Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 8/15 tsamba 8-11
  • Chifukwa Chake Mufunikira Kufika Pamisonkhano Yachikristu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chifukwa Chake Mufunikira Kufika Pamisonkhano Yachikristu
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Akristu “Amanolerana” Wina ndi Mnzake
  • Kupeza Chakudya Chauzimu m’Nthaŵi Zoŵaŵitsa
  • Zokumbutsa za Yehova​—Zonga Liwu la Kumbuyo Kwanu
  • Kulandira Mzimu Woyera Kupyolera Mumpingo
  • Maphunziro Operekedwa ndi Mpingo
  • Pezekani pa Misonkhano “Koposa”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kusonkhana?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Kodi Ndi Zinthu Ziti Zomwe Mudzasangalale Nazo Pamisonkhano Yathu Yachikhristu?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
  • Kuyamikira Misonkhano Yachikristu
    Nsanja ya Olonda—1998
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 8/15 tsamba 8-11

Chifukwa Chake Mufunikira Kufika Pamisonkhano Yachikristu

KWA miyezi yambiri, Rosario, amene amakhala ku South America, anasangalala kuphunzira Baibulo ndi Elizabeth. Zinamsangalatsa Rosario kudziŵa za Ufumu wa Mulungu ndi mmene udzabweretsera mikhalidwe ya Paradaiso padziko lapansi. Komabe, nthaŵi iliyonse imene Elizabeth anamuitana kupita kumisonkhano ku Nyumba Yaufumu, iye anakana. Analingalira kuti akhoza kuphunzirira Baibulo panyumba ndi kuchita zimene limanena, popanda kufika pamisonkhano yampingo. Kodi nanunso munayamba mwakayikira ngati misonkhano Yachikristu imakupindulitsanidi? Kodi nchifukwa ninji Mulungu anapanga makonzedwe akuti anthu ake adzisonkhana pamodzi?

Popeza kuti Akristu a m’zaka za zana loyamba anali osiyana kwambiri ndi anthu owazinga, mayanjano abwino anali ofunika kuti apulumuke. Mtumwi Paulo analembera mpingo umodzi woyambirira wa Akristu kuti: ‘Munakhala osalakwa ndi owona, opanda chirema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera ngati mauniko m’dziko lapansi.’ (Afilipi 2:15) Akristu anakumana ndi mavuto aakulu m’Yudeya, ndipo Paulo anawalembera kuti: “Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.” (Ahebri 10:24, 25) Kodi timafulumizana motani ku chikondano ndi ntchito zabwino mwakusonkhana pamodzi?

Mmene Akristu “Amanolerana” Wina ndi Mnzake

Liwu Lachigiriki limene Paulo anagwiritsira ntchito ndi lomasuliridwa monga ‘kufulumizana’ m’lingaliro lenileni limatanthauza “kunola.” Mwambi wa m’Baibulo umalongosola mmene Akristu “amanolerana” wina ndi mnzake pamene umanena kuti: “Chitsulo chinola chitsulo; chomwecho munthu anola nkhope ya mnzake.” (Miyambo 27:17; Mlaliki 10:10) Tili ngati zipangizo zimene zimafunikira kunoledwa nthaŵi zonse. Popeza kuti kukonda Yehova ndi kupanga zosankha zozikidwa pa chikhulupiriro chathu kumatanthauza kukhala osiyana ndi dziko, nthaŵi zonse tiyenera kuchita zinthu zosiyana ndi anthu onse.

Kuyesayesa kosalekeza kwakukhala osiyana kungabunthitse changu chathu kaamba ka ntchito zabwino. Koma pamene tili ndi ena amene amakonda Yehova, timanolana​—timafulumizana ku chikondano ndi ntchito zabwino. Kumbali ina, pamene tili tokha, timalingalira kwambiri za ife eni. Malingaliro oipa, adyera, kapena opusa angaloŵe m’maganizo mwathu. “Wopanduka afunafuna chifuniro chake, nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.” (Miyambo 18:1) Ndicho chifukwa chake Paulo analembera mpingo wa mumzinda wa Tesalonika kuti: “Chenjezanani, ndipo mangiriranani wina ndi mnzake, monganso mumachita.”​—1 Atesalonika 5:11.

