaŵi za maholide.

◼ Tamva kuti m’mipingo ina, misonkhano imasinthidwa ndipo nthaŵi zina kuichotserapotu chifukwa cha maliro kapena zochitika zina. Tikufuna kukumbutsa mipingo kuti zimenezi sizoyenera ndipo sizimasonyeza chiyamikiro chachikulu pa chogaŵira cha Yehova chimenechi. Misonkhano yampingo imapanga mbali yofunika ya kulambira koona. Yehova amatilamula kumasonkhana nthaŵi zonse. (Ahebri 10:24, 25) Nthaŵi ya misonkhano yampingo itaikidwa, muyenera kuitsatira mosamalitsa. Sitiyenera konse kusintha nthaŵi ya msonkhano kapena kuichotserapotu kaamba ka kusanguluka kwina kulikonse, maukwati kapena maliro. Zochita zina ziyenera kulinganizidwa panthaŵi yosiyana ndi imene mpingo unaika kuti ndi ya kulambira kwa mpingo.

◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:

Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha—Chicheŵa

1997 Yearbook of Jehovah’s Witnesses—Chingelezi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena