Mbiri Yateokrase
Central African Republic: Ntchito ya utumiki m’mwezi wa October inali yapadera, yokhala ndi chiŵerengero chatsopano chapamwamba cha ofalitsa 1,846. Maprogramu a tsiku la msonkhano wapadera anachitidwa m’malo 19, ndi omvetsera 5,577 ndipo 32 anabatizidwa.
Mexico: Mu November, ofalitsa 411,292 anapereka lipoti. Chimenechi chinali chiŵerengero chinanso chatsopano chapamwamba.
Sri Lanka: Panali ofalitsa 1,873 amene anapereka lipoti mu November, chiwonjezeko chabwino kwambiri cha 9 peresenti.
Taiwan: Kupatulapo chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa 2,523, lipoti la November linasonyeza chiŵerengero chatsopano chapamwamba cha maulendo obwereza 44,514 ndi maphunziro a Baibulo 4,234.
Virgin Islands (U.S.): Chiŵerengero chatsopano chapamwamba cha ofalitsa 647 pamodzi ndi chiwonkhetso cha maphunziro a Baibulo 788 chinali chosangalatsa kwambiri mu November.