Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa “Amithenga a Mtendere Waumulungu” wa 1996
1 Mawu oona mtima a chiyamikiro cha programu yotsitsimula mwauzimu anamveka kuchokera kwa ambiri mwa okwanira 77,879 omwe anapezeka pa Misonkhano Yachigawo ya “Atamandi Achimwemwe” ya 1995 m’gawo la nthambi ya Malaŵi. Mitima yathu inasefukira ndi chisangalalo poona atamandi a Yehova okwanira 1,216 akusonyeza kudzipatulira kwawo mwa ubatizo wa m’madzi. Tinasangalala kulandira zofalitsa ziŵiri zatsopano, Mboni za Yehova ndi Maphunziro ndi Knowledge That Leads to Everlasting Life. Kusangalala kwathu ndi programu yotsitsimula yoteroyo chaka chatha kuyenera kutisonkhezeradi kupanga kuyesayesa kulikonse kuti tidzapezeke paprogramu imene ikulinganizidwa ya Misonkhano Yachigawo ya “Amithenga a Mtendere Waumulungu” ya 1996. Ndithudi, tonsefe tiyenera kuitanira maphunziro athu a Baibulo ndi kuwathandiza kuti adzakhalepo limodzi nafe. Misonkhano imeneyi idzakhala magwero enieni a chilimbikitso ndi nyonga pamene tikupitiriza kutumikira Yehova mwachimwemwe m’masiku ano otsiriza.
2 Khalani wotsimikiza kupanga makonzedwe anu a msonkhano pasadakhale kuti mudzakhalepo ndi kusangalala ndi masiku onse atatu a programu yauzimu yokondweretsa, kuyambira panyimbo yotsegulira mpaka pemphero lomaliza. Mwachikondi, phatikizani m’makonzedwe anu aja ofunikira chithandizo, makamaka okondwerera chatsopano, kuti nawonso adzakhalepo pachigawo chilichonse. Kudzakhala kothandiza kwambiri kukambitsirana chidziŵitso cha m’mphatika ino pamodzi ndi ophunzira nawo Baibulo alionse amene angakonzekere kudzakhalapo. (Agal. 6:6, 10) Programu idzayamba ndi nyimbo zamalimba pa 9:30 a.m. pa Lachisanu ndi kutha pafupifupi 4:30 p.m. Programu ya pa Loŵeruka idzayamba ndi 9:30 a.m. ndi kutha ndi nyimbo ndi pemphero pafupifupi 4:30 p.m. Chigawo chammaŵa pa Sande chidzayamba ndi 9:30 a.m., ndipo programu ya tsikulo idzatha pafupifupi 4:00 p.m. masana. Chidziŵitso chotsatirachi chidzakuthandizani pa kukonzekera kwanu koyambirira.
3 Makonzedwe a Malo Ogona: Nthaŵi zambiri abale amapanga makonzedwe awoawo a kukhala ndi achibale kapena mabwenzi m’mizinda ya misonkhano yachigawo. Kumidzi, abale amamanga misasa kapena amagona m’mipanda yaikulu yomangidwa ndi antchito odzifunira a msonkhano wachigawo. Pamisonkhano yachigawo yoŵerengeka amagwiritsira ntchito zipinda za sukulu monga malo ogona ena opezekapo. Pamene tikukhala panyumba za abale kapena za achibale, sikoyenera kwa ife nthumwi kudyerera kuchereza kwa abale athu mwa kuganiza kuti adzatisunga masiku enanso pambuyo pa msonkhano wachigawo kuti tithe tchuthi chathu. Zipindazo ndi za nyengo ya msonkhano wachigawo chabe. Aja opatsidwa malo ogona ayenera kutsimikizira kuti iwo ndi ana awo akulemekeza nyumba ya wocherezayo ndi kuti sakuwononga zinthu kapena kusanthulasanthula katundu kapena kuloŵa m’zipinda zimene sayenera kuloŵamo. Ngati eni nyumba apeza vuto lililonse pankhaniyi, ayenera mwamsanga kudziŵitsa Dipatimenti ya Zipinda pamsonkhanopo, ndipo abale kumeneko adzakondwa kuthandiza.
4 Zosoŵa Zapadera: Makonzedwe ameneŵa ali kokha a ofalitsa achitsanzo chabwino, kuphatikizapo ana awo odzisunga, amene avomerezedwa ndi Komiti Yautumiki Yampingo. Makonzedwe a kusamalira anthu okhala ndi zosoŵa zapadera ayenera kupangidwa ndi mpingo umene amasonkhanako, osati kusamutsira thayo limeneli ku makonzedwe a msonkhano wachigawo. Akulu ndi ena amene akudziŵa za mikhalidwe ya munthuyo akhoza kuthandiza mwachikondi. Nthaŵi zambiri zimenezi zimafuna kuti ofalitsa alingalire zosoŵa za aja amene ali mu utumiki wanthaŵi yonse, okalamba, ndi athanzi lofooka, ndipo mwina ndi enanso. Ofalitsa akhoza kuthandiza oterowo mwa kuwatenga kapena kusamalira zosoŵa zawo mwanjira zina.—Yak. 2:15-17; 1 Yoh. 3:17, 18.
