Mbiri Yateokrase
Benin: M’November panali ofalitsa 5,331 amene anachitira lipoti, ndipo chimenecho chinali chiŵerengero chapamwamba chotsatizana cha 59.
Cyprus: Chiwonjezeko cha 2 peresenti m’November chinadzetsa chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa 1,758. Panalinso chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha apainiya, ndipo 136 anachitira lipoti.
India: Kupita patsogolo kosangalatsa kwa ntchito yolalikira kunaoneka m’November pamene ofalitsa 18,077 anachitira lipoti utumiki wakumunda. Chimenechi chinali chiŵerengero chapamwamba cha 39.
Liberia: Chiŵerengero chapamwamba koposa ndi kale lonse cha ofalitsa 2,120 anachitira lipoti utumiki wakumunda m’November.
Solomon Islands: Anafika pa chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa, ndipo 1,393 anachitira lipoti m’November.
Taiwan: Avareji ya ofalitsa chaka chino ndi 3,516, ndipo chimenecho ndi chiwonjezeko cha 6 peresenti kuposa chaka chatha.