Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa 2004 Wakuti “Yendani ndi Mulungu”
1 Kodi n’chiyani chimapangitsa misonkhano yathu yachigawo imene imachitika chaka chilichonse kukhala yapadera kwambiri kwa inu? Kodi ndi nkhani zolimbikitsa ndiponso seŵero zimene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amatikonzera? (Mat. 24:45-47) Kodi ndi mabuku atsopano a chakudya chauzimu chapanthaŵi yake? Kodi ndi zokumana nazo za abale ndi alongo zosonyeza mmene Baibulo linasinthira moyo wawo kukhala wabwino? Kodi ndi malipoti a mmene ntchito yolalikira Ufumu ikupitira patsogolo m’mayiko ena? Kodi ndi kucheza ndi okhulupirira anzathu a misinkhu yonse? Inde, timayembekezera mwachidwi misonkhano yathu chifukwa cha zinthu zimenezi komanso zina zambiri.
2 Dzapezekenipo Masiku Onse Atatu: Yehova kudzera mwa Mose, analamula kuti: “Sonkhanitsani anthu . . . kuti amve, ndi kuti aphunzire.” (Deut. 31:12) Pogwiritsa ntchito kagulu ka kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, Yehova wakonza pulogalamu yapadera yotiphunzitsa tsiku lililonse la msonkhano wathu wachigawo. Popeza akutiphunzitsa kuti ‘tipindule,’ tikufuna kudzapezekapo pamene akupereka malangizo ake onse. (Yes. 48:17) Ngati mukufuna kupempha abwana anu tchuti, yambani mwapemphera kwa Yehova ndiyeno kapempheni, potsatira chitsanzo cha kulimba mtima cha Nehemiya. (Neh. 1:11; 2:4) Ndiponso, chingakhale chikondi kuwauza mofulumira achibale anu amene si Mboni zimene mukukonza zokhudza msonkhano wachigawo.
3 Malo Ogona: Nthaŵi zambiri abale amakonza okha zokakhala ndi achibale kapena mabwenzi awo m’mizinda yomwe mukuchitikira msonkhano. M’midzi, abale amamanga misasa kapena amagona m’midadada yomwe antchito odzifunira pamsonkhanopo amanga. Pamisonkhano ina, ena amagona m’nyumba zogona ana asukulu. Ngati mukugona kwa abale kapena achibale, si bwino kupezerapo mwayi pa kuchereza kwa abale athu ndi kukhalabe komweko masiku ena n’cholinga choti muthere komweko tchuti msonkhanowo utatha. Malo ogona amenewo ndi anthaŵi ya msonkhano yokha basi. Amene apatsidwa malowo azionetsetsa kuti iwo pamodzi ndi ana awo akuchita ulemu panyumbapo ndi kuti sakuwononga chilichonse kapena kugwiragwira zinthu kapena kuloŵa malo osayenera iwo kuloŵamo. Ngati pali zina zimene eninyumba zikuwavuta pankhaniyi, aziuza msanga Dipatimenti Yoona za Malo Ogona pamsonkhanopo, ndipo abale kumeneko adzawathandiza.
4 Kuthandiza Anthu Ofunika Thandizo Lapadera: Mtumwi Paulo anakumbutsa mipingo ya ku Galatiya ‘kuchitira onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.’ (Agal. 6:10) Abale ndi alongo okalamba, odwaladwala, makolo opanda mnzawo wa muukwati, kapena amene ali mu utumiki wanthaŵi zonse sangakupempheni thandizo, koma angakhale ndi zovuta zina zofunika kuzithetsa kuti adzapezeke pamsonkhano wachigawo. Kodi mungathe ‘kuwachitira chokoma’ ndi kuwathandiza? Achibale awo achikristu ndiponso akulu ndiye makamaka ayenera kudziŵa mmene zinthu zilili kwa anthu ameneŵa.
5 Pamsonkhano wa anthu a Yehova zaka pafupifupi 2,500 zapitazo, Ezara ndi Alevi anzake anaŵerenga Mawu a Mulungu ndi kufotokozera anthu amene anasonkhanawo. Kodi chotsatira chinali chiyani? Nehemiya 8:12 amatiuza kuti ‘anapita anthu onse . . . akusekerera kwakukulu; popeza anazindikira mawu amene adawafotokozera.’ Kodi sitisangalala kuti kagulu ka kapolo ka odzozedwa, monga Ezara ndi Alevi, kamagwiritsa ntchito Mawu a Mulungu, kuwafotokoza, ndi kutisonyeza mmene tingawagwiritsire ntchito pamoyo wathu? Pochita zimenezi, kapoloyu amasonyeza chikondi chenicheni cha Yehova ndi kutinso amaderadi nkhaŵa anthu a Yehova. Chikhaletu cholinga chanu kusaphonya tsiku lililonse la Msonkhano Wachigawo wakuti “Yendani ndi Mulungu”!
[Bokosi patsamba 3]
Nthaŵi za Pulogalamu
Lachisanu ndi Loŵeruka
8:30 a.m. – 4:00 p.m.
Lamlungu
8:30 a.m. – 3:05 p.m.