Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/98 tsamba 8
  • Itanani Aliyense Waludzu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Itanani Aliyense Waludzu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Nkhani Yofanana
  • Zitsanzo za Maulaliki a Utumiki wa Kumunda
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Kulalikira Uthenga Wabwino Mwachangu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Maulaliki Amene Mungagwiritse Ntchito mu Utumiki wa Kumunda
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Dalirani Yehova Kuti Akulitse Zinthu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
km 2/98 tsamba 8

Itanani Aliyense Waludzu

1 Monga momwe mneneri Amosi ananeneratu, lerolino anthu ‘ngaludzu, osati ludzu la madzi, koma lakumva mawu a Yehova.’ (Amosi 8:11) Kuti tithandize anthu a m’dziko louma mwauzimuli, timawauza za makonzedwe a Mulungu owombolera anthu omvera ku uchimo ndi imfa, omwe asonyezedwa m’chaputala chomaliza cha Chivumbulutso kuti ndi mtsinje wa madzi a moyo.” Tili ndi mwaŵi wakuitana aliyense waludzu la chilungamo ‘kudzatenga madzi a moyo kwaulere.’ (Chiv. 22:1, 17) Kodi zimenezo tingazichite bwanji mu February muno? Mwa kugaŵira anthu ofunitsitsadi brosha lakuti, “Tawonani! Ndikupanga Zonse Zatsopano.” Mwina mungakonde kuyesa maulaliki awa:

2 Popeza anthu ambiri ali ndi mabaibulo m’nyumba zawo, mwina mungaone kuti njira iyi njogwira mtima:

◼ “Anthu ambiri omwe ali ndi Baibulo angakonde kudziŵa zimene limatiuza ponena za Yehova. Kapena mwaganizapo za nkhani imeneyi. [Yembekezerani yankho.] Ndingakonde kukuuzani zimene ine ndadziŵa. [Tengani Baibulo lanu nkulitsegula.] Chonde ŵerengani nane Yohane 4:24.” Ndiyeno ŵerengani ndime 13 ndi 14 m’brosha la “Tawonani!,” mukumafunsa mafunso omwe ali mmunsi mwa ndimezo. Malizani mwa kunena kuti: “Brosha limeneli likufotokoza mmene paradaiso adzakhalira.” Ngati mwini nyumbayo walikondadi, gaŵirani broshalo pa chopereka cha K3.60. Panganani kuti mudzabwererekonso.

3 Mutabwererako, mungapitirize nkhani yanu ija mwa kunena kuti:

◼ “Nthaŵi ija pamene ndinafika pano, tinakambitsirana za chimene Baibulo limatiuza ponena za Yehova. Kodi mukudziŵa chifukwa chake tiyenera kudziŵa zambiri za iye? [Yembekezerani yankho.] Tamvani mawu odabwitsawa.” Ŵerengani Yohane 17:3. Kenaka tsegulani patsamba 8 m’brosha la “Tawonani!” ndiyeno kambitsiranani zili m’ndime 15-17, mukumafunsa mafunso ogwirizana ndi ndimezo ndi kuyang’ana malemba angapo omwe atchulidwamo. Fotokozani kuti Mulungu alibe mbali m’nkhondo zamitundu. Panganani kuti mudzabwererenso kuti mukakambitsirane ndime 18-20 m’brosha lomwelo.

4 Ngati anthu akhala akunenanena za nkhani ina ya panyuzi yokhudza imfa yadzidzidzi, mwina mungayese njira iyi:

◼ “Mwinatu mwamva za [tchulani nkhani ya panyuziyo]. Miyoyo ikamawonongeka mwatsoka chonchi, ambiri samadziŵa kuti angatonthoze bwanji mabanja ofedwawo. Mukuganiza kuti tingatani? Yembekezerani yankho. Ndiyeno tsegulani patsamba 20 m’brosha la “Tawonani!” ndipo msonyezeni chithunzi chachiukiriro chimene chili pamenepo. Pitirizani kuti: “Ambiri amadabwa akamva kuti olungama ndi osalungama omwe adzaukitsidwa m’Paradaiso padziko lapansi. [Ŵerengani Machitidwe 24:15 yomwe yatchudwa m’ndime 41 patsamba 21 ndiye fotokozani zimene zili m’ndime 42.] Broshali likulongosola nkhani zina zosangalatsa ponena za chifuno cha Mulungu chamtsogolo. Ngati mungakonde kudziŵa zambiri, mungatsale nalo broshali pachopereka cha K3.60.” Panganani kuti mudzabwererenso, mutaonetsetsa chimene chamsangalatsa kwenikweni munthuyo ndi chimenenso chamdetsa nkhaŵa.

5 Mutabwererako, sinthani ulaliki wanu kuti uyenerane ndi mwini nyumba. Mwina munganene kuti:

◼ “Nthaŵi imene tinacheza ija, ndinakonda mawu omwe munanena za chiukiriro. [Bwerezaninso mawuwo.] Ndapeza nkhani ina imene ndikuganiza kuti muikonda.” Tsegulani brosha la “Tawonani!” patsamba 3. Ŵerengani ndi kukambitsirana zili m’ndime 1-4 ndiponso malemba ena ambiri ndithu omwe akupezeka m’mawu am’tsinde patsamba 4, omwe akuchirikiza ndimezo. Mutasankha nthaŵi imene mudzabwererako kukapitiriza kukambitsiranako, mfotokozereni mwini nyumbayo za nthaŵi zamisonkhano yampingo. Mfotokozereni za Msonkhano Wapoyera, ndipo mpempheni kudzapezekapo.

6 Ngati mukufuna ulaliki wosavuta wofuna kusonyeza trakiti, munganene izi:

◼ “Ndingakonde kukupatsani trakiti ili lakuti Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Kaamba ka Akufa Okondedwa?” Liperekeni kwa mwini nyumbayo, ndipo mpempheni kuti azikutsatirani mmene mukuŵerenga ndime yoyamba. Mloleni ayankhe funso lafunsidwa kumapeto kwa ndimeyo. Ŵerengani ndime yachiŵiri, kenaka tsegulani pachithunzi cha patsamba 20 m’brosha la “Tawonani!” Pitirizani kuti: “Broshali likufotokoza zambiri ponena za chiukiriro ndi zinanso zosangalatsa zimene Baibulo likulonjeza kuti zidzachitika mtsogolo. Landirani broshali pa chopereka cha K3.60.” Konzani kuti mudzapange ulendo wobwereza.

7 Tikamaitana ena mowakopa, angabwere kumadzi a moyo, omwe Yehova akupereka tsopano lino. Choncho, tiyeni tinene kwa aliyense waludzu kuti, “Idzani”!—Chiv. 22:17.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena