Achinyamata—Kodi Zolinga Zanu Zauzimu Nzotani?
1 Yehova amadziŵa mmene ntchito yofunika ndi zolinga zofikirika zimapatsira chimwemwe. (Onani Genesis 1:28; 2:15, 19.) Lerolino, Yehova wapatsa anthu ake ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa. Ndiponso tili ndi cholinga chachikulu chopeza moyo wosatha m’Paradaiso. Pakali pano, tiyenera kumadziikira zolinga zauzimu za kupita patsogolo kuti tisawonongere nyonga yathu pachabe.—1 Akor. 9:26.
2 Zolinga Zofikirika za Achinyamata: Achinyamata afunikira kukhala ndi zolinga zateokrase zimene angafikire malinga ndi maluso awo. (1 Tim. 4:15) Ana ena aang’ono kwambiri afikira cholinga choloŵeza mabuku a Baibulo asanaphunzire kuŵerenga. Kupyolera m’phunziro la banja, ana amaphunzira kukonzekera misonkhano kuti afikire zolinga zopereka ndemanga zatanthauzo ndi kudzilembetsa mu Sukulu Yautumiki Wateokratiki. Mmene ana akutsagana ndi makolo awo mu utumiki wakumunda, amaphunzira kutengamo mbali pochitira umboni mpaka kufikira cholinga chokhala ofalitsa osabatizidwa. Makolo ayenera kumakumbutsa ana awo aang’ono za cholinga chodzipatulira ndi ubatizo.
3 Ngati muli wachinyamata, kodi zolinga zanu zauzimu zikuphatikizapo chiyani? “Ukumbukirenso Mlengi wako” mwa kulunjika zolinga zofunika kwambiri pamoyo. (Mlal. 12:1; Sal. 71:17) Bwanji osachita upainiya wothandiza m’miyezi yanu yopuma kusukulu? Kodi mwalingalirapo zouchita utumiki umenewu nthaŵi zonse monga mpainiya wokhazikika? Kodi simungaphunzire chinenero chatsopano kuti mtsogolomu muthe kuthandiza anthu azinenero zina kapena mipingo m’dera lanu kapena kwina? Ambiri amene tsopano akutumikira pa Beteli kapena oyang’anira oyendayenda kapena amishonale anadziikira cholinga chawo cha utumiki wanthaŵi zonse adakali kusukulu. Bwanji osatero nanunso?
4 Pamene mudakali wamng’ono, yesetsani kutsanzira chitsanzo cha Yesu. Ngakhale pausinkhu wa zaka 12, analankhula nkhani zauzimu momasuka. (Luka 2:42-49, 52) Kudziikira zolinga zopindulitsa monga kukhala ndi phunziro laumwini, kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku, ndi kucheza nthaŵi zonse ndi Akristu achidziŵitso pamisonkhano ndi mu utumiki kudzakuthandizani kupeza maluso ophunzitsira ena za Ufumu wa Mulungu mmene Yesu anachitira.