Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa 1998 Wakuti “Njira ya Moyo ya Mulungu”
1 Chaka ndi chaka olambira Yehova amakono amayembekezera mwachidwi kukumana muunyinji wawo pamisonkhano yachigawo. Pomatero, amasonyeza mzimu wa atumiki okhulupirika a Yehova ku Israyeli wakale omwe ankaimba mosangalala mawu a Salmo 122 ali m’njira pomka ku Yerusalemu kolambira Yehova. Vesi loyamba la Salmo limenelo limati: “Ndinakondwera mmene ananena nane, Tiyeni kunyumba ya Yehova.” Pa zochitika zoterozo mpamenenso timaona kuti umboni waukulu wakuti mawu ouziridwa a Yesaya 2:2, 3 akukwaniritsidwa.
2 Chaka chino tili ndi chifukwa chapadera chosangalalira chifukwa mwa nthumwi zina zochokera m’maiko ambiri padzakhalanso nthumwi zochokera m’mitundu yonse zomwe zidzapezeka pamisonkhano ina yaikulu. Amishonale obwerera kukaona achibale ndi mabwenzi awo adzapezeka pamisonkhano yambiri. Choncho, kulikonse paprogramu yamsonkhanowo padzakhala zokumana nazo zochokera m’munda ndi malipoti a mmene ntchito yolalikira Ufumu ikuyendera m’maiko ena. Pamisonkhano yachigawoyo zidzaonekeratu m’nkhani zina kuti pali nthumwi zamitundu yonse, chifukwanso cha amishonale omwe adzapezekapo.
3 Mmene tikupitiriza kukonzekera Msonkhano Wachigawo wa 1998 wakuti “Njira ya Moyo ya Mulungu,” tingakonde kufotokoza malangizo ena amene mufunikira kudziŵa kuti mudzapeze malo ogona pamsonkhanopo. Mukagwirizina nafe kwambiri mukhala mukusonyeza kuti mukuyamikira zonse zimene takukonzerani.
4 Zipinda: Nthaŵi zambiri abale amangokonzekera okha zokakhala ndi achibale ndi mabwenzi awo m’mizinda yamsonkhano. Kumidzi, abale amamanga misasa kapena amagona m’misasa yogonamo anthu ambiri yomwe antchito odzifunira amakonza. Pamisonkhano ingapo, osonkhana amawapezera malo ogona m’madomitale a pasukulu. Ngati mukugona kwa abale kapena achibale, si bwino kupezerera ukoma wa abale athu nkumangokhalabe komweko masiku ambiri kuti muthere konko tchuti msonkhanowo utatha. Zipinda zimenezo nzanthaŵi yamsonkhano basi. Amene apatsidwa malo choncho aziona kuti iwowo ndi ana awo akuchita mwaulemu panyumbapo ndi kuti sakuwononga chilichonse kapena kugwiragwira zinthu kapena kuloŵa malo osayenera kuloŵamo. Ngati eni nyumba akuona kuti zina ndi zina zikuwavuta pa nkhani imeneyi, ayenera kukauza Dipatimenti Yazipinda pamsonkhanopo, ndipo abale kumeneko angathandize.
5 Mverani Malangizo a Sosaite: Mfundo imeneyi ikhale imodzi mwa zimene tiyenera kusamala kwambiri. Ahebri 13:17 amati: “Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuŵerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu.” Timapemphedwa kusamala mfundo imeneyi kaŵiri kapena katatu pachaka basi. Ngakhale ngati ifeyo tikanasankha zosiyana, koma chitsanzo chathu chabwino chimene abale athu akuona, chimakulitsa mzimu wa chikondi, wa umodzi, ndi wochirikiza.—Onani 1 Akorinto 16:16; Afilipi 2:1-4.
6 Zosoŵa Zapadera: Achikulire, ofooka, ndi omwe ali mu utumiki wanthaŵi zonse, kapena enanso angafune kuthandizidwa kukapezeka pamsonkhano. Achibale, akulu, ndi ena mumpingo amene amadziŵa kuti ena ali ndi vuto loti amafunikira kusamalidwa mwapadera, ndiwo angakonze mwachikondi njira zoyenera, chifukwa udindo umenewo ngwa banja ndi mpingo, osati wa okonza msonkhano. (Yerekezerani ndi 1 Timoteo 4:4.) Iwowo awathandiza kale mwa njira zina, monga kuwathandiza kukonza njira zothangatira anthu ofuna chisamaliro chapadera kapena kuwathandiza ndi ndalama, ngati nkotheka ndipo ngati nkofunika.—Yak. 2:15-17.
