Nyimbo 121
Chowonadi Chimene Chimamasula Anthu
1. Chilamulo cha Mose ndi ulosi wakale
Zinasonya ku cho’nadi chimene tidziŵa.
Ndicho cho’nadi chomasula, cha Mbewu ya Ya
—Mmene anthu angapezere moyo mwa Yesu.
2. ‘Ndine njira, chowonadi,’ Yesu ananena.
Anadza m’dziko kufera machimo a anthu,
Kuzadziŵitsa dzina la Atate wowona
‘Nthaŵi ya mapeto’ kugonjetsa adaniwo.
3. Kupyolera mwa Mwana wa Ya cho’nadi chadza.
Chimatitsimikiza za kutha kwa uchimo.
Ndiye Mbewu, Wolonjezedwa kutama M’lungu.
Monga Mfumu ndi Wansembe alamula tsono.
4. Ndi chikhulupiliro tilalika za Mwana.
Takonzekera kulengeza mbiri yabwino.
Ufumu Waumesiyawo tichirikize.
Tiusonyeze kwa onse agwirire ntchito.