Lingaliro la Baibulo
Kodi Akufa Ayenera Kulemekezedwa?
“ANTHU AMBIRI ALI NDI MALINGALIRO OMWE ANAZIKAMIZU MWA IWO OPATSA MTEMBO WAMUNTHU ULEMU KOMA WANYAMA AYI.”—ENCYCLOPÆDIA BRITANNICA.
AMBIRI amalemekeza akufa awo mwanjira ina yake. Akufa amalemekezedwa mwa kulengeza imfa yawo m’manyuzipepala, ndipo amalemba nkhani zowatamanda. M’mayiko ena, n’zofala kuti anthu amachita miyambo ya maliro yokhudzana ndi zachipembedzo kapena ya kwawo komweko. Mwambo wokhudza wakufa umatenga masiku, masabata, kapena miyezi. Masukulu, mabwalo a ndege, misewu ndi matauni zimapatsidwa mayina a anthu otchuka amene anamwalira. Amaumba zifaniziro zawo ndiponso amakhazikitsa masiku a tchuthi kuti azikumbukira ntchito zaungwazi zimene anachita.
Komabe, malinga ndi Mawu a Mulungu, akufa sazindikira kuti mumawachitira ulemu. (Yobu 14:10, 21; Salmo 49:17) Akufawo amaoneka ngati amoyo kwa anthu okhawo omwe amawakumbukira. Baibulo limati: “Pakuti amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi.” (Mlaliki 9:5) Malemba amanena za chiyembekezo cha chiukiriro chimene chidzachitika m’tsogolo. (Yohane 5:28, 29; 11:25) Padakali pano, omwe anafa kulibe mpaka itafika nthaŵiyo. Iwo amasanduka fumbi.—Genesis 3:19; Yobu 34:15.
Polingalira za mmene Baibulo limanenera momveka bwino za momwe akufa alili, kodi zimapindula chilichonse ngati tiwalemekeza? Kodi Akristu ayenera kutsatira miyambo yamaliro yakwawo pamene okondedwa awo amwalira?
Miyambo Yoyambira pa Zikhulupiriro Zabodza
Miyambo yambiri ya kumalo osiyanasiyana yokhudza akufa imachokera pa ziphunzitso zachipembedzo zosakhala za m’Baibulo. Encyclopædia Britannica inati cholinga cha miyambo ina ndi “kutetezera wakufa kuti ziŵanda zisamukhudze; nthaŵi zina cholinga cha miyambo ina n’chakutetezera anthu a moyo kuti imfayo isawakhudze kapenanso kuti wakufayo asawavutitse.” Miyambo yonse yotere yomwe maziko ake ndi chikhulupiriro chakuti akufa adakali moyo kumalo ena osaoneka n’zotsutsana kwambiri ndi chiphunzitso cha Baibulo.—Mlaliki 9:10.
Anthu ambiri amalemekeza kwambiri akufa awo. Kulambira kumeneku kumaphatikizapo kupereka nsembe ndi mapemphero kwa makolo omwe anafa kale. Ena mwa amene amachita miyambo imeneyi saona zimenezo monga kulambira, koma monga kupereka ulemu waukulu kwa akufa. Ngakhale zili choncho, kulemekeza makolo kwamtundu umenewu kuli ngati kulambira ndipo zimatsutsana ndi chiphunzitso cha Baibulo. Yesu Kristu anati: “Ambuye Mulungu wako uzim’gwadira, ndipo Iye yekha yekha uzim’tumikira.” Luka 4:8.
Kuchita Molongosoka
Si kuti kuchitira ulemu akufa nthaŵi zonse n’kogwirizana ndi ziphunzitso za chipembedzo chonyenga. Mwachitsanzo, Baibulo limanena za mmene anthu analemekezera Mfumu Hezekiya itafa. Anthu a Mulungu ‘anamuika polowera kumanda a ana a Davide; ndi Ayuda onse ndi okhala m’Yerusalemu anam’chitira ulemu pa imfa yake.’ (2 Mbiri 32:33) Chitsanzo china ndi Yesu. Baibulo limanena kuti ophunzira ake “anatenga mtembo wa Yesu, nauzenenga ndi nsalu zabafuta pamodzi ndi zonunkhira, monga mwa maikidwe a maliro a Ayuda.”—Yohane 19:40.
