Nyimbo 112
Ndipo Adzadziŵa
1. Adaniwo anyoza dzinalo,
Mwachinyengo adetsa malowo.
Msanga Mfumu imveketsa zanu;
Ufumu wa Satana udzatha.
(Korasi)
2. Satanayo, apeputsa mphamvu,
Idzatuluka osakanidwa.
Khamu lake, pa Armagedoyo,
Lidzafika pakuwonongedwa.
(Korasi)
3. Odzikweza nkhaza kwa ofatsa
Afuna kuma lamulirabe.
Dzanja lanu lidzathyola goli.
Oputa mkwiyo wanu adzatha.
(KORASi)
Adzadziŵa inu nokha Yehova;
Kuti njira zanu nzolungama.
Adzadziŵa muchilengedwe chonse,
Chifuno chanu mudzachichita.