Bokosi la Mafunso
◼ Pamene mpingo wapemphedwa kuthandiza kusamalira maliro, pangabuke mafunso otsatirawa:
Kodi ndani ayenera kupereka nkhani yamaliro? Apabanja ndiwo adzapanga chosankha chimenechi. Angasankhe mbale wobatizidwa aliyense wakaimidwe kabwino. Ngati bungwe la akulu lapemphedwa kupereka wokamba nkhani, iwo nthaŵi zambiri adzasankha mkulu wokhoza bwino kuti apereke nkhani yozikidwa pa autilaini ya Sosaite. Ngakhale sitikutamanda wakufayo mopambanitsa, kungakhale bwino kutchula mikhalidwe yopereka chitsanzo chabwino imene iye anali nayo.
Kodi Nyumba ya Ufumu ingagwiritsiridwe ntchito? Inde ingatero ngati bungwe la akulu lapereka chilolezo ndipo ngati sizisokoneza nthaŵi yamsonkhano wanthaŵi zonse. Holo ingagwiritsiridwe ntchito ngati wakufayo anali ndi mbiri yabwino ndipo anali chiŵalo cha mpingo kapena mwana wamng’ono wa chiŵalo china. Ngati munthuyo anali atadzetsa chitonzo chodziŵika kwa anthu mwa khalidwe lina losakhala lachikristu, kapena ngati pali nkhani zina zimene sizingapereke chithunzi chabwino cha mpingo, akulu angasankhe kusalola kugwiritsira ntchito holo.—Onani buku la Uminisitala Wathu, masamba 62-3.
Kwenikweni, Nyumba za Ufumu sizimagwiritsiridwa ntchito pamaliro a osakhulupirira. Zimenezo zingachitike kokha ngati achibale ake amoyo akugwirizana mwachangu ndi mpingo monga ofalitsa obatizidwa, ambiri mumpingo amamdziŵa wakufayo kuti anali wokonda choonadi wokhala ndi mbiri yabwino yakhalidwe lake m’chitaganya, ndipo palibe miyambo yakudziko imene idzaloŵetsedwa m’programuyo.
Popereka chilolezo cha kugwiritsira ntchito Nyumba ya Ufumu, akulu adzalingalira ngati kuli kozoloŵereka kuti anthu amayembekezera kuona bokosi lamaliro pamaliropo. Ngati amatero, angaloleze kuibweretsa m’holo.
Bwanji nanga za maliro a anthu akunja? Ngati wakufayo anali ndi mbiri yabwino m’chitaganya, mbale angapereke nkhani ya Baibulo yotonthoza pamaliropo kapena kumanda. Mpingo sudzavomera kusamalira maliro a munthu amene anali wodziŵika ndi khalidwe lachisembwere ndi losayeruzika kapena amene moyo wake unali wosemphana kotheratu ndi mapulinsipulo a Baibulo. Ndithudi mbale sangagaŵane ndi mtsogoleri wachipembedzo kuchititsa programu ya chikhulupiriro choloŵana kapena kugaŵanamo m’maliro alionse ochitidwira m’tchalitchi cha Babulo Wamkulu.
Bwanji ngati wakufayo anali wochotsedwa? Nthaŵi zambiri mpingo sumaloŵamo. Nyumba ya Ufumu singagwiritsiridwe ntchito. Ngati munthuyo anali kusonyeza umboni wa kulapa ndi kusonyeza chikhumbo cha kubwezeretsedwa, chikumbumtima cha mbale chingamlole kupereka nkhani ya Baibulo kunyumba yamaliro kapena kumanda, kuti apereke umboni kwa osakhulupirira ndi kutonthoza achibale. Komabe, asanapange chosankha chimenechi kungakhale bwino kwa mbaleyo kufunsira kwa bungwe la akulu ndi kulingalira zimene iwo anganene. Pamikhalidwe imene sikungakhale kwanzeru kuti mbaleyo aloŵemo, kungakhale koyenera kuti mbale amene ali wambanja la munthu wakufayo apereke nkhani yotonthoza achibale.
Malangizo owonjezereka amapezeka m’makope a Nsanja ya Olonda a October 15, 1990, masamba 30-1; March 15, 1982, tsamba 31; September 15, 1980, masamba 5-7; December 1, 1978, masamba 5-8; December 1, 1977, masamba 550-51; October 1, 1970, masamba 454-5; ndi Galamukani! wa September 8, 1990, masamba 26-7 ndi wa January 8, 1978, masamba 16-20.