Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 7/15 tsamba 20-24
  • Kaonedwe Kachikristu ka Miyambo ya Maliro

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kaonedwe Kachikristu ka Miyambo ya Maliro
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Njozikidwa pa Chikhulupiriro Chimodzi
  • Bwanji za “Kuyeretsa mwa Kugonana”?
  • Miyambo Yolondera Maliro Usiku Wonse
  • Miyambo ya Maliro Yolemekezeka
  • Kodi Zovala Zolirira Maliro Nzololedwa?
  • Pewani Kutsatira Miyambo Yosemphana ndi Malemba
  • Mwambo wa Maliro Achikhristu Umakhala Wolemekezeka, Wosadzionetsera Ndiponso Wokondweretsa Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kodi a Mboni za Yehova Amakhulupirira Zotani pa Nkhani ya Mwambo wa Maliro?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • Kodi Akufa Ayenera Kulemekezedwa?
    Galamukani!—1999
  • Kuchepetsa Mavuto a Imfa
    Galamukani!—1992
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 7/15 tsamba 20-24

Kaonedwe Kachikristu ka Miyambo ya Maliro

IMFA yamwadzidzidzi ndi yosayembekezereka ya munthu amene umamkonda imapwetekadi kwambiri. Imasokoneza maganizo, ndi kuchititsa kuvutika ndi malingaliro. Zimasiyana ndi pamene wokondedwayo agona mu imfa atadwala ndi kuvutika kwanthaŵi yaitali, komabe chisoni ndi kutayikiridwa kwakukuluko zimakhalapobe.

Mosasamala kanthu za mmene wokondedwayo wafera, ofedwawo amafunikira kuchirikizidwa ndi kutonthozedwa. Mkristu wofedwa angazunzidwenso ndi anthu ena amene amaumirira kuti atsatire miyambo ya maliro yosemphana ndi Malemba. Zimenezi zimachitika kaŵirikaŵiri m’maiko ambiri a mu Afirika ndi m’madera enanso a dziko lapansi.

Kodi nchiyani chimene chingathandize Mkristu wofedwa kupewa miyambo ya maliro yosemphana ndi Malemba? Kodi okhulupirira anzake angamchirikize bwanji panthaŵi ya chiyeso yotereyi? Kwa onse amene amafunafuna kukondweretsa Yehova, mayankho amafunso ameneŵa ngofunika chifukwa “mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m’chisautso chawo, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa maŵanga ndi dziko lapansi.”​—Yakobo 1:27.

Njozikidwa pa Chikhulupiriro Chimodzi

Miyambo yochuluka yamaliro imazikidwa pachikhulupiriro chakuti akufa amakhalabe ndi moyo m’dziko losaoneka la makolo akale. Kuti awasangalatse, olira ambiri amalingalira kuti ayenera kuchita miyambo inayake. Mwinanso amaopa kukhumudwitsa anthu a pamudzi amene amakhulupirira kuti pamudzipo pangagwe tsoka ngati satsatira miyamboyo.

Mkristu woona sayenera kuchita nawo miyambo imene sikondweretsa Mulungu chifukwa choopa anthu. (Miyambo 29:25; Mateyu 10:28) Baibulo limasonyeza kuti akufa sadziŵa kalikonse, pakuti limati: “Amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi . . . Mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziŵa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.” (Mlaliki 9:5, 10) Motero Yehova Mulungu anachenjeza anthu ake akale kuti asamayese kusangalatsa akufa kapenanso kulankhula nawo. (Deuteronomo 14:1; 18:10-12; Yesaya 8:19, 20) Choonadi cha Baibulo chimenechi chimawombana ndi miyambo ya maliro yambiri yotchuka.

Bwanji za “Kuyeretsa mwa Kugonana”?

M’maiko ena a pakati pa Afirika, mkazi kapena mwamuna wofedwa amayembekezeredwa kuti agonane ndi wachibale wapafupi wa wakufayo. Amakhulupirira kuti ngati zimenezi sizingachitidwe ndiye kuti wakufayo adzazunza otsala a m’banjamo. Mwambo umenewu amautcha kuti “kuyeretsa mwa kugonana.” Koma Baibulo limanena kuti unansi uliwonse wakugonana kunja kwa ukwati ndi “chisembwere.” Popeza kuti Akristu amayenera ‘kuthaŵa chisembwere,’ iwo amakana molimba mtima mwambo wosemphana ndi Malemba umenewu.​—1 Akorinto 6:18, NW.

