Kodi Ndifunikira kumasinthasintha?
Kope lililonse la Utumiki Wathu Waufumu limakhala ndi maulaliki a m’Malemba osiyanasiyana amene tingagwiritsire ntchito pochitira umboni. Ofalitsa ambiri amene ali okangalika amafunitsitsa kupeza malingaliro atsopano ndi kugwiritsira ntchito njira zosiyanasiyana. Utumiki Wathu Waufumu umawathandiza mwa kupereka malingaliro ochulukirapo mwezi uliwonse.
Komabe, mwina mungalingalire kuti simufunikira kumasinthasintha zimene mumagwiritsira ntchito. M’mwezi uliwonse mwina mungakhale ndi maola oŵerengeka chabe ochitira ntchito ya kunyumba ndi nyumba. Mkati mwa nyengo yaitali, mungakhale mutakonza maulaliki ena amene simuvutika nawo, ndipo mumakhala ndi zotsatirapo zabwino mwa kuwagwiritsira ntchito. Mwina mumadalira pa malemba ena ogwiritsiridwa ntchito kaŵirikaŵiri, kuphatikizapo Salmo 37:9-11, 2 Petro 3:13, Chivumbulutso 21:4, ndi ena. Ngati ndi choncho, simufunikira kudziona kukhala wokakamizika kusinthira ku kanthu kena nthaŵi ndi nthaŵi. Cholinga chathu chachikulu ndicho kuuza ena za chiyembekezo cha Ufumu ndi kuwathandiza kuphunzira zimene ayenera kuchita kuti ayenerere dalitso la Yehova. Ngati mwapeza maulaliki apanthaŵi yake ndi okopa m’buku la Kukambitsirana amene mungakonde kugwiritsira ntchito ndipo mukupeza nawo zotulukapo zabwino, musazengereze kuwagwiritsira ntchito.