Mbiri Yateokratiki
Bolivia: Nthambi inachitira lipoti chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa 9,588 mu October. Iwo anafikiranso ziŵerengero zapamwamba zatsopano za maphunziro a Baibulo apanyumba, maulendo obwereza, ofalitsa ampingo, ndi apainiya okhazikika. Ofalitsa ampingo anachita avareji ya maola 14 muutumiki wakumunda.
India: Mu October chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa 13,217 chinafikiridwa. Ichi chinali chiŵerengero chawo chapamwamba chotsatizana chachitatu.
Lithuania: Lipoti la October limasonyeza chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa 871, chimene chili chiwonjezeko cha 39-peresenti kuposa October wa 1992.
Zambia: Pa December 19, 1993, tinakhala ndi kumaliza maphunziro kwa ophunzira 25 oyambirira a Sukulu Yophunzitsa Utumiki mu Zambia. Iwo anachokera kumaiko asanu a kummwera kwa Afrika. Miyezi iŵiri ya kosi yopanikizika inakonzekeretsa ophunzirawo kuthandiza bwino lomwe mipingo imene adzaitumikira. Makalasi ena anayi adzachitidwa pa Makeni mu 1994. Sukulu imeneyi njotseguka kwa akulu ndi atumiki otumikira amene ali mbeta.