Lingaliro la Baibulo
Kudzipha—Kodi Pali Chiukiriro?
NKHANI yowopsya ya kudzipha simatseka chaputala m’miyoyo ya achibale ndi mabwenzi; iyo imatsegula china—chaputala cha malingaliro osanganizika achifundo ndi aukali, achisoni ndi aliŵongo. Ndipo imadzutsa funso lakuti: Kodi tingamuyembekezere bwenzi lathu amene anadzipha?a
Ngakhale kuti imfa yodzidzetsera simalungamitsidwa konse, siimakhalapo yolungama, mtumwi Paulo anali ndi chiyembekezo chabwinopo ngakhale cha anthu ena osalungama. Pakuti iye anauza motere khoti la lamulo Lachiroma: ‘Ndi kukhala ndi chiyembekezo cha kwa Mulungu . . . kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.’—Machitidwe 24:15.
Komabe, akatswiri a maphunziro azaumulungu ambiri atsutsa kwanthaŵi yaitali malingaliro aliwonse akuti kuuka kwa osalungama kungapereke chiyembekezo kwa omwe amadzipha. Kodi nchifukwa ninji?
Akatswiri a Maphunziro Azaumulungu Atsutsa Chiyembekezo cha Chiukiriro
William Tyndale anazindikira motere mbali ya vutoli m’mawu ake oyamba a Baibulo lake la m’zaka za zana la 16: “Kuika miyoyo yotuluka mwa anthu m’mwamba, mu helo, kapena mu puligatoriyo munthuwe umathetsa mfundo ya chiukiriro imene Kristu ndi Paulo anaitsimikizira.” Inde, zaka mazana ambiri zapitazo, anthu atchalitchi anayambitsa chiphunzitso chosakhala m’Baibulo ichi: miyoyo yosafa imene imatuluka m’thupi paimfa imanka kumwamba, puligatoriyo, Limbo, kapena ku helo. Chiphunzitsochi chinaombana ndi chiphunzitso chomvekera cha Baibulo cha chiukiriro chamtsogolo. Monga mmene Charles Andrews, minisitala wa Baptist anafunsira kuti: “Ngati moyo ukupuma kale m’mwamba (kapena ukuwotchedwa kale mwachilungamo mu helo), kodi pangafunikirenji chinachake chowonjezereka?” Iye anawonjezera motere: “Chitsutso chamkati ichi chakhalapobe kugonjetsa Akristu m’zaka mazana onsewa.”
Chotulukapo chimodzi cha kulakwa kwa maphunziro aumulungu kumeneku chinali chakuti “chiyambire nthaŵi ya Augustine [354 mpaka 430 C.E.], tchalitchi chakhala chikutsutsa kudzipha kukhala uchimo,” akutero Arthur Droge mu Bible Review, December 1989, “chimo lopanda chiombolo, mofananadi ndi mpatuko ndi chigololo.”
Kugamula kwakuti liri “lopanda chiombolo,” kapena kuponyedwa m’moto wa helo popanda chiyembekezo kunakaikiritsa m’kangano wa kuperekedwa kwa chiweruzo pa imfa. National Catholic Reporter ikuvomereza motere: “Aŵiri a akatswiri aakulu kwenikweni a tchalitchi anatsutsa kudzipha—Augustine anakufotokoza kukhala ‘konyansa ndi kuipa koipitsitsa’ ndipo Aquinas anasonyeza kuti kunali uchimo wakupha [wosakhululukidwa] wotsutsana ndi Mulungu ndi chitaganya—koma siakatswiri atchalitchi onse omwe avomereza ichi.”
Mwachimwemwe, tingachipewe “chitsutso chamkati” chimenechi mwa kuvomereza zowonadi zazikulu ziŵiri za m’Baibulo. Choyamba ndi ichi, ‘moyo wochimwawo ndiwo udzafa.’ (Ezekieli 18:4) Chachiŵiri nchakuti, chiyembekezo chenicheni cha miyoyo yakufa (anthu) nchakukhalanso ndi moyo kupyolera “m’kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Machitidwe 24:15) Pamenepa, kodi nchiyani chimene tingayembekezere moyenerera kwa anthu amene amadzipha?
Osalungama Amene Adzaukitsidwa
Yesu anauza wachifwamba woweruzidwira ku imfa motere: “Udzakhala ndine m’Paradaiso.” Munthuyu anali wosalungama—wakuswa lamulo osati mnkhole wa kudzipha kwachiwawa—waliŵongo lovomereza yekha mwa gogogo. (Luka 23:39-43) Iye analibe chiyembekezo chopita kumwamba kukalamulira ndi Yesu. Chotero Paradaiso amene mbalayi ikayembekezera kuukiramo akakhala dziko lapansi lokongola pansi pa kulamulira kwa Ufumu wa Yehova Mulungu.—Mateyu 6:9, 10; Chibvumbulutso 21:1-4.