5 Aja amene ali ndi zosoŵa zapadera SAYENERA kupita ku msonkhano wachigawo ndi kupempha chipinda pamene afika pakuti Dipatimenti ya Zipinda iyenera kukhala ndi umboni wa Komiti Yautumiki Yampingo.
6 Nthumwi Zochokera ku Chigawo China: Kaŵirikaŵiri, malo amene mumagaŵiridwa kukapezekako ndi aja apafupi ndi mpingo wanu. Makonzedwe akuti pakhale malo okhala okwanira, mabuku, ndi zipinda zogona, ndi zina zotero, amapangidwa pamaziko akuti unyinji wa ofalitsa adzapita ku msonkhano wachigawo kumene mpingo wawo wagaŵiridwa. Komabe, ngati pachifukwa chomveka mudzapezeka kumsonkhano umene simunagaŵiridwe ndipo mudzafuna malo ogona, mlembi wa mpingo angaode Fomu Yopemphera Chipinda ku Sosaite imene muyenera kulemba ndi kusaina. Ndiyeno itumizeni kumalikulu a msonkhano umene mudzapezekako.
7 Kugwirizanika Kwanu Kukufunika: Chipambano cha makonzedwe a malo ogona ameneŵa chikudalira pa kugwirizanika kwa onse amene akuloŵetsedwamo.—Yerekezerani ndi Ahebri 13:17.
8 Mwa kukhalapo pa misonkhano ya anthu a Yehova, timalimbitsidwa kuchita chifuniro cha Yehova ndipo timatetezeredwa ku ziyambukiro zakunja za dziko zimene zingawononge chikhulupiriro chathu chachikristu. Tonsefe tikuthokoza kuti Yehova wapereka nyengo zimenezi zakuti anthu ake odzipatulira atsitsimulidwe mwauzimu m’nthaŵi ino ya mapeto.
9 Kuletsa Moto ndi Ngozi Zina: Mosakayikira, chimene makamaka chimabutsa moto pamisonkhano sindicho kuphika chakudya pafupi ndi misasa, koma ana osayang’aniridwa oseŵera ndi moto kapena kuuyang’anira. Chotero, kaamba ka chisungiko chanu ndi cha abale anu, musalole ana anu kuyendayenda ali okha; musasiyire ana aang’ono madzi oŵira kuti awayang’anire, kapena kuti mwanjira iliyonse ayang’anire moto wophikira. Iwo angathe kuchita bwino kwambiri zinthu zimenezi kunyumba, koma pamalo a msonkhano ndi pena ndipo pafunika chisamaliro chachikulu kuti pasachitike ngozi. Anthu ambiri amakhalirana pafupi, ndipo ana amakonda kuseŵera maseŵero pamene ali ndi ana anzawo. Amacheutsidwa mosavuta ndipo samaona ngozi, ndipo pazifukwa zimenezi sitiyenera kuwapatsa makandulo, macheso kapena nyali. Vuto lina limabuka pamene makolo apita kukamvetsera maprogramu tsikulo nasiya ana aang’ono alibe wowayang’anira kumsasa. Ana ayenera kukhala pamodzi ndi makolo awo mkati mwa programu. Pamene akalinde aona ana akuyendayenda pamalo a msonkhano ali okha, ayenera kubweza anawo kwa makolo awo. Makolo, chonde gwirizanani ndi antchito a msonkhano ndipo mwakutero sonyezani ‘kukonda abale.’—1 Pet. 2:17.
10 Gulu la Yehova mwachikondi limapereka zikumbutso zapanthaŵi yake zokhudza misonkhano. Nzachisoni kunena kuti pamisonkhano ingapo m’zaka zapitazi, ena opezeka pamisonkhano anataya zinthu zawo chifukwa cha moto umene ukanapeŵedwa. Abale amene ali ndi mathayo pamisonkhano, ndipo makamaka makolo, akupemphedwa kusamalitsa mfundo zofunika zimenezi kuti misonkhano yathu idzakhale ya chiyanjano chomangirira ndi chokondweretsa, ndipo isadzakhale ya kulira ndi chisoni chifukwa cha kusasamala kochititsa ngozi.
Chidziŵitso ku Bungwe la Akulu: Akulu SAYENERA kulinganiza Msonkhano Wautumiki mkati mwa mlungu wa msonkhano. Mlungu umenewu suyenera kukhala ndi msonkhano uliwonse. Mlembi wa mpingo ayenera kusamalira nkhani zokhudza msonkhano wachigawo ndi zilengezo pa Misonkhano Yautumiki yamtsogolo ngati kutheka, kusiyapo ngati tatchula wina kapena ngati ali wosakhoza kutero.