Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/98 tsamba 2
  • Misonkhano Yautumiki ya March

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Misonkhano Yautumiki ya March
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira March 2
  • Mlungu Woyambira March 9
  • Mlungu Woyambira March 16
  • Mlungu Woyambira March 23
  • Mlungu Woyambira March 30
Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
km 3/98 tsamba 2

Misonkhano Yautumiki ya March

Mlungu Woyambira March 2

Nyimbo Na. 3

Mph. 8: Zilengezo zapampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu.

Mph. 15: “Chitani Ichi Chikhale Chikumbukiro Changa.” Nkhani yokamba mkulu. Kambanipo mwachidule za m’buku la Uminisitala Wathu, pamasamba 80-1, kugogomezera kuti nkofunika kupezeka pa Chikumbutso.

Mph. 22: “Dziŵitsani Ena za Chiyembekezo cha Moyo Wosatha.” Nkhani yokambitsirana ndi omvetsera. Fotokozani mwachidule mmene munthu angagwiritsire ntchito bwino mafunso kuti apitirize kukambitsirana. Perekani zitsanzo zina za mafunso otsogolera ndi mafunso opempha maganizo amene angagwiritsiridwe ntchito paulaliki. (Onani Bukhu Lolangiza la Sukulu, masamba 51-2, ndime 10-12.) Wofalitsa wina waluso achitire chitsanzo umodzi mwa maulaliki oyambawo limodzi ndi ulendo wobwereza, namasonyeza kuyambika kwa phunziro la Baibulo.

Nyimbo Na. 88 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira March 9

Nyimbo Na. 60

Mph. 8: Zilengezo zapampingo. Lipoti la maakaunti.

Mph. 15: Pindulani Kwambiri ndi 1998 Yearbook. Tate akupenda masamba 3-6, 31 ndi banja lake, omwe akusonyeza zipambano zateokrase za chaka chatha padziko lonse. Akukambitsirana mmene banja limapindulira poŵerenga lemba la tsiku ndi kukambitsirana pamodzi nkhani za mu Yearbook panthaŵi yakudya, natsimikiza kumachita zimenezo chaka chonse.

Mph. 22: “Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova Wakuti “Njira ya Moyo ya Mulungu.” Mlembi asamalire nkhaniyi mwa mafunso ndi mayankho m’mphatika, pandime 1-5. Mwa malemba, gogomezerani kufunika kwa kutsatira malangizo a Sosaite. Yamikirani abale kaamba kotsatira malangizo a Sosaite.

Mlungu Woyambira March 16

Nyimbo Na. 43

Mph. 5: Zilengezo zapampingo. Itanani onse okondwerera kuti adzamvetsere nkhani yapadera pa March 29. Nkhaniyo ili ndi mutu wakuti “Chifukwa Chake Mungakhulupirire Baibulo.”

Mph. 20: “Kodi Misonkhani Yathu Yachikristu Muyenera Kuiona Bwanji?”

Mph. 20: “Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova Wakuti “Njira ya Moyo ya Mulungu.” Nkhani ya mafunso ndi mayankho ya m’mphatika ya msonkhano wachigawo, ndime 6-11. Isamaliridwe ndi mlembi.

Nyimbo Na. 224 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira March 23

Nyimbo Na. 94

Mph. 10: Zilengezo zapampingo. Alimbikitseni onse kuyamba kuitanira okondwerera ku Chikumbutso, pa April 11. Lengezani maina onse a amene adzachita upainiya wothandiza m’April. Fotokozani kuti sikuchedwa kupereka fomu yofunsirapo tsopano. Longosolani dongosolo lonse la misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda m’April.

Mph. 20: Konzekeretsani Atsopano Kuloŵa m’Utumiki Wakumunda. Nkhani ndi kukambitsirana ndi omvetsera. Amene akuchititsa phunziro m’buku la Chidziŵitso angaganize zokonzekeretsa wophunzira wawo kutsagana nawo ku utumiki wakumunda. Fotokozani zimene zalongosoledwa m’buku la Chidziŵitso, masamba 105-6, ndime 14, ndi patsamba 179, ndime 20. Pendani kachitidwe kake mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 1988, masamba 16-17, ndime 7-10, mmene atsopano angakhalire ofalitsa osabatizidwa. Onani malingaliro ali m’mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa June 1996, ndime 19, othandizira ofalitsa atsopano osabatizidwa kuyamba kutumikira.

Mph. 15: Bokosi la Mafunso. Mafunso ndi mayankho. Mkulu akupenda nkhani ya m’buku la Uminisitala Wathu, tsamba 131, ndime 1 ndi 2.

Nyimbo Na. 47 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira March 30

Nyimbo Na. 29

Mph. 12: Zilengezo zapampingo. Kumbutsani onse kuti apereke malipoti awo a utumiki wakumunda a March. Sonyezani makope atsopano a magazini, tchulani nkhani zimene angaziunike powagaŵira, tchulaninso mfundo zina zokambitsirana. Pendani “Zokumbutsa za Chikumbutso,” ndiyeno fotokozani makonzedwe a Chikumbutso pampingo wanu. Tonse tikonzekere kuthandiza ophunzira Baibulo ndi okondwerera enanso kuti adzapezekepo. Akumbutseni onse kuti atsimikize kutsatira ndandanda ya kuŵerenga Baibulo ya Chikumbutso, ya April 6-11, yomwe ili mu Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku.

Mph. 13: “Ananu—Mumatisangalatsa Kwabasi!” Mafunso ndi mayankho. Simbani chokumana nacho cha mu Nsanja ya Olonda ya August 1, 1987, tsamba 25.

Mph. 20: Njira Zogonjetsera Kutopa Kwauzimu. Akulu aŵiri akambitsirane za m’bokosi la mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 1986 tsamba 19. Pa chilichonse cha “Zizindikiro za Kutopa,” fotokozani mwa Malemba mmene munthu angapindulire ndi “Zithandizo za Kupirira.” Ndiyeno funsani ofalitsa aŵiri asimbe mmene anathandizikira kupezanso nyonga yawo yauzimu atagwiritsira ntchito mfundo zimenezo.

Nyimbo Na. 140 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena