Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa 2000 Wakuti: “Akuchita Mawu a Mulungu”
1 “Ndidzakuyamikani mu msonkhano waukulu: M’chikhamu cha anthu ndidzakulemekezani.” (Sal. 35:18) Tangolingalirani chisangalalo chimene Davide akanakhala nacho lerolino kuona anthu zikwi zambiri akusonkhana pamodzi mwamtendere kudzalandira malangizo a Mulungu pamisonkhano yathu ya m’chilimwe! Kodi muli pakati pa 123,242 amene anapezeka pa umodzi wa Misonkhano Yachigawo ya “Mawu Aulosi a Mulungu? Kuyambira August mpaka kumayambiriro a September 1999, m’Malaŵi muno munachitika misonkhano 15. Misonkhano yathu yachigawo ya 2000 idzatipatsa mipata yatsopano yosonkhana pamodzi ndi otamanda Yehova anzathu amene “amazindikira kusoŵa kwawo kwauzimu” ndi amene amasangalala ndi kukhala achidwi chakuti “amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo.”—Mat. 5:3, NW; Chiv. 2:29.
2 Kusamalira Amene Ali ndi Zosoŵa Zapadera: Achibale, akulu ndi ena mumpingo omwe akudziŵa za mkhalidwe wapadera wa okalamba, athanzi lofooka, atumiki anthaŵi zonse, kapena ena amene ali ndi zosoŵa zapadera angasonyeze kuwadera nkhawa kwawo kwachikondi ndi chisamaliro mwa kuwathandiza kuti akapezeke pamsonkhano.—Yerekezani ndi 1 Timoteo 5:4.
3 Konzani Zokapezekapo Masiku Onse Atatu: Kodi Satana akukudodometsani kuti munyalanyaze zinthu zauzimu? Zachisoni kuti abale ndi alongo athu ambiri ndiponso mabanja awo akumanidwa chakudya chofunika chauzimu. Motani? Mwa kuphonya mapulogalamu a msonkhano wachigawo a Lachisanu. Nthaŵi zina kwapezeka kuti chiŵerengero chachikulu zedi cha abale athu amamanidwa malangizo auzimu ndi mayanjano amene amakhalapo Lachisanu.
4 N’zotheka kuti abale ena amachedwa kupita kwa abwana awo kukapempha tchuthi kuti adzapezeke pamsonkhano. Kodi umenewu ndiwo mkhalidwe wanu? Bwanji osapemphera kwa Yehova za nkhaniyo ndiyeno n’kulimba mtima kumufotokozera bwana wanu za mkhalidwe wanuwo? Kumbukirani zotsatira zabwino za Nehemiya, amene anali mu mkhalidwe wofananawo. (Neh. 2:1-6) Khulupirirani kuti Atate wathu wa kumwamba ndi wofunitsitsa kukuthandizani, podziŵa kuti ngati muika zinthu za Ufumu patsogolo, adzakupatsani zinthu zofunika pamoyo.—Mat. 6:32b, 33.
5 Kodi Misonkhano Yathu Imakukhudzani Motani? Mlongo wina wa kum’maŵa kwa United States analemba kuti: “Zikomo kwambiri chifukwa cha msonkhano wachigawo wa 1999. Kucheza ndi abale amene ndimaŵaona kamodzi pachaka kumandipatsa chimwemwe kwambiri. Ndinadziŵa choonadi ndili mtsikana nthaŵi imene ndinali woyembekezera, ndipo ndikukumbukirabe ndi chimwemwe chonse nthaŵi imene wondichititsa phunziro la Baibulo wanga anapita nane kumsonkhano kwanthaŵi yoyamba. Ndinalira n’tayang’ana namtindi wa anthu amene anali m’mwamba mwa sitediyamu yopanda denga imeneyi pamene tinkaimba nyimbo ya Ufumu yakuti, ‘Unyinji wa Abale.’ ‘Pakati pa anthu okongola onseŵa,’ ndinadzifunsa kuti, ‘Yehova angafunenso ine bwanji?’ Tsiku limenelo ndinaganiza zotumikira Yehova mokwanira.” Si kusangalatsa kwake! Ndithudi ndi chinthu chosangalatsa kukhala pamodzi ndi anthu oyera a Yehova, kodi sichoncho?
6 Kumapeto kwenikweni m’masiku otsiriza ano, tikufunikira kwambiri msonkhano wachigawo wapachaka kuposa kale lonse. Ndi makonzedwe ochokera kwa Yehova kuti tikhalebe ndi thanzi lauzimu komanso maganizo abwino. Chotero, tsimikizani mtima kudzapezekapo masiku onse atatu a Msonkhano Wachigawo wachaka chino wakuti “Akuchita Mawu a Mulungu”. Kodi mungakwaniritse motani zimene mwasankha kuchita? Pemphani abwana anu nthaŵi ilipo kuti adzakupatseni tchuthi kuti mudzapezeke pamsonkhano wonse. Ngati kupeza kwanu kuli kovutirapo, yambani lero kusunga ndalama zofunika kuti mudzapezekepo. Pemphani Yehova kuti akuthandizeni kugonjetsa zopinga zilizonse. Mukatero, mungayembekezere kukasangalala ndi mayanjano abwino a abale ndi alongo anu ndiponso kukamva mawu a moyo wosatha ochokera kwa Atate wathu wakumwamba wachikondi, Yehova.—Yerekezani ndi Yohane 6:68.
[Bokosi patsamba 6]
Nthaŵi ya Mapulogalamu
Lachisanu ndi Loŵeruka
8.30 a.m. – 5:00 p.m.
Lamlungu
8:30 a.m. – 4:00 p.m.