Kodi Mungawonjezere Chitamando Chanu kwa Yehova m’April?
1 Wamasalmo Davide anali ndi chikhumbo chochokera pansi pamtima cha kutamanda Yehova movomerezeka, motero analengeza kuti: “Ndidzayamika Yehova kwakukulu pakamwa panga; ndi pakati pa anthu aunyinji ndidzamlemekeza.” (Sal. 109:30) April ndinthaŵi yabwino ya ‘kuwonjezera kumlemekeza’ mwa kuwonjezera phande lathu muutumiki wakumunda. (Sal. 71:14) Kodi mukulinganiza kudzakhala pakati pa ambiri omwe akuchita zimenezi mwa kuloŵa m’ntchito yaupainiya wothandiza?
2 Linganizani Tsopano: “Zoganizira za wakhama zichulukitsadi katundu,” tikukumbutsidwa motero pa Miyambo 21:5. Zimenezi zimafuna kuti mupereke nkhaniyo kwa Yehova m’pemphero, mukumamuika patsogolo m’makonzedwe anuwo. (Miy. 3:5, 6) Chotsatira, pendani mosamalitsa programu yanu yapanthaŵi ino ndi kuona mmene mungapangire masinthidwe kuti mukhale wokhoza kuthera maola pafupifupi aŵiri patsiku muutumiki. “Kuwombola” kwanu nthaŵi ku zochita zina kudzakulolani kupereka nthaŵi yowonjezereka kuntchito yolalikira.—Aef. 5:16, NW.
3 Lankhulanani ndi Kugwirizana: Mtumwi Paulo analankhula za anthu ena amene anali ‘omkhalira chomtonthoza’ pochita utumiki wake. (Akol. 4:11) Kambitsiranani makonzedwe anu ndi ena ofuna kulembetsa upainiya m’April. Chichirikizo chawo ndi kutsagana kungadzetse mapindu kwa nonsenu. Woyang’anira utumiki angakuthandizeni ngati muli ndi mafunso ponena za makonzedwe autumiki kapena ntchito ya m’gawo.
4 Kugwirizana ndi kuchirikizana kwa m’banja kungathandize ziŵalo zosiyanasiyana kuchita upainiya wothandiza. Ntchito zapanyumba zingafunikire kugaŵiridwa kwa ena kwakanthaŵi. Programu ya kusamalira ntchito zimenezi ingafunikirenso kusinthidwa. Kukambitsirana kwa banja ponena za zofunika zimenezi kungakhale kothandiza m’kukwaniritsa cholinga chanu. Kulankhulana kwabwino ndi kugwirizana ndiko chinsinsi cha chipambano.
5 Khalani ndi Malingaliro Otsimikiza: Musafulumire kuchotsapo lingaliro la upainiya wothandiza chifukwa cha mikhalidwe yosayanja. Achichepere amene ali pasukulu, anthu opuma pantchito, akazi apanyumba ndi ana, mitu ya banja yogwira ntchito za tsiku lonse, onsewo akhala okhoza kuchita kudzimana koteroko—ndipo atero mwachisangalalo—kuti achite upainiya wothandiza m’April. Iwo amavomerezana ndi wamasalmo kuti “owongoka mtima ayenera kulemekeza,” ndipo iwo sanaone kuchita zoyesayesa zowonjezereka kuti athere maola 60 muutumiki kukhala kowatayitsa zambiri. (Sal. 33:1) Ngati inu simutha kulembetsa, bwanji osakhala ndi phande m’chisangalalocho mwa kuwonjezera ntchito yanu monga wofalitsa wampingo?
6 Kwa ambiri, upainiya wothandiza mu April wakhala mwala wowolokera ku utumiki waupainiya wokhazikika. Pokhala atawonjezera kale ntchito yawo, anapeza kuti kusinthira ku ntchito yaupainiya wokhazikika kunakhaladi kosavuta.
7 Sosaite yalinganiza tsiku la magazini lapadera kwambiri. Tsikuli lidzakhala Loŵeruka loyamba la April. Nkhani yophunzira yachiŵiri mu Nsanja ya Olonda ya January 1, 1994, imapereka malingaliro angapo ogwira ntchito kaamba ka kusonkhezera utumiki umenewu. Mwezi wa May 1994 udzakhalanso wapadera wogaŵira magazini ndi masabusikripishoni m’munda ndi wolimbikitsira utumiki wa upainiya wothandiza. Komabe, magazini ayenera kugaŵiridwa mwachangu mwezi uliwonse. Kaamba ka chimenechi, mipingo ingalinganize masiku okhazikika amagazini ndi cholinga cha kukulitsa chisangalalo. Tiyeni tigwire ntchito mwauchamuna m’kufalitsa “chinenero choyera” mwa magazini.—Zef. 3:9, NW.