Kodi Mulungu adzamuukitsiranji wachifwambayu? Kodi nkuchitira kuti Iye akapitirizebe kumuŵerengera machimo ake akumbuyoko motsutsana naye? Kutalitali, popeza kuti Aroma 6:7, 23 akuti: ‘Pakuti iye amene anafa anamasulidwa kuuchimo,’ ndipo ‘mphotho yake ya uchimo ndi imfa.’ Ngakhale kuti machimo ake akumbuyoko sadzakumbukiridwa kwa iye, iye adzafunikirabe dipo lomubweretsa ku ungwiro.
Chotero, katswiri wa maphunziro aumulungu Albert Barnes anali wolakwa ndi wosokeretsa pamene anati: “Ochita zoipa adzaukitsidwa kuti adzakanidwe, kapena kutaidwa. Iyi ndiyo idzakhala nkhani powaukitsa; uku ndiko kulinganizidwa konse.” Ndizinthu zopanda pake chotani nanga kwa Mulungu wachilungamo ndi chikondi! Mmalo mwake, kuukitsidwira ku moyo m’paradaiso wa padziko lapansi kudzapatsa kwa wachifwamba wakaleyu (ndi osalungama ena) mwaŵi wopambana wa kuweruzidwa ndi zimene adzachita pambuyo pa kuukitsidwa kwawo.—1 Yohane 4:8-10.
Mwaŵi Wachifundo
Chotero mabwenzi ovutitsidwa a minkhole ya kudzipha angapeze chitonthozo kudziŵa kuti ‘Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye. Popeza adziŵa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife pfumbi.’ (Salmo 103:10-14) Ndi Mulungu yekha amene angamvetsetse matenda amaganizo, kupsyinjika kopambanitsa, ngakhale zilema zobadwa nazo, “m’ngozi ya kudzipha,” imene, National Observer inati, “sichinthu chochitika nthaŵi zonse [koma] kaŵirikaŵiri nkhani yochitika m’mphindi zochepa kapena m’maola ochepa okha.”—Onani Mlaliki 7:7.
Ndizowona kuti, munthu amene amadzipha amadzilanda mwaŵi wa kulapa kudzipha kwakeko. Koma kodi ndani anganene kaya munthu wodziphayo akadasintha kuyesera kudzipha kwakeko kukanalephera? Kwenikweni, akupha anthu ena asintha ndikupeza chikhululukiro cha Mulungu m’nthaŵi yawo ya kukhala ndi moyo.—2 Mafumu 21:16; 2 Mbiri 33:12, 13.
Chotero, Yehova, pokhala atalipira “dipo la anthu ambiri,” ngwoyenereradi kufutukulira chifundo, ngakhale kwa odzipha okha, mwakuwaukitsa ndikuwapatsa mwaŵi wamtengo wapatali wa ‘kulapa, ndikutembenukira kwa Mulungu, ndi kuchita ntchito zoyenera kutembenuka mtima.’—Mateyu 20:28; Machitidwe 26:20.
Kulingalira Moyo Kwathayo, ndi Kwamalemba
Moyo ndimphatso yochokera kwa Mulungu, sichinthu chofunikira kugwiritsidwa molakwa kapena kuthetsedwa ndi munthu mwini. (Yakobo 1:17) Chotero, Malemba amatilimbikitsa kuti tidzilingalire tokha kukhala, osati miyoyo yosafa, koma monga zolengedwa za mtengo wapatali za Mulungu amene amatikonda, amene amanyadira kukhala kwathu ndi moyo, ndi amene akuyang’ana kutsogolo mwachisangalalo ku nthaŵi ya chiukiriro.—Yobu 14:14, 15.
Chikondi chimalimbitsa kuzindikira kwathu kuti kudzipha—ngakhale kuti kumathetsa zothodwetsa za munthu—kumangowunjika mavuto ambiri pa otsala okondedwa. Ponena za nkhani ya munthu amene amadzipha yekha, anthufe sitingaweruze kaya ngati munthuyo adzaukitsidwa kapena ayi. Kodi iye anali wa liŵongo motani? Mulungu yekha ndiye asanthula ‘mitima yonse nazindikira zolingalira zonse zamaganizo.’ (1 Mbiri 28:9) Koma tingakhale ndichidaliro kuti ‘Woweruza wa dziko lonse lapansi adzachita chokondeka, cholungama, ndi cholondola!’—Genesis 18:25.
[Mawu a M’munsi]
a Nkhaniyi yalinganizidwira otsala a minkhole yodzipha. Kaamba ka kukambidwa kwathunthu kwa nkhani ya kudzipha, onani The Watchtower, August 1, 1983, masamba 3-11 ndi Awake!, August 8, 1981, masamba 5-12.
[Mawu a Chithunzi patsamba 26]
Kollektie Rijksmuseum Kröller-Müller, Otterlo