Msonkhano Wachigawo wa “Atamandi Achimwemwe” wa 1995 wa Mboni za Yehova
1 Chinali chisangalalo chotani nanga kukhala pakati pa 327,856 amene anafika pa Misonkhano Yachigawo ya “Mantha Aumulungu” m’gawo la nthambi ya Zambia chilimwe chapitachi! Okwanira 1,555 anasonyeza mantha oyenera aumulungu mwa kubatizidwa. Kudzakhala kolimbikitsa chotani nanga kusonkhana chaka chino kaamba ka Misonkhano Yachigawo ya “Atamandi Achimwemwe” ya 1995 ya masiku atatu! Mutu wake wodzutsa chidwiwo uyenera kutisonkhezeradi kupanga kuyesayesa kuli konse kuti tidzafikepo limodzi ndi ophunzira Baibulo athu. Programu yake idzakhaladi magwero enieni a chitsitsimulo chauzimu kwa tonsefe pamene tikupitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika m’nthaŵi ino yamapeto.
2 Tsimikizirani kupanga makonzedwe anu amsonkhano padakali nthaŵi kotero kuti mudzakhalepo kuti mudzasangalale pamasiku onse atatu a programu yokondweretsa yauzimuyo, kuyambira pa nyimbo yotsegulira kufikira pa pemphero lomaliza. M’makonzedwe anu phatikizanimo mwachikondi awo amene angafunikire thandizo, makamaka okondwerera chatsopano, kotero kuti nawonso adzakhale pamagawo onse. Kungakhale kothandiza kukambitsirana chidziŵitso cha mu mphatika ino ndi ophunzira Baibulo athu amene angafune kudzafikapo. (Agal. 6:6, 10) Programu yake idzayamba ndi nyimbo pa 9:20 a.m. patsiku loyamba ndi kumalizidwa cha ku ma 5:00 p.m. Patsiku lachiŵiri programuyo idzayamba pa 9:00 a.m. ndi kumalizidwa ndi nyimbo ndi pemphero cha ku ma 4:30 p.m. Chigawo chammaŵa patsiku lachitatu chidzayamba pa 9:30 a.m., ndipo programu ya tsikulo idzamalizidwa cha ku ma 4:15 p.m. masana. Chidziŵitso chotsatirachi chidzakuthandizani pa kukonzekera kwanu koyambirira.
3 Makonzedwe a Malo Ogona: Kaŵirikaŵiri abale amapanga makonzedwe awo a kukhala ndi achibale kapena mabwenzi awo okhala m’mizinda ya malo amsonkhano. Kumadera akumidzi, abale amamanga misasa kapena amagona m’mipanda yaikulu yomangidwa ndi antchito odzifunira amsonkhano. Misonkhano ingapo imagwiritsira ntchito zipinda za sukulu kukhala malo ogona a ena a awo amene afikapo. Pokhala m’nyumba za abale kapena achibale, sikuli koyenera kuti nthumwi ziyese kulandira alendo kwa abale awo kumeneko kukhala mwaŵi wakuti akhale ndi tchuthi msonkhanowo utatha mwa kuyembekezera kuloledwa kukhalabe kwa masiku owonjezereka. Malo ameneŵa nganyengo ya msonkhano wachigawo chabe. Awo amene adzapatsidwa malo ogona otero limodzi ndi ana awo ayenera kuchita mwaulemu panyumba ya wowalandira wawo ndipo sayenera kuwononga kalikonse kapena kungogwiritsira ntchito zinthu kapena kumaloŵa m’malo amseri a nyumbayo. Ngati eninyumba akupeza vuto lililonse pankhaniyi, ayenera kudziŵitsa zimenezi nthaŵi yomweyo ku Dipatimenti ya Malo Ogona ya pamsonkhano, ndipo abale a kumeneko adzakhala ofunitsitsa kuthandiza.
4 Zosoŵa Zapadera: Makonzedwe ameneŵa ali a ofalitsa achitsanzo chabwino okha, kuphatikizapo ana awo amakhalidwe abwino, amene ali ovomerezedwa ndi Komiti Yautumiki Yampingo. Makonzedwe akusamalira anthu amene ali ndi zosoŵa zapadera ayenera kupangidwa ndi mpingo umene iwowo amasonkhana nawo, osati kupereka thayoli kwa oyendetsa msonkhano. Akulu ndi ena amene akudziŵa za mikhalidwe ya anthu enawo angapereke thandizo mwachikondi. Kaŵirikaŵiri zimenezi zimafuna kuti ofalitsa alingalire za zosoŵa za awo amene ali mu utumiki wanthaŵi yonse, okalamba, odwala, ndipo mwinamwake ndi enanso. Ofalitsa angapereke thandizo mwa kukhala ndi oterowo kapena kusamalira zosoŵa zawo m’njira zina.—Yak. 2:15-17; 1 Yoh. 3:17, 18.