Talingalirani za mkazi wamasiye wotchedwa Mercy.a Mwamuna wake atamwalira mu 1989, achibale anafuna kuti amyeretse mwa kugonana ndi wachibale wina wachimuna. Iye anakana, nalongosola kuti mwambowo ngwosemphana ndi malamulo a Mulungu. Achibalewo anakhumudwa ndipo anachoka atamnyoza. Patapita mwezi umodzi anabweranso namlanda katundu yense wa m’nyumbamo nachotsa malata ake. “Chipembedzo chako chikuthandize,” iwo anatero.

Mpingo unamtonthoza Mercy ndi kummangiranso nyumba yatsopano. Anthu a pamudzipo anachita chidwi kwambiri kwakuti ena anaganiza zogwira nawo ntchitoyo, ndipo mkazi wa mfumu yemwe ndi Mkatolika anali woyamba kubweretsa udzu wovikira nyumbayo. Kukhulupirika kwa Mercy kunalimbikitsa ana ake. Pakali pano, anayi mwa anawo adzipatulira kwa Yehova Mulungu, ndipo posachedwapa mmodzi wa iwo anakachita nawo Sukulu Yophunzitsa Utumiki.

Akristu ena akwatirana ndi osakhulupirira chifukwa cha mwambo umenewu wa kuyeretsa mwa kugonana. Mwachitsanzo, mwamuna wina wofedwa wazaka za m’ma 70 anakwatira mtsikana wamng’ono yemwe anali wachibale wa mkazi wake. Mwakutero iye akanatha kunena kuti anayeretsedwa mwa kugonana. Komabe, kachitidwe kotero kamatsutsana ndi uphungu wa Baibulo wakuti Akristu ayenera kukwatira “mwa Ambuye.”​—1 Akorinto 7:39.

Miyambo Yolondera Maliro Usiku Wonse

M’maiko ambiri, olira amasonkhana panyumba ya wakufayo nkuchezera. Kaŵirikaŵiri kulondera maliro kumeneku kumaphatikizapo phwando ndi kuimba mofuula. Amakhulupirira kuti zimenezi zimasangalatsa wakufayo ndi kutetezera a m’banja otsalawo ku mfiti. Nkhani zokometsera zingakambidwe kuti apeze chiyanjo cha wakufayo. Munthu atalankhula, olirawo amaimba nyimbo yachipembedzo poyembekezera kuti winanso alankhulepo. Zingapitirirebe choncho mpaka mmaŵa.b

Mkristu woona sachita nawo miyambo yolondera maliro usiku chifukwa Baibulo limasonyeza kuti akufa sangathandize kapena kuvulaza anthu amoyo. (Genesis 3:19; Salmo 146:3, 4; Yohane 11:11-14) Malemba amatsutsa kuchita zamizimu. (Chivumbulutso 9:21; 22:15) Komabe, mkazi wachikristu wofedwa zingamuvute kuti aletse anthu ena kuti asachite zinthu zokhudzana ndi mizimu. Iwo angaumirire kuti alonde maliro usiku wonse m’nyumba mwake. Kodi okhulupirira ena angathandize motani Akristu anzawo ofedwa amene akumana ndi vuto lowonjezereka lotereli?

Akulu a mpingo kaŵirikaŵiri akhala okhoza kuchirikiza banja lachikristu lofedwa mwa kukambirana ndi achibale kapena anthu a pamudzi. Atakambirana, anthuŵa angavomere kuti azipita ndi kukabweranso tsiku loika maliro. Koma bwanji ngati ena ayamba mkangano? Kupitiriza kukambirana nawo kungayambitse chiwawa. ‘Kapolo wa Ambuye sayenera kuchita ndewu, komatu ayenera kukhala woleza.’ (2 Timoteo 2:24) Choncho ngati achibale osamvetsetsa zinthu mwaukali ayamba kulamulira zochitikazo, mkazi wachikristu wofedwa ndi ana ake sangathe kuletsa zimenezi. Koma iwo sangachite nawo miyambo yachipembedzo chonyenga iliyonse imene ikuchitikira m’nyumba mwawo, chifukwa amamvera lamulo la Baibulo lakuti: “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupira osiyana.”​—2 Akorinto 6:14.

