Misonkhano Yautumiki ya June
Mlungu Woyambira June 2
Mph. 8: Zilengezo zapamalopo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Fotokozani lipoti la utumiki wakumunda m’February, la m’dzikomo ndi la mumpingo.
Mph. 15: “Chitani Changu.” Mafunso ndi mayankho.—Onaninso Nsanja ya Olonda ya April 15, 1993, masamba 28-30.
Mph. 22: “Chidziŵitso Chochokera kwa Mulungu Chimayankha Mafunso Ambiri.” Tcheyamani akukambitsirana nkhaniyo ndi ofalitsa aŵiri kapena atatu, kuphatikizapo wachinyamata. Kambanipo pa ndime 1, kugogomezera mmene buku la Chidziŵitso limatithandizira poyankha mafunso. Sonyezani chitsanzo choyeseza ulaliki, ndipo tchulani mbali zofunika kuwongolera pambuyo pa ulaliki uliwonse.
Nyimbo Na. 200 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira June 9
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 15: Zikumbutso za m’Chilimwe. Nkhani yokamba yophatikizapo kukambitsirana ndi omvetsera. Ambiri a ife timalinganiza zochita zochuluka m’chilimwe, ndipo zimenezo zingaphatikizepo tchuti, kuchezera achibale, kapena kusanguluka. Kodi tingalinganize bwanji zinthu kuti tisanyalanyaze zochita zateokrase? Kambitsiranani zotsatirazi: (1) Kupezeka pa msonkhano wachigawo masiku onse atatu. (2) Kupezekanso pa misonkhano nthaŵi zonse, kaya tili kwathu kapena kwina. (3) Kulinganiza kukhala ndi mbali nthaŵi zonse mu utumiki, ndipo ngati tili kumalo akutali, kutumiza malipoti a utumiki wakumunda ku mpingo. (4) Kunyamula mabuku ochitira umboni wamwamwaŵi pamene tili paulendo. (5) Kuchita zambiri mu umboni wamadzulo. (6) Kulembetsa upainiya wothandiza kwa mwezi umodzi kapena ingapo. (7) Akulu akumalinganiza zochita zampingo ndi kuona kuti pamene wina palibe mbali yake ikusamalidwa ndi wina.
Mph. 20: Kuphunzitsa Ena—Kukufunika Mwamsanga. Nkhani ya mkulu. Pendani lipoti la utumiki ladziko lonse la chaka cha 1996 patsamba 33 mu Yearbook ya 1997. Kuyesayesa kwakhama kuchitira umboni kulikonse kumene anthu angapezeke kukubala zipatso. Chofunika msanga tsopano ndicho kubwerera kumene tinasiya mabuku ndi kukawaphunzitsa anthu choonadi. Ngati tawapeza pamakwalala, tiziwapempha mwaluso dzina ndi keyala yawo kuti tidzawachezerenso. Sitiyenera kungobzala chabe mbewu za Ufumu; tiyeneranso kuzithirira. (1 Akor. 3:6-8) Ngati tabzala mbewuyo panthaka yabwino, kuphunzitsa kogwira mtima kungamthandize munthuyo kudziŵa tanthauzo lake. (Mat. 13:23) Tiyenera kukhala ndi mbali mokwanira ndi mwaluso pantchito yophunzitsayi. (Aheb. 5:12a) Phatikizanipo mfundo zili m’mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa June 1996, ndime 25-6. Gogomezerani kuyesayesa kuyamba maphunziro kaya m’brosha la Mulungu Amafunanji kapena m’buku la Chidziŵitso.
Nyimbo Na. 204 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira June 16
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Sonyezani mfundo zokambitsirana zili m’magazini atsopano.
Mph. 15: Zosoŵa zapamalopo.
Mph. 20: Kuzindikira Chipembedzo Chanu Monga Choona Kapena Chonyenga. Mkulu akukambitsirana ndi ofalitsa aluso aŵiri kapena atatu nkhani yochokera mu Galamukani! ya January 8, 1990, tsamba 26. Anthu oona mtima akufikiridwa kaŵirikaŵiri. Komabe, sanavomerezepo phunziro la Baibulo. Kambitsiranani mmene tingagwiritsire ntchito mfundo za nkhani ya mu Galamukani! imeneyi kuwaonetsa kuti afunikira kuchita mogwirizana ndi chidziŵitso cholongosoka. Tchulaninso mfundo zofunika m’buku la Chidziŵitso, mutu 5: “Kodi Mulungu Amavomereza Kulambira kwa Yani?” Ŵerengani ndime 20. Tingabwerere kwa anthu oterowo kukawalimbikitsa mokoma mtima ndi mwaluso kuti tiziphunzira nawo ndikuti azipezeka pamisonkhano.
Nyimbo Na. 201 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira June 23
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo.
Mph. 15: Kodi Akuti Bwanji za Ife? Nkhani yozikidwa pa chidziŵitso chochokera mu Watch Tower Publications Index 1986-1995, masamba 341-3. Sankhani ndemanga zabwino kwambiri “Zimene Ena Amanena” ponena za Mboni za Yehova—khalidwe lathu ndi ntchito yathu. Sonyezani mmene ena achitira chidwi ndi zimene amaona mwa ife. Fotokozani chifukwa chake zimenezi ziyenera kutisonkhezera kusunga mayendedwe abwino nthaŵi zonse ndi kulimbikira ntchito yathu. Sonyezani mmene tingagwiritsire ntchito ndemanga zabwinozo pamene tikulankhula ndi anansi ndi anthu okondwerera amene akufuna kudziŵa zambiri za ife.
Mph. 20: “Makolo—Phunzitsani Ana Anu Kulalikira.” Mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo malangizo ali m’buku la Uminisitala Wathu, pamasamba 99-100, pakamutu kakuti “Kuthandiza Anthu Achichepere.”
Nyimbo Na. 211 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira June 30
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Akumbutseni onse kupereka malipoti autumiki wakumunda a June.
Mph. 20: “Achinyamata—Kodi Zolinga Zanu Zauzimu Nzotani?” Atate aŵiri akukambitsirana nkhaniyo. Akukambitsirana mmene angathandizire ana awo kuzindikira chifukwa chake kuli kofunika kudziikira zolinga zateokrase, zimene zidzawapatsa madalitso auzimu, m’malo mokonda zinthu zakuthupi.—Onaninso buku la Uminisitala Wathu, pamasamba 116-18.
Mph. 15: Kukonzekera Buku Logaŵira m’July. Tengani brosha limodzi kapena aŵiri amene anakondedwa m’gawo la kwanuko, ndipo pendani mfundo zina zazikulu za m’mabroshawo. Sonyezani mmene tingaziphatikizire mfundozo mu ulaliki. Akumbutseni onse kulemba mabuku amene agaŵira ndi kubwererako kukakulitsa chidwi.
Nyimbo Na. 109 ndi pemphero lomaliza.