Ananu—Mumatisangalatsa Kwabasi!
1 Anyamata ndi atsikana inu, kodi mumalidziŵa lamulo la Yehova lakuti muziphatikizidwa pantchito zampingo? (Deut. 31:12; Sal. 127:3) Nzosangalatsa kukhala nanu pafupi polambira Yehova pamodzi! Mitima yathu imasangalala mukakhala phee pamisonkhano nkumamvetsera mwatcheru. Chimene chimatikondweretsa kwenikweni mpamene mumayesa kuyankha ndi mawu anuanu. Mpingo wonse umakondwa mukamakamba nkhani zanu pa Sukulu Yautumiki Wateokratiki, mukamatsagana nafe mofunitsitsa mu utumiki wakumunda, ndiponso tikamamva kuti mumachitira umboni molimba mtima kwa anzanu a kusukulu ndi kwa aphunzitsi.—Sal. 148:12, 13.
2 Tikufuna kuti mudziŵe kuti timasangalala tikamaona makhalidwe anu abwino, mutavala bwino, mayendedwe anu oyera, ndi ulemu umene mumapatsa achikulire. Timasangalala mosaneneka tikamaona kuti ‘mukukumbukira Mlengi wanu’ mwa kudziikira zolinga zateokrase.—Mlal. 12:1; Sal. 110:3.
3 Tatiuzani Zolinga Zanu: Mnyamata wina wazaka zisanu ndi zitatu anauza woyang’anira chigawo kuti: ‘Choyamba ndikufuna kudzabatizidwa, kenaka ndingakonde kudzamathandiza mumpingo mwa kusamalira zokuzira mawu ndi mamaikolofoni, kuti ndidzakhale kalinde, nandimathandiza kusamalira mabuku, nzidzaŵerenga pamaphunziro a buku ndi pa Maphunziro a Nsanja ya Olonda. Kenaka ndingakonde kudzakhala mtumiki wotumikira, ndiyeno mkulu. Ndingakondenso kudzakhala mpainiya nkudzapita kusukulu ya apainiya. Ndiyeno ndingakonde kudzapita ku Beteli, nkudzakhala woyang’anira dera kapena woyang’anira chigawo.’ Ameneyotu anasonyeza kuti amayamikira mwaŵi wakutumikira Mulungu!
4 Mmene mukukula mwakuthupi ndi mwauzimu, timakondwa kukuonani mukufikira zolinga zanu. (Yerekezerani ndi Luka 2:52.) Chaka chilichonse, ena a inu zikwizikwi mumakhala ofalitsa osabatizidwa ndiyeno m’madzayenerera kubatizidwa nkukhala atumiki odzipatulira kwa Yehova. Kenaka timadzapambana kukondwa tikamakuonani mukukalimira upainiya wothandiza ngakhale kuloŵa utumiki wanthaŵi zonse. Ndithudi, ananu mumatisangalatsa kwabasi ndipo mukuchititsa Atate wathu wakumwamba kulandira chitamando chodabwitsa. Yehova akudalitseni zedi!—Miy. 23:24, 25.