Pulinsipulo limeneli limagwiranso ntchito poika maliro. Mboni za Yehova siziimba, kupemphera, kapena kuchita nawo miyambo yotsogozedwa ndi mtsogoleri wa chipembedzo chonyenga. Ngati Akristu aona kuti nkoyenerera kuti akaike nawo maliro a wachibale wawo, iwo sachita nawo zochitikazo.​—2 Akorinto 6:17; Chivumbulutso 18:4.

Miyambo ya Maliro Yolemekezeka

Miyambo ya maliro yochitidwa ndi Mboni za Yehova siphatikizapo miyambo yofuna kusangalatsa akufa. Nkhani ya Baibulo imakambidwa kaya m’Nyumba Yaufumu, kunyumba yachisoni, kunyumba ya wakufayo, kapena kumanda. Cholinga cha nkhaniyi nkutonthoza ofedwa mwa kulongosola zimene Baibulo limanena zokhudza imfa ndi chiyembekezo cha chiukiriro. (Yohane 11:25; Aroma 5:12; 2 Petro 3:13) Nyimbo yozikidwa pa Malemba ingaimbidwe, ndipo mwambowo umamalizidwa ndi pemphero lotonthoza.

Posachedwapa, mwambo wa maliro woterewu unachitika pamaliro a mmodzi wa Mboni za Yehova amene anali mlongo wake wamng’ono pa onse wa Nelson Mandela, pulezidenti wa ku South Africa. Mwambowo utatha, pulezidentiyo anathokoza wolankhulayo moona mtima. Anthu olemekezeka ndi akuluakulu a boma ochuluka analipo pa mwambowo. “Uwu ndi mwambo wa maliro wolemekezeka kwambiri kuposa ina yonse yomwe ndapezekapo,” inatero nduna ina ya boma.

Kodi Zovala Zolirira Maliro Nzololedwa?

Mboni za Yehova zimalira okondedwa awo akamwalira. Mofanana ndi Yesu, iwo angalire misozi. (Yohane 11:35, 36) Koma siziona kuti nkofunikira kusonyeza kuti zili ndi chisoni mwa kuvala chinachake. (Yerekezerani ndi Mateyu 6:16-18.) M’maiko ambiri, akazi amasiye amayembekezeredwa kuvala zovala zapadera zolirira maliro kuti asangalatse akufa. Zovalazi zimavalidwa kwa miyezi ingapo mwinanso chaka chathunthu maliro atachitika, ndipo zimavulidwa pamwambo winanso.

Ngati munthu saonetsa zizindikiro zoti akulira amati akulakwira wakufayo. Pachifukwachi, Mboni za Yehova m’madera ena a Swaziland zathamangitsidwa ndi mafumu m’midzi ya kwawo. Komabe, Akristu okhulupirika oterowo akhala akusamaliridwa ndi abale awo auzimu m’madera ena.

Bwalo Lalikulu Lamilandu la ku Swaziland linagamula mokomera Mboni za Yehova likumati ziyenera kuloledwa kukakhala kumidzi ya kwawo. Pachochitika china, mkazi wina wamasiye wachikristu analoledwa kumakhala panyumba pake atasonyeza kalata ndi tepu mmene munajambulidwa mwamuna wake akunena momveka bwino asanamwalire kuti mkazi wake asadzavale zovala zolirira maliro. Motero iye anasonyeza kuti analidi kulemekeza mwamuna wake.

Nzopindulitsa kwambiri kuneneratu zoti anthu akachite pamaliro ako iweyo usanafe, makamaka m’madera amene mumachitika miyambo yochuluka yosemphana ndi Malemba. Talingalirani za Victor wa ku Cameroon. Analemberatu programu yokatsatiridwa pamaliro ake. M’banja lawo munali anthu ambiri otchuka omwe anali anthu a miyambo yamphamvu yokhudza akufa, kuphatikizapo kulambira zibade za anthu. Popeza kuti Victor anali munthu wolemekezeka m’banjalo, anadziŵa kuti chibade chake akachita nacho zoterozo. Choncho iye anapereka malangizo atsatanetsatane a mmene Mboni za Yehova zikachitire mwambo wa maliro ake. Zimenezi zinapangitsa kuti mkazi ndi ana ake asavutike, ndipo zinapereka umboni wabwino pamudzipo.

