Ngati Umagwira Mtima, Ugwiritsireni Ntchito!
1 Utumiki Wathu Waufumu suleka kutipatsa maulaliki achitsanzo ogwiritsira ntchito mu utumiki. Amenewa amatipatsa malingaliro atsopano a mmene tingachititsire anthu chidwi ndi uthenga wa Ufumu. Mwina mumayesetsa kuti mwezi uliwonse muphunzire ulaliki umodzi kapena angapo. Komabe, mwina ofalitsa ena amaona kuti pamene angogwiritsira ntchito ulaliki umodzi kangapo, kope lina la Utumiki Wathu Waufumu limabwera ndi maulaliki ena atsopano. Nzachionekere kuti nzosatheka kuti aliyense aphunzire ulaliki wina watsopano asanakhoze bwino woyamba uja.
2 Nzoona kuti pali apainiya ndi ofalitsa zikwizikwi amene amawononga nthaŵi yaitali ali mu utumiki wakumunda. Ndiponso, mipingo yambiri imafola gawo lawo lonse patangopita milungu yoŵerengeka. Pamenepo mpamene ofalitsa angafunedi njira zina ndi malingaliro atsopano operekera uthenga. Zimenezo zimawathandiza kukulitsa maluso awo. Zimapangitsanso utumiki wawo kusangalatsa kwambiri ndi kubala zipatso ndi kuwathandiza kugonjetsa zopinga zimene amakumana nazo.
3 Mulimonse mmene zingakhalire, ngati mwakonza ulaliki umene umagwira mtima pakukulitsa chidwi, chonde pitirizani kuugwiritsira ntchito! Sikofunika kuleka kugwiritsira ntchito ulaliki wogwira mtima womwe umapangitsa anthu kumvetsera. Ingousinthani pang’ono kuti uyenerane ndi buku limene mukugaŵira mwezi womwewo. Mukamapenda malingaliro operekedwa mu Utumiki Wathu Waufumu, yang’anani mfundo zosangalatsa zimene mungakonde kutchula mu ulaliki wanu.
4 Choncho mukalandira kope latsopano la Utumiki Wathu Waufumu, muzikumbukira kuti maulaliki amene alimowo angokhala malingaliro basi. Ngati mungawagwiritsire ntchito, zili bwinonso. Koma ngati mwapeza kale ulaliki umene umapangitsa anthu kumvetsera m’gawo lanu, ugwiritsireni ntchito! Chinthu chofunika ndicho ‘kukwaniritsa utumiki wanu’ mwa njira yabwino, kupeza anthu oyenera ndi kuwathandiza kukhala ophunzira.—2 Tim. 4:5.