Misonkhano Yautumiki ya July
CHIDZIŴITSO: Utumiki Wathu Waufumu udzandandalika Msonkhano Wautumiki wa mlungu uliwonse m’milungu ya msonkhano wachigawo. Mipingo ingasinthe mofunikira kuti ikapezeke pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Kukhulupirira Mawu a Mulungu” ndi kukwanitsa kupenda mfundo zazikulu za programuyo kwa mphindi 30 pa Msonkhano Wautumiki wa mlungu wotsatira. Kupenda programu ya msonkhano wachigawo ya tsiku ndi tsiku kuyenera kugaŵiridwa msonkhano wachigawo usanafike kwa abale aŵiri kapena atatu oyenerera amene adzakhoza kusumika maganizo pa mfundo zofunikira. Kupenda kokonzekeredwa bwino kumeneku kudzathandiza mpingo kukumbukira mfundo zazikulu zogwiritsira ntchito mwaumwini ndi zogwiritsira ntchito m’munda. Ndemanga za omvetsera ndi zokumana nazo zimene zinasimbidwa ziyenera kukhala zachidule ndi zolunjika. Popeza msonkhano wachigawo chaka chino udzakhala wa masiku atatu, palibe chifukwa chosachitira Phunziro la Buku la Mpingo mlungu wamsonkhano. Komabe, simudzachita misonkhano yonse inayo ya mlungu umene mpingo wanu udzapita kumsonkhano wachigawo.
Mlungu Woyambira July 7
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Tchulani lipoti la utumiki wakumunda la February la dzikoli ndi la mpingo wanu.
Mph. 15: “Kukhulupirika Kufupidwa.” Mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo chitsanzo chosimbidwa mu Galamukani! yachingelezi ya January 22, 1993, masamba 18-21.
Mph. 20: “Thandizani Ena Kupeza Chitonthozo.” Kukambitsirana ndi omvetsera. Chitirani chitsanzo ulaliki umodzi kapena maulaliki aŵiri. Pemphani omvetsera kusimba njira zimene ayambira makambitsirano, mwa kugwiritsira ntchito mabrosha amodzimodziwo. Alimbikitseni kugwiritsira ntchito mawu apafupi, osankhidwa bwino podzutsa chidwi. (Onani Bukhu Lolangiza la Sukulu, tsamba 7, ndime 9-11.) Tchulani mabrosha ena amene tingagaŵire amene mpingo uli nawo m’stoko.
Nyimbo Na. 70 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 14
Mph. 12: Zilengezo zapamalopo. Lipoti la maakaunti. Pendani “Tidzaphunzira Buku la Chimwemwe cha Banja.”
Mph. 15: “Chitani Umboni Kulikonse Kumene Kuli Anthu.” Nkhani. Ngati muli ndi nthaŵi, mungasimbe zokumana nazo zina za mu 1997 Yearbook, masamba 43-6.
Mph. 18: “Msonkhano Wachigawo wa 1997 wa ‘Kukhulupirira Mawu a Mulungu.’” (Ndime 1-12) Mafunso ndi mayankho. Ŵerengani ndime 7, 9, ndi 12. Gogomezerani kuti kudzisungira mosamala pakaonekedwe kathu ndi khalidwe lathu lachifatso lachikristu ndi kuyang’anira bwino ana athu nkofunika mwamalemba.
Nyimbo Na. 71 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 21
Mph. 12: Zilengezo zapamalopo. Pendani “Programu Yatsopano ya Msonkhano Wadera.”
Mph. 13: “Kodi Ndani Adzatimukira Ife?” Nkhani yolimbikitsa. Phatikizanipo chilimbikitso cha kuchita upainiya wokhazikika ndi chokumana nacho cha m’mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa February 1997, ndime 16-17. Awo amene sangakhale apainiya okhazikika angalinganize kuchita upainiya wothandiza m’miyezi yakutiyakuti chaka chautumiki chikudzachi.
Mph. 20: “Msonkhano Wachigawo wa 1997 wa ‘Kukhulupirira Mawu a Mulungu.’” (Ndime 13-19) Mafunso ndi mayankho. Ŵerengani ndime 13 ndi malemba osonyezedwa. Gogomezerani kuti kulinganizika ndi kulingalira ena nkofunika, makamaka pankhani yamipando. Malizani ndi nkhani yachidule yopenda “Zikumbutso za Msonkhano Wachigawo”
Nyimbo Na. 72 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 28
Mph. 12: Zilengezo zapamalopo. Kumbutsani onse kupereka malipoti awo a utumiki wakumunda. Pendani mabuku ogaŵira mu August. Yesetsani kubwerera kumene munagaŵira mabrosha mu July pamaulendo obwereza mu August, kuyesa kuyamba maphunziro a Baibulo. Mwa kugwiritsira ntchito mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa May 1997, tchulani zofunika zina kuti ulendo wobwereza ukhale wogwira mtima. Maphunziro ayenera kuyambidwa m’brosha la Mulungu Amafunanji kapena m’buku la Chidziŵitso.
Mph. 15: Zosoŵa zapamalopo.
Mph. 18: Tsirizani Utumiki Wanu. Nkhani ya woyang’anira utumiki yochokera m’buku la Uminisitala Wathu, masamba 5-8. Gogomezerani kufunika kwa kuchita changu pantchito yolalikira, kusonkhezera onse kuona udindo wawo monga atumiki kukhala wofunika kwambiri.
Nyimbo Na. 75 ndi pemphero lomaliza.