Mbiri Yateokrase
Liberia: Ofesi yanthambi ku Monrovia inatsegulidwanso pa September 1, itatsekedwa kwa miyezi 15 chifukwa cha nkhondo yachiŵeniŵeni m’dzikomo. Mu September anapereka lipoti latsopano la chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa 1,977.
Mozambique: Anafikira chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa 28,005 mu September. Chiŵerengero chapamwamba chakale chinali 25,790 mu May 1975, choncho mu mbiri yateokrase ya Mozambique chimenecho nchosaiŵalika.
Nepal: Anafikira chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa 306 mu September. Pakali pano akuchititsa maphunziro a Baibulo pafupifupi 500.
St. Helena: Banja lililonse pachisumbu chimenechi linapatsidwa kope la Uthenga wa Ufumu Na. 35.
Maiko angapo anayamba chaka chautumiki chatsopano ndi ziŵerengero zapamwamba zatsopano za ofalitsa, zowonjezeka ndi 5 peresenti kuposa avareji ya chaka chatha: Hong Kong, 4,230; Madagascar, 8,749 (kuphatikizapo chiŵerengero chapamwamba cha apainiya okhazikika 912); Taiwan, 3,497.