M’malemba muli nkhani zambiri zonena zochitika zosiyanasiyana zokhudza mmene mtembo anauchitira ndi mmene anauyikira. Uku sikunali kulambira makolo, kapenanso si kuti panali chikhulupiriro chakuti akufa amapitiriza kuchita zinthu zomwe zingakhudze zochita za anthu amoyo. Koma kuti olira ankasonyeza ulemu wawo waukulu kwa amene ankawakonda. Baibulo silikana ulemu wamtundu umenewo, popeza kuti umachokera pachikondi chachibadwidwe chimene munthu ali nacho ngakhale kuti Baibulo silivomereza kuchita zinthu monyanyira kapena mokhala ngati wasokonezeka maganizo pamaliro. Komanso sililimbikitsa kuti Akristu azingokhala osamva chisoni pamene anthu amene amawakonda amwalira.
Chifukwa cha chimenechi Mboni za Yehova zikapita ku maliro a anthu amene ankawakonda zimasonyeza ulemu woyenera ndi kulemekeza wakufayo. (Mlaliki 7:2) Ikakhala nkhani yoika maluwa, zochitika pamaliro, ndi miyambo ina, Akristu amachita zinthu mwanzeru kuti asachiteko zina zomwe zimatsutsana ndi Baibulo. Kuti izi zitheke, pafunika kumalingalira bwino. Encyclopædia of Religion and Ethics imanena kuti “tanthauzo ndi phindu la mwambo wina zimasintha pamene nthaŵi ikusintha ndipo tanthauzo la mwambo limatheka kudzakhala losiyana kwambiri ndi tanthauzo la poyamba, ndipo mmene angalilongosolere pambuyo pake sizingakuthandizeni kuzindikira tanthauzo la poyambapo.”a
Kodi N’kulakwa Kulemba Zotamanda Wakufayo?
Mfundo yakuti tiyenera kuchita zinthu molongosoka imakhudzanso kulemba nkhani zokhudza anthu akufa. Pamaliro, Mboni za Yehova zimayesetsa kutonthoza olira. (2 Akorinto 1:3-5) Pologalamu yonse ikayenda bwino, mwina munthu mmodzi kapena angapo akhoza kukamba nkhani. Koma sizingakhale zoyenera kupangitsa pologalamuyo kukhala yotenga nthaŵi yaitali kuŵerenga makalata olemekeza wakufayo. Mmalo mwake, mwambo wa malirowo uyenera kupereka mpata wosonyezera makhalidwe abwino a Mulungu, kuphatikizapo ubwino wake potipatsa ife chiyembekezo cha chiukiriro.
Komabe izi sizikutanthauza kuti n’kulakwa kukumbukira makhalidwe abwino a munthu wakufayo pokamba nkhani yamaliro (Yerekezerani ndi 2 Samuel 1:17-27.) Ngati wakufayo anali wokhulupirika kwa Mulungu mpaka imfa yake, iye amakhala chitsanzo chabwino choti n’kutsanzira. (Ahebri 6:12) N’koyenera kulingalira za kukhulupirika kwa atumiki a Mulungu. Kuuzako ena mfundo zimenezi panthaŵi yamaliro kumatonthoza omwe ali moyowo ndipo pamene mukukumbukira wakufayo mumam’kumbukira monga wolemekezeka.
Akristu oona salambira akufa. Sachita nawo miyambo imene imatsutsana ndi choonadi cha Baibulo. Komabe panthaŵi yomweyo, atumiki a Mulungu sachita kunyanya kulingalira kuti popeza omwe anafa tsopano ndi fumbi chabe ndiye kuti miyambo yonse yokhudzana ndi maliro ndi yopanda ntchito ndi yosafunika. Iwo amalira ndipo amakumbukira akufa awo. Komabe amatonthozedwa mtima ndi choonadi cha Baibulo chakuti akufa sakuvutika ndi kuti pali chiyembekezo chakuti adzauka.
[Mawu a M’munsi]
a Nsanja ya Olonda ya October 15, 1991, tsamba 31, inapereka malangizo awa: ‘Mkristu weniweni ayenera kulingalira izi: Kodi ngati nditsatira mwambowu zisonyeza kwa ena kuti ndikukhulupirira kapena kuchita zinthu zosakhala za m’Malemba? Nthaŵi ndi malo kumene muli ndizo mwina zingathandize kuti mupeze yankho. Mwambowo (malinga ndi mmene wakhalira) utha kukhala kuti unali ndi tanthauzo labodza lokhudzana ndi chipembedzo zaka chikwi zapitazo mwinamwake ndi wotero lerolino kudziko lina lakutali. Koma kuti musataye nthaŵi kufufuza, dzifunseni kuti: ‘Kodi kuno kumene ndimakhala anthu amauona motani?’—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 10:25-29.’
[Chithunzi patsamba 10]
Mwambo wamaliro kulemekeza Gustav II, mfumu ya ku Sweden, itamwalira mu 1632
[Mawu a Chithunzi]
Kuchokera m’buku la Bildersaal deutscher Geschichte