5 Awo amene ali ndi zosoŵa zapadera SAYENERA kupita kumsonkhano ndi kukapempha malo ogona pamene afika chifukwa chakuti Dipatimenti ya Malo Ogona idzayenera kukhala itadziŵitsidwa ndi Komiti Yautumiki Yampingo.
6 Nthumwi Zochokera Kuchigawo China: Kaŵirikaŵiri, malo amene mwagaŵiridwa kukafikapo ndiwo amene ali pafupi ndi mpingo wanu. Makonzedwe a kukhala ndi malo okhala okwanira, mabuku, zipinda zogona, ndi zina zotero, aikidwa pamaziko akuti unyinji wa ofalitsa udzafika pa msonkhano umene mipingo yawo yagaŵiridwa. Komabe, ngati pali chifukwa chabwino cholinganiza kukaloŵa msonkhano umene simunagaŵiridwe ndipo mudzafunikira malo ogona, mlembi wampingo angaode Formu wa Kupempha Cipinda limene muyenera kulemba ndi kulisayina. Ndiyeno litumizeni kumalikulu amsonkhano umene mudzafikako.
7 Kugwirizanika Kwanu Kukufunika: Chipambano cha makonzedwe a malo ogona ameneŵa chikudalira pa kugwirizanika kwa onse amene akuloŵetsedwamo. (Aheb. 13:17) Kayendedwe katawatawa ndi kachipambano ka makonzedwe a malo ogona ndi a chakudya kakudalira pa kugwirizanika kwa aliyense woloŵetsedwamo.
8 Mwa kukhala wophatikizidwa m’misonkhano ya anthu a Yehova, timalimbikitsidwa kuchita chifuniro cha Yehova ndipo timatetezeredwa pa ziyambukiro zakunja za dziko zimene zingafooketse chikhulupiriro chathu Chachikristu. Tonsefe tingakhale othokoza kuti Yehova wagaŵira nyengo zimenezi za kutsitsimulidwa kwauzimu kwa anthu ake odzipatulira m’nthaŵi ino yamapeto.
9 Kutetezera Moto ndi Ngozi Zina: Mosakayikira, chochititsa kubuka kwa moto chachikulu pa misonkhano yaikulu sindicho kuphika chakudya pafupi ndi misasa, koma ana osayang’aniridwa oseŵera ndi moto kapena kuuyang’anira. Motero, kaamba ka chitetezo chanu ndi cha abale anu, musalole ana anu kuyendayenda mosayang’aniridwa; musasiyire ana aang’ono kuyang’anira madzi oŵira, kapena kuti ayang’anire moto wophikira mwa njira iliyonse. Iwo akhoza kuchita zinthu zimenezi bwino lomwe kunyumba, koma pamalo amsonkhano ndi pena ndipo chisamaliro chowonjezereka chiyenera kuperekedwa kupeŵa ngozi. Anthu ambiri amakhalirana pafupi, ndipo ana amakonda kuseŵera maseŵero pamene ali ndi ana ena anzawo. Amacheukitsidwa mosavuta ndipo samaona ngozi, motero kaamba ka zifukwa zimenezi sitiyenera kuwasungitsa makandulo, macheso kapena nyali. Vuto lina limabuka pamene makolo apita kukamvetsera magawo amsonkhano mkati mwa tsiku ndi kusiya ana aang’ono alibe wowayang’anira kumisasa. Ana ayenera kukhala pamodzi ndi makolo awo mkati mwa programu. Pamene akalinde aona ana akuyendayenda pa malo a msonkhano opanda wowayang’anira, iwo ayenera kutengera anawo kwa makolo awo. Makolo! chonde gwirizanani ndi antchito amsonkhano ndipo mwa njira imeneyi sonyezani ‘kukonda abale.’—1 Pet. 2:17.
10 Gulu la Yehova mwachikondi limapereka zikumbutso zapanthaŵi yake zokhudza misonkhano. Nzomvetsa chisoni kunena kuti pa misonkhano ingapo m’zaka zapitazi, ofika pa misonkhano ena anatayikiridwa ndi zinthu zawo ndi moto umene ukanapeŵedwa. Abale amene ali ndi thayo pa misonkhano, ndipo makamaka makolo, akupemphedwa kusamalitsa pa mfundo zofunika zimenezi kotero kuti misonkhano yathu idzakhale ya chiyanjano chomangirira ndi chokondweretsa, ndipo isadzakhale ya kulira ndi chisoni chifukwa cha kusasamala kochititsa ngozi.
Chidziŵitso ku Bungwe la Akulu: Akulu SAYENERA kulinganiza Msonkhano Wautumiki mkati mwa mlungu wamsonkhano. Mlungu umenewu suyenera kukhala ndi msonkhano uliwonse. Mlembi wampingo ayenera kusamalira nkhani zokhudza msonkhano wachigawo ndi zilengezo pa Misonkhano Yautumiki yamtsogolo monga momwe kungathekere, kusiyapo ngati kwasonyezedwa kapena ngati ali wosakhoza kuchita motero.