Msonkhano Wachigawo wa “Mantha Aumulungu” wa 1994 wa Mboni za Yehova
1 Mawu achiyamikiro chochokera pansi pamtima kaamba ka programu yotsitsimula mwauzimu anamvedwa kuchokera kwa ambiri mwa okwanira 317,357 amene anapezeka pa Misonkhano Yachigawo ya “Chiphunzitso Chaumulungu” ya 1993 m’gawo la nthambi ya Zambia. Atsopano amene anabatizidwa monga chotulukapo cha kutchera khutu kwawo ku chiphunzitso chaumulungu chopezeka m’Baibulo anafika chiwonkhetso cha 1,975. Kusangalala kwathu ndi programu yomangirira yoteroyo chaka chatha kuyenera kutisonkhezeradi kupanga kuyesayesa kulikonse kwakuti tikapezeke pa programu yotsitsimula yomwe ikulinganizidwa kaamba ka Misonkhano Yachigawo ya “Mantha Aumulungu” ya 1994 m’chilimwe chilinkudza. Poona mavuto ochuluka amene mtundu wa anthu ukuyang’anizana nawo lerolino, ndithudi tonsefe tidzaitanira ophunzira Baibulo athu ndi kupanga makonzedwe akuti akakhalepo limodzi nafe. Kudzakhaladi kolimbikitsa kwambiri ndi kopatsa nyonga pamene tikupitiriza kutumikira Yehova ndi mantha aumulungu mosasamala kanthu za zopinga zilizonse zimene zingatigwere m’masiku alinkudza.
2 Khalani wotsimikizira kupanga makonzedwe anu amsonkhano wachigawo mosamalitsa ndi mwapemphero kotero kuti mukakhalepo ndi kusangalala ndi masiku onse atatu a programu yauzimu yokomayo, kuyambira panyimbo yoyambira mpaka papemphero lomalizira. Mwachikondi, phatikizani m’makonzedwe anuwo awo amene angafunikire chithandizo, makamaka okondwerera chatsopano, kotero kuti nawonso akapezeke pa gawo lililonse. Kukakhala kothandiza kwambiri kukambitsirana za m’mphatika inoyi limodzi ndi ophunzira Baibulo alionse amene angakonzekere kukapezekapo. (Agal. 6:10) Programu idzayamba ndi nyimbo zamalimba pa 9:20 a.m. patsiku loyamba ndipo idzatha pafupifupi ndi 4:00 p.m. Patsiku lachiŵiri programu idzayamba ndi 9:00 a.m. ndi kutha ndi nyimbo ndi pemphero pafupifupi ndi 4:30 p.m. Gawo la mmaŵa patsiku lomalizira lidzayamba ndi 9:30, ndipo programu ya tsikulo idzatha pafupifupi ndi 4:15 p.m. Chidziŵitso chotsatirachi chidzakuthandizani popanga makonzedwe oyambirira.
3 Kuchinjiriza Moto ndi Ngozi Zina: Mosakayikira konse, chochititsa ngozi za moto chachikulu pamisonkhano yachigawo, sindicho kuphikira chakudya pafupi ndi misasa, koma ana osayang’aniridwa amene amaseŵera kapena kusamalira moto. Chifukwa chake, kaamba ka chisungiko chanu ndi cha abale anu, musalole ana anu kuyendayenda okha; musaike ana aang’ono kusamalira madzi oŵira, kapena m’njira zina kusamalira moto wophikira. Iwo angakhale okhoza kuchita zinthuzi bwino lomwe kunyumba, koma malo amsonkhano ali osiyana ndipo pamafunikira chisamaliro chapadera kuti tiletse ngozi kuchitika. Anthu ambiri amakhala pafupipafupi, ndipo ana amakonda kuchita maseŵera pamene ali ndi ana anzawo. Iwo amachenjeneketsedwa mosavuta ndipo samaoneratu ngozi, motero kaamba ka zifukwa zimenezi sitiyenera kupatsa ana makendulo, machisa kapena nyali. Vuto lina limabuka pamene makolo apita kumaprogramu mkati mwa tsiku ndi kusiya ana aang’ono osayang’aniridwa kumsasa. Ana ayenera kukhala ndi makolo awo mkati mwa programu. Pamene akalinde aona ana akuyendayenda okha pamalo amsonkhano, ayenera kubwezera anawo kwa makolo awo. Makolo inu! chonde gwirizanani ndi ogwira ntchito pamsonkhano ndipo mwanjirayi “kondani abale.”—1 Pet. 2:17.
4 Gulu la Yehova mwachikondi limapereka zikumbutso za panthaŵi yake ponena za misonkhano yaikulu. Nzachisoni kunena kuti pamisonkhano yachigawo ingapo chaka chatha m’Zambia, osonkhana ena anatayikiridwa katundu wawo m’ngozi za moto zimene zikanapeŵedwa. Awo abale okhala ndi thayo pamisonkhano ndipo makamaka makolo, akupemphedwa kupereka chisamaliro chapadera pamfundo zofunika kwambiri zimenezi kotero kuti misonkhano yathu idzakhale ndi chotulukapo chomangilira ndi mayanjano okoma, ndi kuti isadzaphatikizepo chisoni chifukwa cha kusasamala kochititsa ngozi.
