Athandizeni Kutsatira Mosamalitsa Malangizo ndi Chitsogozo cha Yehova Mulungu
1 Ntchito yathu yolalikira imapatsa anthu mpata wa ‘kumva’ zifuno za Mulungu. (Aroma 10:13, 14) Zino zili “nthaŵi zoŵaŵitsa,” ngakhale kwa achichepere. (2 Tim. 3:1) Komabe, ndi chidziŵitso cha Mawu a Mulungu, iwo angapyole mwachipambano m’nthaŵi yovuta imeneyi. Miyoyo ili pangozi! Chotero tsimikizirani kubwererako kwa awo amene poyamba anasonyeza chikondwerero muumodzi wa maulaliki amene mwagwiritsira ntchito mwezi uno.
2 Ngati munagaŵira buku la “Achichepere Akufunsa,” munganene kuti:
◼ “Ndakondwa kuonananso nanu. Pamene tinakambitsirana nthaŵi ija, tinakamba za mikhalidwe yambiri yatsopano imene achichepere amayang’anizana nayo imene imafuna kuti iwo apange zosankha, ndipo ndinakusiyirani buku limene limafotokoza mmene angachitire zimenezo. Ndiyesa munaona kuti ngakhale kuti buku la Achichepere Akufunsa lakonzedwera kuthandiza achichepere, limathandizanso makolo kukambitsirana ndi ana awo za miyezo yolungama. Kodi muganiza kuti phunziro la Baibulo lingathandize achichepere kuchita ndi vutoli? [Yembekezerani yankho.] Buku limeneli limakusonyezani mmene Baibulo lingathandizire achichepere kuchita ndi mikhalidwe yovuta, yonga ija yondandalikidwa pampambo wa zamkatimu.” Ndiyeno tsegulani pamutu woyenerera umene mungagwiritsire ntchito kuyambira phunziro la Baibulo la panyumba.
3 Ngati munagaŵira trakiti la “Kodi Dzikoli Lidzapulumuka?” paulendo wanu woyamba, munganene zonga izi:
◼ “Ndakondwa kukupezani panyumba. Pamene ndinakuchezerani posachedwapa, tinakambitsirana za zochitika zopanga chizindikiro chimene chikaonekera mapeto a dziko atatsala pang’ono kudza. [Pendani mbali zoyenerera za chizindikiro pa Mateyu 24:3-14.] Kodi mwaona chochitika chilichonse chimene chachitika posachedwapa m’dziko kapena kwathu kuno chimene muganiza kuti mwina chingakhale kukwaniritsidwa kwa mbali ya chizindikirocho?” Mukumagwiritsira ntchito mfundo za m’mutu 38 m’buku la Achichepere Akufunsa, pamasamba 306-7, kambanipo pa kukwaniritsidwa kwa ena a maulosi a Baibulo ameneŵa. Pamapeto a kuchezako, tchulani mutu wa nkhani yapoyera ya mlunguwo, ndipo itanirani mwininyumbayo ku Nyumba Yaufumu.
4 Ngati munaitanira mwininyumba ku Chikumbutso, nenani kuti:
◼ “Paja pamene ndinakuchezerani, tinakambitsirana za mmene imfa ya Yesu ilili yofunika kwa anthu. Ndiponso ndinakuitanirani kupezeka pa Chikumbutso cha imfa yake, chimene chidzachitidwa ndi Akristu padziko lonse pa March 26. Ndabwera lero kudzakukumbutsani kuti mukuitanidwa ku chochitika chofunika chimenecho. [Tchulani nthaŵi ndi malo a phwandolo.] Mwina kungakuthandizeni kumvetsetsa tanthauzo la chochitikacho ngati tingapende madalitso amene tili nawo tsopano chifukwa cha zimene Yesu anachitira mtundu wa anthu, limodzi ndi madalitso amtsogolo.” Ndiyeno yesayesani kukambitsirana mfundo zoyenerera za m’magazini aposachedwapa kapena za m’mutu 39 m’buku la Achichepere Akufunsa. Ndiponso mungagogomezere kufunika kwa misonkhano Yachikristu pamasamba 316-17. Ngati kutheka, pangani makonzedwe othandiza wokondwererayo kupezeka pa Chikumbutso.
5 Ngati munthuyo anali chabe womvetsera wabwino, mwina zotsatirazi zingakhale zothandiza:
◼ “Ndinakondwera kwambiri ndi kukambitsirana kwathu kwaposachedwapa ponena za Baibulo. Ndabweranso chifukwa chakuti ndifuna kuti mukapeze zimene Mulungu walonjeza kwa awo amene afuna kuphunzira zambiri ponena za iye.” Ŵerengani Yohane 17:3, ndiyeno pitani ku trakiti la Moyo m’Dziko Latsopano la Mtendere.
6 Kukonda kwanu moyo ndi chiyamikiro kaamba ka dipo zikusonkhezerenitu kuchita maulendo obwereza kwa okondwerera. Athandizeni kuphunzira zambiri ponena za Ufumu wa Mulungu. Ayenera kulimbikitsidwa kupezeka pamisonkhano nthaŵi zonse ndi anthu a Yehova.—Aheb. 10:24, 25.