Mboni za Yehova—Alaliki Enieni
1 Yesu Kristu anapatsa ophunzira ake onse udindo wakulalikira, nkuwalamula mwachindunji kuti akalalikire uthenga wabwino wa Ufumu. (Mat. 24:14; Mac. 10:42) Ophunzira ake oyambirira anasonyeza chitsanzo cha zimenezi pamene ankalalikira Ufumu mosalekeza—osati pamalo olambirira pokha komanso kulikonse kumene ankapeza anthu pamakwalala ndiponso pomka kunyumba ndi nyumba. (Mac. 5:42; 20:20) Ife Mboni za Yehova lerolino tadzisonyeza kuti ndife alaliki enieni achikristu, chifukwa tikulalikira uthenga wa Ufumu m’maiko 232, ndipo tinabatiza ophunzira atsopano oposa miliyoni imodzi pazaka zitatu zokha zapitazi! Kodi nchifukwa chiyani ntchito yathu yolalikirayi ikuyenda bwino chonchi?
2 Uthenga Wabwino Umatisangalatsa: Alaliki ndiwo amithenga a uthenga wabwino. Ndiye poti ndife amene, tili ndi mwaŵi wosangalatsa wakulengeza Ufumu wa Yehova—wokhawo womwe uli uthenga wabwino weniweni umene uyenera kuperekedwa kwa anthu osautsika. Tili achimwemwe chifukwa tadziŵiratu kuti pali miyamba yatsopano yomwe idzalamulira molungama dziko lapansi latsopano lopangidwa ndi anthu okhulupirika m’Paradaiso akudzayo. (2 Pet. 3:13, 17) Ndife tokha amene tili ndi chiyembekezo chimenechi, ndipo tikufunitsitsa kuuza ena za icho.
3 Chikondi Chenicheni Nchimene Chimatisonkhezera: Kulalikira ndi ntchito yopulumutsa miyoyo. (Aroma 1:16) Nchifukwa chake timasangalala zedi pofalitsa uthenga wa Ufumu. Ifeyo pokhala alaliki enieni, timakonda anthu, ndipo chikondicho chimatisonkhezera kuwauzako uthenga wabwino—achibale, anansi athu, odziŵana nawo, ndi enanso ambiri. Kuichita ntchito imeneyi ndi mtima wonse ndiyo njira yabwino kopambana yosonyezera kuti timakondadi ena.—1 Ates. 2:8.
4 Mzimu wa Mulungu Umatichirikiza: Mawu a Mulungu amatilonjeza kuti tikamagwira ntchito yathu yobzala mbewu ya Ufumu ndi kuithirira, Yehova ndiye amene ‘amakulitsa.’ Zimenezo zangokhala ndendende nzimene tikuona zikuchitika m’gulu lathu lero. (1 Akor. 3:5-7) Mzimu wa Mulungu ndiwo umatichirikiza pantchito yathu yolalikira ndipo umapangitsa zinthu kutiyendera bwino kwambiri.—Yow. 2:28, 29.
5 Popeza 2 Timoteo 4:5 akutilimbikitsa ‘kuchita ntchito ya mlaliki,’ ndipo chifukwa chakuti timakonda anthu, tiyenitu tisonkhezereke kuwauza uthenga wa Ufumu wosangalatsawu pampata uliwonse, tikumadalira kuti Yehova azidalitsabe ntchito yathu.