Chakudya cha panthaŵi Yake
Monga kunalengezedwa m’kope la January 1994 la Utumiki Wathu Waufumu, nkhani yapoyera yapadera ya nyengo ya Chikumbutso chaka chino idzaperekedwa m’mipingo yochuluka pa April 10. Nkhaniyo ili ndi mutu wakuti “Chipembedzo Chowona Chikwaniritsa Zofunika za Chitaganya cha Anthu.” Kuyesayesa kwapadera kuyenera kupangidwa kuitanira aja amene anapezeka pa Chikumbutso pa March 26.