Nyimbo 4
Lonjezo la Mulungu la Paradaiso
1. Ya walonjeza Paradaiso,
M’kulamu la kwa Kristuyo,
Adzachotsa uchimo wonse,
Ndi imfa ndi zopweteka.
(Korasi)
2. Mwamsanga padzikoli
Yesu Adzau kitsa akufa.
Linali lonjezo la Kristu:
‘Udzakhala m’Paradaiso.’
(Korasi)
3. Nchimwemwe chotani kuwona!
Ambiri akuutsidwa!
Kudzakhala kulangizidwa,
Kopandadi mikangano.
(Korasi)
4. Paradaiso Walonjezedwa.
Yesu Mbuye ali Mfumu.
Tiyamika Mulungu wathu.
Tikondwere; Timyimbire.
(KORASI)
Paradaiso adzakhala.
Mwachidaliro tiwona.
Kristu adzakwaniritsa,
Chifuniro cha Mulungu.