Misonkhano Yautumiki ya March
Mlungu Woyambira March 7
Mph. 15: Zilengezo za pampingo ndi Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Kambitsiranani “Phwando la Chikumbutso la 1994.”
Mph. 15: “Gwiritsani Chilengezo Chapoyera cha Chiyembekezo Chanu Mosagwedera.” Kukambitsirana kwa mafunso ndi mayankho kochitidwa ndi wochititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda. Pezani ndemanga kwa awo amene agonjetsa mantha a kuyankha pamisonkhano. Gogomezerani kufunika kwa kukonzekera kwapasadakhale. Limbikitsani mpingo kukonzekera kukhala ndi phande mokwanira m’phunziro lampingo la Nsanja ya Olonda mlungu uliwonse.
Mph. 15: “Gaŵirani Buku la Achichepere Akufunsa m’March.” Kukambitsirana ndi omvetsera. Khalani ndi ofalitsa okonzekera bwino lomwe akumasonyeza maulaliki a m’ndime 2 ndi 3. Pambuyo pachitsanzo chilichonse pemphani omvetsera kukambapo pazimene aphunzira m’chitsanzocho. Limbikitsani onse kukhala ndi mbali m’kugaŵira buku la Achichepere Akufunsa mwezi uno.
Nyimbo Na. 225 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira March 14
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Mbiri Yateokratiki. Sonyezani mfundo zachindunji m’magazini atsopano amene angagwiritsiridwe ntchito muutumiki wakumunda mlungu uno.
Mph. 15: “Kodi Mungawonjezere Chitamando Chanu kwa Yehova m’April?” Kukambitsirana kwa mafunso ndi mayankho. Pezani ndemanga kwa amene anachitapo upainiya wothandiza kumbuyoku. Aloleni afotokoze mmene anasinthira zochita zawo kuti akhoze kutenga mwaŵi umenewu. Limbikitsani onse amene akulinganiza kuchita upainiya wothandiza m’April kupereka mafomu awo mwamsanga.
Mph. 20: “Achititseni Kudzimva Olandiridwa pa Chikumbutso.” Kukambitsirana kwa mafunso ndi mayankho. Pambuyo pa ndime 3, khalani ndi chitsanzo chachidule cha mtumiki wotumikira yemwe akulandira munthu watsopano pa Chikumbutso.
Nyimbo Na. 150 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira March 21
Mph. 10: Zilengezo za pampingo, phatikizanipo lipoti la maakaunti ndi ziyamikiro za zopereka. Kambitsiranani bokosi la mutu wakuti “Chakudya cha Panthaŵi Yake.” Limbikitsani onse kuitanira okondwerera kunkhani yapadera imene idzaperekedwa pa April 10.
Mph. 20: “Athandizeni Kutsatira Mosamalitsa Malangizo ndi Chitsogozo cha Yehova Mulungu.” Kukambitsirana. Khalani ndi zitsanzo zokonzekeredwa bwino za maulaliki a m’ndime 2 ndi 3.
Mph. 15: “Msonkhano Wachigawo wa ‘Mantha Aumulungu’ wa 1994 wa Mboni za Yehova.” Kukambitsirana mphatika kwa mafunso ndi mayankho kochititsidwa ndi mlembi.
Nyimbo Na. 121 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira March 28
Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Kambitsiranani ndi kuchitira chitsanzo njira zoyenera zochitira umboni m’gawo lakumaloko ndi chogaŵira cha m’April. Simbani zokumana nazo zosonyeza mmene ofalitsa anapezera masabusikripishoni.
Mph. 15: Mwa kugwiritsira ntchito mfundo zazikulu zosankhidwa pamasamba 19-32 a 1994 Yearbook, mkulu afotokoza kufutukuka kwa padziko lonse kwa ntchito ya Ufumu ndi kugogomezera mbali zabwino za chichirikizo cha mipingo ya pamalopo. Sonyezani mmene Yehova akudalitsira molemeretsa anthu ake, kuphatikizapo awo opereŵera m’zimene angachite.
Mph. 15: “Mpatsi wa ‘Mphatso Iliyonse Yabwino.’” Nkhani yokambidwa ndi mkulu, yozikidwa pa Nsanja ya Olonda ya December 1, 1993, masamba 28-31.
Nyimbo Na. 15 ndi pemphero lomaliza.