“Chitani Ichi Chikhale Chikumbukiro Changa”
1 Anthu amakonda kuiŵala kufunika kwa zinthu zina zofunika m’kupita kwa nthaŵi. Chimenechi nchifukwa china chimene Yesu, pokhazikitsa “Mgonero wa Ambuye,” analamulira ophunzira ake kuti: “Chitani ichi chikhale chikumbukiro changa.” Kungoyambira pamenepo, likafika tsiku la imfa ya Yesu, Akristu momvera ‘amalalikira imfa ya Ambuye kufikira akadza Iye.’—1 Akor. 11:20, 23-26.
2 Posachedwapa tsopano, Yesu adzalandira kumwamba otsirizira otsalira a “kagulu ka nkhosa” omwe akucheperachepera. (Luka 12:32; Yoh. 14:2, 3) Chaka chinochi otsalira odzozedwa limodzi ndi khamu lalikulu lomakulakula la “nkhosa zina” adzakhala nawonso pa Mgonero wa Ambuye, pa April 11. (Yoh. 10:16; Chiv. 7:9, 10) Tidzawonjezera kuyamikira kwathu chikondi chachikulu cha Yehova potumiza Mwana wake wobadwa yekha kuti apindulitse anthu. Zimene zidzagogomezeredwa ndizo chitsanzo cha Yesu, chikondi chake, kukhulupirika kwake mpaka imfa popereka dipo, ndi kuti tsopano ali Mfumu yolamulira ya ufumu wa Mulungu wokhazikitsidwa, ndiponso madalitso amene Ufumuwo udzapatsa anthu. Ndithudi nchochitika chosaiŵalika!
3 Konzekerani Tsopano: Tonsefe tiyeni tiyesetse kuti kwa ife enife ndi kwa ena onse omwe adzasonkhana nafe, nyengo ya Chikumbutso ino ikhale yosangalatsa ndi yakuyamikira. Tingakonzeketse mtima wathu mwa kuŵerenganso nkhani za m’Baibulo zonena za masiku oŵerengeka otsirizira a utumiki wa Yesu ndi zimene zinachitika atatsala pang’ono kufa. Pamilungu ingapo Chikumbutsocho chisanafike, mwina phunziro lathu la banja lingakhale kukambitsirana mitu 112-16 m’buku la Munthu Wamkulu.
4 Kodi ndi angati omwe mumadziŵa omwe angafike pa Chikumbutso mutawathandiza kuzindikira kufunika kwa chochitikacho, kenako mutawaitanira kumeneko, ndi kuwatsimikizira kuti ali olandiridwa? Lembani mndandanda wa mainawo tsopano, ndipo athandizeni kuti adzapezekepo. Pambuyo pa zimenezo, athandizeni kukulabe mwauzimu mwa kuwalimbikitsa kumapezeka pamisonkhano nthaŵi zonse.
5 M’nyengo ya Chikumbutso, padzakhala makonzedwe apadera a kuwonjezera mipata ya aliyense yolalikira. Mutalinganiza zinthu bwino, kodi mungachite upainiya wothandiza m’April kapena m’May? Imodzi mwa njira zabwino kwambiri zosonyeza kuti timakumbukira moyamikira zonse zimene nsembe ya Yesu imatanthauza kwa ife ndiyo kulankhula za Mulungu wathu, Yehova, ndi za madalitso amene ulamuliro wa Ufumu wochitidwa ndi Mwana wake udzabweretsa.—Sal. 79:13; 147:1.