Pewani Kutsatira Miyambo Yosemphana ndi Malemba

Ena amene akudziŵa zimene Baibulo limanena amaopa kuoneka osiyana ndi anthu ena. Pofuna kupewa kuzunzidwa, ayesa kusangalatsa anthu a pamudzi mwa kuchita zinthu zokhala ngati kuti akuchita mwambo wolondera maliro. Pamene kuli kwakuti nkoyamikirika kuchezera ofedwa kuti tiwatonthoze, sizifunika kuti kamwambo ka maliro kachitidwe panyumba ya wakufayo usiku uliwonse tsiku loika malirowo lisanafike. Kutereku kungakhumudwitse anthu openya, chifukwa angakhale ndi chithunzi chakuti amene akuchita zimenezo sakhulupiriradi zimene Baibulo limanena pa mkhalidwe wa akufa.​—1 Akorinto 10:32.

Baibulo limalimbikitsa Akristu kuika kulambira Mulungu pamalo oyamba m’moyo wawo ndi kugwiritsira ntchito mwanzeru nthaŵi yawo. (Mateyu 6:33; Aefeso 5:15, 16) Komabe, m’madera ena zochitika za mpingo zaimitsidwa kwa mlungu umodzi kapena ingapo chifukwa cha maliro. Ili sivuto la mu Afirika mokha. Lipoti lochokera ku South America linasimba za maliro ena ake kuti: “Pamisonkhano itatu yachikristu panali anthu ochepa zedi. Kwa masiku ngati khumi anthu sanali kupita mu utumiki wakumunda. Ngakhale anthu akunja ndi ophunzira Baibulo anali kudabwa ndi kukhumudwa poona kuti abale ndi alongo athu ena anali kutengamo mbali m’zochitika za malirowo.”

M’madera ena, banja lofedwa lingaitane mabwenzi angapo kuti akadye chakudya kunyumba kwawo maliro ataikidwa. Koma m’madera ambiri a mu Afirika, anthu ochuluka amene amafika pamaliro amayembekezera kuti akapatsidwa chakudya kukhomo la wakufayo, kumene kaŵirikaŵiri amapha ziweto. Ena amene ali mumpingo wachikristu atsatira mwambo umenewu, ndipo apereka chithunzi cha kuchita miyambo yosangalatsa akufa.

Miyambo ya maliro yochitidwa ndi Mboni za Yehova sisenzetsa ofedwa chimtolo chachikulu. Choncho sikofunikira kuti pachite kukhala makonzedwe apadera oti anthu omwe afikapo azipereka ndalama zolipirira zinthu zochuluka zowonongedwa pamaliropo. Ngati akazi ofedwa ali osauka kwakuti sangathe kulipira zoonongedwa zofunikira, ndithudi ena mumpingo adzakhala osangalala kuwathandiza. Ngati chithandizocho chili chopereŵera, akulu angakonze zopereka chithandizo chakuthupi kwa awo oyenerera.​—1 Timoteo 5:3, 4.

Si nthaŵi zonse pamene miyambo ya maliro imawombana ndi mapulinsipulo a Baibulo. Pamene yatero, Akristu amatsimikiza kutsatira zimene Malemba amanena.c (Machitidwe 5:29) Ngakhale kuti izi zingabweretse mavuto owonjezereka, atumiki ambiri a Mulungu angachitire umboni kuti iwo anapambana ziyeso zoterozo. Atero ndi nyonga yochokera kwa Yehova, “Mulungu wa chitonthozo chonse,” ndiponso ndi chithandizo cha okhulupirira anzawo amene awatonthoza pamene anali m’mavutowo.​—2 Akorinto 1:3, 4.

[Mawu a M’munsi]

a Maina omwe ali m’nkhaniyi tawasintha.

b Anthu a zinenero zina ndiponso m’miyambo ina akamati “kulondera maliro” amanena za kukacheza ndi ofedwa kwa kanthaŵi kuti akawatonthoze. Palibe chilichonse chotsutsana ndi Malemba chimene chingaloŵetsedwepo. Onani Galamukani! yachingelezi ya May 22, 1979, masamba 27-8.

c Kumene miyambo ya maliro ikhozadi kubweretsa chiyeso chachikulu pa Mkristu, akulu angakonzekeretse anthu ofuna ubatizo za zimene angakumane nazo. Pamene akukumana ndi achatsopano ameneŵa kuti akambitsirane nawo mafunso a m’buku la Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu, ayenera kupereka chisamaliro chapadera ku zigawo za “Moyo, Uchimo ndi Imfa” ndi “Kugwirizana Zipembedzo.” Zigawo zonsezi zili ndi mafunso odzisankhira a kukambitsirana. Akulu angagwiritsire ntchito mbaliyi kuti apereke chidziŵitso pa miyambo ya maliro yosemphana ndi Malemba kotero kuti munthu wofuna ubatizoyo angadziŵe zimene Mawu a Mulungu amafuna kwa iye ngati atayang’anizana ndi mikhalidwe yoteroyo.

[Bokosi patsamba 23]

Anadalitsidwa Chifukwa cha Kusagwedera Kwawo

Sibongili ndi mkazi wamasiye wachikristu wolimba mtima amene amakhala ku Swaziland. Posachedwapa mwamuna wake atamwalira, anakana kutsatira miyambo imene ambiri amakhulupirira kuti imasangalatsa akufa. Mwachitsanzo, iye sanamete tsitsi. (Deuteronomo 14:1) Achibale asanu ndi atatu zinawakwiyitsa ndipo anammeta mokakamiza. Analetsanso Mboni za Yehova kufika panyumbapo kukamtonthoza Sibongili. Komabe, anthu ena okondweretsedwa ndi uthenga wa Ufumu anali okondwa kukampatsira makalata a chilimbikitso olembedwa ndi akulu. Patsiku limene Sibongili ankayembekezeredwa kuvala zovala zapadera zolirira maliro panachitika zodabwitsa. Munthu amene pabanjalo amamuopa anachititsa msonkhano kuti akambirane za kukana kwake kuchita miyambo yawo ya maliro.

Sibongili anati: “Anandifunsa ngati zikhulupiriro zanga za chipembedzo zingandilole kuti ndivale zovala zamaliro zakuda kuti ndisonyeze chisoni. Nditawalongosolera malingaliro anga anati sandiumiriza. Zinandidabwitsa kuti onse anandipepesa kuti ankandichitira nkhanza ndi kuti anandimeta ine ndisakufuna. Onse anandipempha kuti ndiwakhululukire.” Kenako, mng’ono wake wa Sibongili anasonyeza kuti akukhulupirira kuti Mboni za Yehova zili ndi chipembedzo choona, ndipo anapempha kuti aphunzire Baibulo.

Talingalirani za chitsanzo china: Benjamin wa ku South Africa anali ndi zaka 29 pamene anamva kuti atate ake amwalira mwadzidzidzi. Benjamin ndiye yekha anali Mboni m’banja lawo panthaŵiyo. Poika malirowo, aliyense anayembekezeredwa kuti adutse pomwe panali dzenje loikamo malirowo ali pamzere ndi kuthira dothi lodzala dzanja pabokosi lamaliro.d Maliro ataikidwa, achibale onse anameta. Popeza kuti Benjamin sanachite nawo miyambo yonseyi, anthu a pamudzi ndi achibale ankanena kuti mzimu wa atate ake akufawo udzamlanga.

Benjamin anati: “Palibe chimene chinandichitikira chifukwa ndimadalira Yehova.” Achibale anaona zimene zinamchitikira. Patapita nthaŵi, ochuluka a iwo anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndipo anabatizidwa posonyeza kudzipatulira kwawo kwa Mulungu. Nanga bwanji za Benjamin? Iye anayamba ntchito yolalikira nthaŵi zonse. Kwa zaka zingapo zapitazi, wakhala ndi mwayi wa kutumikira mipingo ya Mboni za Yehova monga woyang’anira woyendayenda.

[Mawu a M’munsi]

d Ena sangaone chovuta chilichonse ndi kuponya maluŵa kapena dothi m’manda. Komabe, Mkristu adzapewa zimenezi ngati anthu a kumeneko amaziona ngati njira imodzi yosangalatsira akufa kapenanso ngati mwambowo ukutsogozedwa ndi mtsogoleri wa chipembedzo chonyenga.​—Onani Galamukani! yachingelezi ya March 22, 1977, tsamba 15.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena