Zilengezo
◼ Mabuku ogwiritsira ntchito mu March: Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. April ndi May: Sabusikripishoni ya Nsanja ya Olonda. June: Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. CHIDZIŴITSO: Mipingo imene idzafuna zinthu za mkupiti zotchulidwazo iyenera kuziodetsa pa fomu yawo yotsatira ya mwezi ndi mwezi ya Literature Order (S-14).
◼ Kuyambira mlungu wa June 13, 1994, buku la Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe lidzaphunziridwa pa Phunziro Labuku Lampingo m’Chicheŵa.
◼ Aliyense wogwirizana ndi mpingo ayenera kutumiza masabusikripishoni atsopano ndi akulembetsanso onse a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, kuphatikizapo masabusikripishoni aumwini, kupyolera mumpingo.
◼ Woyang’anira wotsogoza kapena munthu wina wogaŵiridwa ndi iye ayenera kuŵerengera maakaunti ampingo pa March 1 kapena mwamsanga pambuyo pake. Lengezani kumpingo mutachita zimenezi.
◼ Mabuku Omwe Alipo:
Chingelezi: 1994—Yearbook of Jehovah’s Witnesses.
◼ Mabuku Omwe Mulibe m’Sitoko Kwachikhalire:
Chicheŵa: Mitu ya Nkhani ya Baibulo Yokambitsirana. Chingelezi: Mitu ya Nkhani ya Baibulo Yokambitsirana.