7 Kwa amene sangasamalidwe mwa njira imeneyi, fomu ya Sosaite ya Special Needs Room Request imalongosola ziyeneretso za amene akufunikira fomu imeneyo. Ofalitsa a khalidwe labwino okha ndiwo adzapindula ndi makonzedwe ameneŵa, kuphatikizapo omwe ali ndi ana omvera, omwe Komiti Yautumiki Yampingo yavomereza. Koma musanadzaze fomu ya Special Needs Room Request, muŵerenge mosamala mawu ali mmunsi mwa fomuyo. Mafomu ameneŵa ayenera kutumizidwa mwamsanga ku Dipatimenti ya Zipinda. Chonde gwiritsirani ntchito keyala ya msonkhano yomwe ili kumbuyo kwa fomu ya Special Needs.
8 Odzasonkhana Ochokera Kwina: Pafupifupi nthaŵi zonse, msonkhano umene mumagaŵiridwa kukapezekapo ndiwo wapafupi ndi mpingo wanu. Malo okhala okwanira, mabuku, zipinda zogona, ndi zina zotero, zimakonzedwa moyerekezera ndi unyinji wa ofalitsa amene adzakhala pamsonkhano womwe mpingo wawo unagaŵiridwa kukapezekapo. Komabe, ngati muli ndi chifukwa chabwino chokapezekera pamsonkhano wina osati umene munagaŵiridwa kukapezekapo, moti mukafuna malo ogona, mlembi wampingo angaode ku Sosaite fomu ya Room Request, yomwe inu mudzayenera kudzaza ndipo isainidwe. Ndiyeno muitumize kulikulu lamsonkhano womwe mudzapezekako.
9 Mawu Omaliza: Zimene antchito a m’hotela amanena zimasonyeza kuti abalenu ndi alongo mumachita zoyamikirika chifukwa mumasonyeza mikhalidwe yaumulungu. Amanija a hotela ina anati Mboni za Yehova ndiwo “anthu okoma ndi akhalidwe labwino kwenikweni amene timachereza.” Wina anati: “Ndinaganiza zoti ndinene kuti zikomo m’malo mwa antchito onse a pahotelayi. Tikuzitamanda nthumwi zanu chifukwa ndizo ena mwa anthu abwino kwambiri, ogwirizana, ndi aulemu omwe tinakondwera powatumikira. Amasonyezadi ubwino wa gulu lanu ndi kuti limalemekeza anthu moona mtima. Tikuyembekezera kuzakucherezaninso.” Mlongo wina pofunsira chipinda chogona pamsonkhano wa chaka chatha, kalaliki wopereka zipinda anamuuza kuti: “Ndimadziŵiratu kuti yemwe waimba foniyu ndi mmodzi wa Mboni za Yehova. Nthaŵi zonse mumakhala odekha, aulemu, ndi olankhula momasuka. Ine wa baptist nthaŵi zonse ndimachita nanu chidwi, ndipo nonsenu ndikukutamandani.” Mawu ngati amenewo ngosangalatsa kuwamva, si choncho? Khalidwe la abale ndi alongo limene linapangitsa anthu kunena mawu amenewo ndithudi limakondweretsa mtima wa Yehova.
10 Sosaite imalandira makalata ambiri kwa abale ndi alongo osonyeza kuyamikira kwawo zimene inawakonzera. Banja lina la ku Illinois linati: “Tikungofuna mudziŵe kuti msonkhano wachigawo umene uja tinauyamikira kwambiri. Tikuzindikira kuti suunangochitika mwamwaŵi iyayi, koma kuti abale ambiri anagwira ntchito mwa kalikiliki. Talemba kuti tikuyamikireni.” Mlongo wina wa ku Michigan analemba kuti: “Ndikuthokoza ndi mtima wonse abale anga onse omwe anakonzeratu zipinda zogona. Ine ndi mwamuna wanga tikuyamikira kuti tinalipira mitengo yotsika, poonanso kuti mwamuna wanga ndiye yekha akugwira ntchito kuti ineyo ndizichitabe upainiya. Makonzedwe ameneŵa amatithandiza kupindula kwambiri ndi msonkhano.”
11 Nzachionekere kwa tonsefe kuti Yehova akuchirikiza makonzedwe a misonkhano ya chaka ndi chaka. Popeza kuti abale ambiri amene amachita kuyendera misonkhano yachigawo amafuna zipinda, tikudalira kuti Yehova adzagaŵira zofunika zimenezinso. Tikamasonyeza kuti ndife okhulupirika “m’chaching’onong’ono” tidzalandira madalitso aakulu omwe akuyembekeza anthu amene Yehova amakonda.—Luka 16:10.
[Bokosi patsamba 3]
Nthaŵi za Programu
Lachisanu ndi Loŵeruka
8:45 a.m. – 4:50 p.m.
Lamlungu
8:45 a.m. – 4:50 p.m.