5 Makonzedwe a Zipinda Zogona: Kaŵirikaŵiri abale amapanga makonzedwe awoawo okakhala ndi achibale kapena mabwenzi m’mizinda yamsonkhano. M’malo akumidzi, abale amamanga timisasa kapena amagona m’misasa yaikulu yomangidwa ndi antchito odzipereka modzifunira amsonkhano. Misonkhano ingapo imagwiritsira ntchito zipinda zogona za pasukulu kotero kuti apezere malo onse ofika pamsonkhano. Pamene nthumwi zipatsidwa malo ndi abale kapena achibale, sikoyenera kwa nthumwizo kudyerera pa kuchereza kwa abale athu mwa kuyembekezera kusungidwabe kwa masiku owonjezereka kotero kuti akhale ndi tchuthi pambuyo pamsonkhano. Zipinda zimenezi zili kaamba ka nyengo yamsonkhano yokha. Awo amene apatsidwa malo oterowo ayenera kuona kuti iwo limodzi ndi ana awo akuchita mwaulemu kulinga ku nyumbayo ndi owachereza awo ndipo sayenera kuwononga kalikonse kapena kugwiritsira ntchito paokha zinthu kapena kuloŵa m’malo amtseri a nyumbayo. Ngati eninyumba akhala ndi mavuto alionse m’zimenezi, mwamsanga ayenera kuuza Dipatimenti ya Zipinda pamsonkhanopo, ndipo abale kumeneko adzakhala okondwa kuthandiza.
6 Zosoŵa Zapadera: Makonzedwe ameneŵa ali kaamba ka ofalitsa achitsanzo chabwino okha, kuphatikizapo ana awo odzisungira bwino, amene avomerezedwa ndi Komiti Yautumiki Yampingo. Makonzedwe akusamalira anthu okhala ndi zosoŵa zapadera ayenera kupangidwa ndi mpingo umene amapitako mmalo mwa kuika thayo limeneli pa makonzedwe amsonkhano. Akulu ndi ena omwe amadziŵa za mikhalidwe ya munthu akhoza kupereka thandizo mwachikondi. Zimenezi kaŵirikaŵiri zimafuna kuti ofalitsa alingalire zosoŵa za awo amene ali muutumiki wanthaŵi yonse, okalamba, opunduka, ndipo mwinamwake enanso. Ofalitsa angapereke chithandizo mwa kutenga oterowo kupita nawo limodzi kapena kusamalira zosoŵa zawo mwa njira zina.—Yak. 2:15-17; 1 Yohane 3:17, 18.
7 Awo okhala ndi zosoŵa zapadera SAYENERA kupita kumsonkhano ndi kukapempha chipinda pamene afika, chifukwa chakuti Dipatimenti ya Zipinda iyenera kukhala ndi chidziŵitso cha Komiti Yautumiki Yampingo.
8 Nthumwi Zopezekapo Zochokera Kunja kwa Dera Logaŵiridwa: Pafupifupi nthaŵi zonse, malo kumene mwagaŵiridwa kukasonkhanako amakhala apafupi kwambiri ndi mpingo wanu. Kulinganiza malo okhala okwanira, mabuku, chakudya, zipinda zogona, ndi zina zotero zimazikidwa palingaliro lakuti ochuluka a ofalitsa adzapezeka pamsonkhano umene mpingo wawo wagaŵiridwa. Komabe, ngati pazifukwa zabwino mudzapita kumsonkhano wina wosakhala wa mpingo wanu ndipo mudzafunikira malo ogona, mlembi wampingo akhoza kukupatsani Fomu ya Chipinda Chogona, imene mudzayenera kudzaza ndi kusainitsa ndiyeno kuitumiza kumalikulu amsonkhano umene mudzapezekako.
9 Kugwirizanika Kwanu Kuli Kofunikira: Kuyenda mwatawatawa ndi chipambano cha makonzedwe a zipinda zogona ndi utumiki wa chakudya zimadalira pa kugwirizanika kwa munthu aliyense woloŵetsedwamo. (Yerekezerani ndi Ahebri 13:17.) Sosaite imayamikira kwambiri chichirikizo chabwino chimene abalenu ndi alongo mwachipereka pa makonzedwe autumiki wa chakudya pamisonkhano yachigawo kwa zaka zambiri zapitazo. Zimenezi zatikhozetsa kuchita lendi masitediyamu abwino m’mizinda ndi kusamalira zolipiriridwa za msonkhano. Zakukhozetsaninso kukhalabe pamalo amsonkhano pakupuma kwa masana ndi kukhalaponso pamthaŵi yake ndi kutsitsimulidwa, ndi programu yauzimu yofunika kwambiri.
10 Mwa kukhala oloŵetsedwamo m’misonkhano ya anthu a Yehova, timalimbitsidwa kuchita chifuniro cha Yehova ndipo timatetezeredwa ku zisonkhezero zadziko zakunjaku zimene zingadodometse chikhulupiriro chathu Chachikristu. Tonsefe tiyenera kukhala oyamikira kuti Yehova wapereka nyengo zimenezi za chitsitsimulo chauzimu kwa anthu ake odzipatulira m’nthaŵi ino yamapeto.
[Chidziŵitso ku Bungwe la Akulu: Mlembi wampingo ayenera kusamalira nkhani zokhudza msonkhano wachigawo ndi zilengezo pa Misonkhano Yautumiki ilinkudza. Akulu onse ayenera kugwirizana mokwanira kuti pakhale kusamaliridwa kwamsanga, kosangalatsa, ndi kogwira mtima kwa nkhani zokhudza msonkhano wachigawo.]