Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa 2001 Wakuti “Aphunzitsi a Mawu a Mulungu”
1 Mneneri Yesaya anatchula Yehova kuti Mlangizi Wamkulu, amene monga atate amalangiza anthu ake kuti: “Njira ndi iyi, yendani inu m’menemo.” (Yes. 30:20, 21) Koma kodi mawu amene Yehova walankhula kuti tipindule nawo timawamva motani? Yehova amalankhula kwa anthu ake kudzera m’Baibulo komanso m’mabuku ofotokoza Baibulo, misonkhano ya pampingo, misonkhano yadera, ndi misonkhano yachigawo yokonzedwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45) Tiyenera kuthokoza Yehova kuti akupitirizabe kutitsogolera njira yoti tiyendemo.
2 Chaka chilichonse, msonkhano wachigawo umatipatsa mpata wosonkhana ndi okhulupirira anzathu komanso womvetsera mwatcheru malangizo a Yehova. Chaka chatha, anthu 134,562 anapezeka pa misonkhano yotsitsimula mwauzimu yamutu wakuti “Akuchita Mawu a Mulungu.” Mu 2001, m’Malaŵi muno mudzachitika Misonkhano Yachigawo yamasiku atatu yamutu wakuti “Aphunzitsi a Mawu a Mulungu.” Tikudziŵa kuti mukufunitsitsa kukonzekera kuti mudzapezekepo, choncho tikupereka malangizo ali m’munsiŵa pankhani ya malo ogona.
3 Malo Ogona: Nthaŵi zambiri abale amakonza okha zokakhala ndi achibale kapena mabwenzi awo m’mizinda yomwe mukuchitikira msonkhano. M’midzi, abale amamanga misasa kapena amagona m’midadada yomwe antchito odzifunira amamanga pamsonkhano. Pamisonkhano ina, ena amagona m’makalasi a ana asukulu. Ngati mukugona kwa abale kapena achibale, si bwino kupezerapo mwayi pa kuchereza kwa abale athu n’kumangokhalabe komweko masiku ambiri kuti muthere konko tchuthi msonkhanowo utatha. Zipinda zimenezo ndi zanthaŵi ya msonkhano yokha basi. Choncho amene apatsidwa malo ayenera kuona kuti iwo pamodzi ndi ana awo akuchita ulemu panyumbapo ndi kuti sakuwononga chilichonse kapena kugwiragwira zinthu kapena kuloŵa malo osayenera iwo kuloŵamo. Ngati eninyumba zina zikuwavuta pankhani imeneyi, akauze msanga Dipatimenti ya Zipinda pamsonkhanopo, ndipo abale kumeneko adzawathandiza.
4 Kusamalira Anthu Amene Ali ndi Zosoŵa Zapadera: Okalamba, odwala, ndi omwe ali mu utumiki wanthaŵi zonse, kapena enanso angafunike kuwathandiza kuti akapezeke pamsonkhano. Achibale, akulu, ndi ena mumpingo amene akudziŵa kuti ena ali ndi vuto lofunika kusamalidwa mwapadera, ndiwo angasamalire anthu ameneŵa mwachikondi. Tisapatse oyendetsa msonkhano udindo umene uli wa banja ndi mpingo.—1 Tim. 5:4.
5 Mawu Omaliza: Pamene nthaŵi yopita ku msonkhano wachigawo ikuyandikira, m’pempheni Yehova kuti mudzakhalepo pa zigawo zonse masiku onse atatu ndikuti mudzapindule kwambiri ndi pulogalamuyi. Kodi mwapempha kale kuntchito kuti adzakupatseni tchuthi masiku atatu a msonkhano umene mukufuna kudzapita? Ngati simunatero, chitani zimenezo mwamsanga. Nthaŵi zambiri kupempha tchuthi nthaŵi itatha kale saloleza. Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru wakonza Msonkhano Wachigawo wachaka chino wamutu wakuti “Aphunzitsi a Mawu a Mulungu” kuti utilangize mwauzimu ndi kulimbitsa chikhulupiriro chathu. Chotero yambani kukonzekera pakalipano kuti mudzapezekepo, motsatira langizo la wamasalmo lakuti: “Lemekezani Mulungu m’masonkhano”!—Sal. 68:26.
[Bokosi patsamba 8]
Nthaŵi ya Mapulogalamu
Lachisanu ndi Loŵeruka
8:30 a.m. – 5:00 p.m.
Lamlungu
8:30 a.m. – 4:00 p.m.