Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa 2003 Wakuti “Patsani Mulungu Ulemerero”
1 Yehova mwa mneneri wake wokhulupirika Yesaya, analamula kuti: “Mverani Ine, inu anthu anga, ndi kunditcherera makutu, iwe, mtundu wa anthu anga.” (Yes. 51:4) Kodi nthaŵi yotsiriza ino imene mavuto akuipiraipirabe, tingakane kuti kumvera malamulo a Yehova n’kofunika kwambiri kuposa kale lonse? Kutsatira lamulo lake losonkhana pamodzi polambira ndi njira imodzi imene ‘timatchera makutu’ kwa Yehova. Tikudikira mwachidwi mpata wapadera umene timakhala nawo pamsonkhano wachigawo umene umachitika kamodzi pachaka. Mu chaka cha 2003 Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova lakonzanso misonkhano yachigawo yambiri yoti idzachitike m’gawo lino la nthambi ya Malaŵi.
2 Monga ananenera mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 2002, misonkhano ya mayiko idzachitikiranso m’mizinda imene aisankha, ndipo padzakhala nthumwi za m’mayiko apadziko lonse. Popeza misonkhano ya mayiko idzachitikira m’mizinda yochepa, kudzapita mipingo yokha imene yauzidwa kuti ikapezeke kumeneko. Koma misonkhano yonse yachigawo idzakhala ngati misonkhano ya mayiko chifukwa chakuti, pamisonkhano yachigawo yambiri, padzakhala amishonale, ndipo tidzakhala ndi mwayi womva zina mwa zimene akumana nazo. Kodi tingatani kuti tikapindule kwambiri ndi zimene akukonza pamisonkhano yathu yachigawo imene ikubwerayi?
3 Dzapezekenipo Tsiku Lililonse: Tiyenera kukapezeka pamsonkhano wonse, kuti tikapindule ndi malangizo operekedwa kudzera mwa gulu la “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45) Kodi mufunika kupempha bwana anu masiku a tchuthi kuti tsiku lililonse la msonkhano mudzakhalepo? Nehemiya asanakapemphe Mfumu Aritasasta chilolezo chakuti apite ku Yerusalemu kukamanga linga, ‘anapemphera kwa Mulungu wa Kumwamba.’ (Neh. 2:4) Muyeneranso kupemphera kwa Yehova kuti akulimbitseni mtima kuti mukapemphe bwana anu tchuthi kuti mudzakhale nawo pamsonkhanowu masiku onse atatu. Bwanji ngati bwana anu akukana kukupatsani tchuthi? Mwina zimene zingathandize kuti akukomereni mtima ndi kuwafotokozera kuti malangizo amene timalandira pamisonkhano yathu yachigawo amatithandiza kukhala oona mtima, olimbikira ntchito, ndiponso okhulupirika pantchito. Komanso, ngati m’banja lathu muli anthu ena achipembedzo china, ndi bwino kuwauza mofulumira zimene takonza zokhudzana ndi msonkhano.
4 Kuthandiza Anthu Ofunika Thandizo Lapadera: Kodi mu mpingo wanu muli ena amene angafunike kuwathandiza kuti adzapezeke pamsonkhano wachigawo? Kwenikweni amene amapereka thandizo lapadera kwa anthu okalamba, odwaladwala, kapena kwa amene ali mu utumiki wa nthaŵi zonse ndi achibale awo achikristu. Koma akulu ndi anthu ena amene akudziŵa moyo wa anthu ameneŵa angawathandizenso chifukwa chowakonda.
5 Ndife Choonetsedwa: Kodi anthu amaona kusiyana kwa Mboni za Yehova ndi anthu a dziko? Inde amaona. Onani zina zimene oyang’anira pa hotela ina mu mzinda wina ananena: “Nthaŵi zonse timakhala ndi anthu odzachita misonkhano, koma inu ndi anthu ogwirizanika kwambiri ndiponso okoma mtima.” “Mlungu watha tinali ndi gulu lina la chipembedzo pompano. Munthu sangafunse kuti mukusiyana nawo pati anthu amenewo.” “Timadziŵa kuti ndinu anthu othandiza ndiponso ogwirizanika.” Kodi ndemanga zimenezi sizikutipangitsa kuona momwe “nzeru yochokera kumwamba” imathandizira pa makhalidwe athu? (Yak. 3:17) Chifukwa chakuti ndife “choonetsedwa ku dziko lapansi,” nthaŵi zonse khalidwe lathu lizisonyeza ulemu ndi ulemerero wa Mulungu wathu, Yehova.—1 Akor. 4:9.
6 Popeza “maonekedwe a dziko ili apita [“akusintha,” NW],” tikufunika misonkhano yathu yachigawo kuti itithandize kuika mtima pa zinthu zauzimu. (1 Akor. 7:31) Kukonza zodzapezekapo tsiku lililonse n’kofunika khama, koma mpake kuchita zimenezo. Msonkhano Wachigawo wachaka chino wakuti “Patsani Mulungu Ulemerero” wakonzedwa kuti utithandize kukhala olimba pamene tikudikira kuti Yehova aweruze dziko la Satanali. Tisaloletu china chilichonse kutilepheretsa kukalandira malangizo amene Yehova watikonzera.—Yes. 51:4, 5.
[Bokosi patsamba 3]
Nthaŵi ya Pulogalamu
Lachisanu ndi Loŵeruka
8:30 a.m. - 5:00 p.m.
Lamlungu
8:30 a.m. - 4:00 p.m.