Misonkhano Yautumiki ya February
Mlungu Woyambira February 2
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Mbiri Yateokrase.
Mph. 15: “Mboni za Yehova—Alaliki Enieni.” Mafunso ndi mayankho. Pendani bokosi lapatsamba 19 mu Nsanja ya Olonda ya September 1, 1992.
Mph. 20: “Itanani Aliyense Waludzu.” Ifotokozeni nkhaniyo, mukumasonyeza mmene maulaliki achitsanzo akonzedwera kuchititsa chidwi ndi kusonkhezera omvetsera. Wachikulire wina achitire chitsanzo ndime 2-3 kapena 4-5, ndipo wachinyamata achitire chitsanzo ndime 6.
Nyimbo Na. 208 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira February 9
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 15: Zosoŵa zapamalopo.
Mph. 20: “Mmene Akristu Amaonera Makonzedwe Osamalira Maliro ndi a Ukwati.” Nkhani yamafunso ndi mayankho m’ndime 1-11. Ikambidwe ndi mkulu wokhoza bwino. Ŵerengani ndime 9 ndi 11.
Nyimbo Na. 220 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira February 16
Mph. 5: Zilengezo zapamalopo.
Mph. 12: Chifukwa Chake Mufunikira Kufika Pamisonkhano ya Mpingo. Mkulu akufotokoza mfundo zazikulu mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 1993, masamba 8-11, nagogomezera kuti nkofunika kupezeka pamisonkhano nthaŵi zonse.
Mph. 18: “Mmene Akristu Amaonera Makonzedwe Osamalira Maliro ndi a Ukwati.” Nkhani yamafunso ndi mayankho m’ndime 12-26. Ikambidwe ndi mkulu wokhoza bwino.
Mph. 10: “Yehova Ndiye Mthandizi Wanga.” Nkhani yolimbikitsa yokambidwa ndi mkulu.
Nyimbo Na. 15 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira February 23
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Fotokozani za buku logaŵira m’March. Tchulani njira imodzi kapena ziŵiri zogaŵirira buku la Chidziŵitso, mwakugwiritsira ntchito mfundo za mu Utumiki Wathu Waufumu wa December 1995, tsamba 8. Gogomezerani kuti cholinga chizikhala choyamba maphunziro a Baibulo.
Mph. 15: “Ngati Umagwira Mtima, Ugwiritsireni Ntchito!” Mafunso ndi mayankho. Wofalitsa mmodzi kapena aŵiri okhoza bwino, ali khale m’gulu momwemo, akambepo za maulaliki amene awagwiritsirabe ntchito chifukwa cha kufeŵa kwa maulalikiwo ndi zimenenso zakhala zotsatira zake. Kenaka enanso anenepo za njira zina zotchulidwa posachedwapa mu Utumiki Wathu Waufumu zomwe zakhalanso zogwira mtima.
Mph. 20: Yesezani Maulaliki Anu. Nkhani yaifupi yochokera mu Bukhu Lolangiza la Sukulu, tsamba 99, ndime 8-9. Gogomezerani kuti nkofunika kumapenda maulaliki athu ndi kufunafuna njira zimene tingakhalire ogwira mtima kwambiri. Alongo aŵiri achite chitsanzo cha mmene amapendera zimene anachita pakhomo, namakambitsirana mmene angawongolere. Ndiyenso ayeseze mwachidule ulaliki wina umene ati akakambe panthaŵi ina, namapatsana malingaliro othandiza. Tcheyamani akumaliza mwa kulimbikitsa onse kuti azipenda maulaliki awo ndi kuwayeseza.
Nyimbo Na. 103 ndi pemphero lomaliza.