Pamene Rosario anamaliza kuphunzira ziphunzitso zazikulu za Baibulo, iye sanafunebe kuyanjana ndi mpingo. Chotero, polephera kupereka chithandizo chowonjezereka, Elizabeth analeka kumchezera. Miyezi ingapo pambuyo pake woyang’anira woyendayenda anamfikira Rosario namfunsa kuti: “Ngakhale ngati chiŵalo chilichonse cha banja chingakhoze kupeza chakudya chabwino mwakupita kukadya ku hotela, kodi nchiyani chimene ziŵalo zonse za banjalo zidzakhala zikuphonya mwakusadyera pamodzi kunyumba?” Rosario anayankha kuti: “Akaphonya ubwenzi wa banja.” Anamvetsetsa mfundoyo ndipo anayamba kufika pamisonkhano mokhazikika. Iye amaiona kukhala yopindulitsa kwambiri kwakuti amafika pafupifupi pamsonkhano uliwonse kuyambira pamene anayamba kufikapo.

Kumva anthu ena akufotokoza chikhulupiriro chawo m’zinthu zimodzimodzizo zimene mumakhulupirira limodzinso ndi kuona ukulu wa chikhulupiriro chimene chasintha miyoyo yawo kumalimbikitsa. Paulo anadziŵa zimenezi mwa chokumana nacho chake, ndipo analembera mpingo wa ku Roma kuti: “Ndilakalaka kuonana ndinu, kuti ndikagawire kwa inu mtulo wina wauzimu, kuti inu mukhazikike; ndiko, kuti ine ndikatonthozedwe pamodzi ndi inu, mwa chikhulupiriro cha ife tonse aŵiri, chanu ndi changa.” (Aroma 1:11, 12) Kwenikweni, panapita zaka zingapo Paulo asanapite ku Roma, ndipo pamene anadzapitako, anapita monga wandende m’manja mwa Aroma. Koma pamene iye anaona abale ochokera ku Roma amene anayenda mtunda wa makilomita 60 kuchokera kumzindako kubwera kudzakumana naye, “Paulo . . . anayamika Mulungu, nalimbika mtima.”​—Machitidwe 28:15.

Kupeza Chakudya Chauzimu m’Nthaŵi Zoŵaŵitsa

Akali wobindikiritsidwa m’Roma, Paulo analembera Ahebri ponena za kusaleka kusonkhana kwawo pamodzi. Nkosangalatsa kwa ife kuti anawonjezera mawu akuti: “Koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.” (Ahebri 10:25) Mboni za Yehova zasonyeza nthaŵi zonse m’Malemba kuti chaka cha 1914 chinali kuyambika kwa nthaŵi yamapeto ya dzikoli ndi kuti “tsiku la chiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osapembedza” layandikira. (2 Petro 3:7) Malinga nkunena kwa buku la Baibulo la Chivumbulutso, pamene Mdyerekezi anagwetsedwa kumwamba pachiyambi cha nthaŵi yamapeto, iye anali ndi mkwiyo waukulu ndipo ‘anachoka kumka kuchita nkhondo ndi otsala . . . amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nawo umboni wa Yesu.’ (Chivumbulutso 12:7-17) Chifukwa chake, kusunga malamulo a Mulungu nkovuta kwambiri tsopano; tifunikira kusonkhana ndi okhulupirira anzathu koposa ndi kalelonse. Misonkhano idzatithandiza kulimbitsa chikhulupiriro chathu ndi chikondi chathu cha pa Mulungu kotero kuti tipeŵe ziukiro za Mdyerekezi.

Chikondi cha pa Mulungu ndi chikhulupiriro sizili ngati nyumba zimene zimamangidwa kamodzi kwatha. M’malomwake, zili ngati zinthu zamoyo zimene zimakula pang’onopang’ono ndi chakudya chosalekeza ndipo zimafota ndi kufa ngati zamanidwa chakudya. Nchifukwa chake Yehova amapereka chakudya chauzimu chosalekeza kuti alimbitse anthu ake. Tonsefe timafunikira chakudya chimenecho, koma kodi nkuti kumene tingalandire chakudyacho kusiyapo ku gulu la Mulungu ndi misonkhano yake? Palibe.​—Deuteronomo 32:2; Mateyu 4:4; 5:3.

Yesu anafunsa funso limene lingatithandize kuona mmene amadyetsera mpingo Wachikristu. Iye anafunsa kuti: “Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake anamkhazika woyang’anira banja lake, kuwapatsa zakudya pa nthaŵi yake? Wodala kapolo amene mbuye wake, pakufika, adzampeza iye alikuchita chotero.” (Mateyu 24:45, 46) Kodi ndani amene Yesu anamuika m’zaka za zana loyamba kudyetsa otsatira ake, ndipo ndani amene anampeza akuwadyetsa mokhulupirika pamene anabwerera muulamuliro wa Ufumu? Mwachidziŵikire, palibe munthu amene anakhala kwa nthaŵi ya zaka mazana amenewo. Umboni umaloza kwa kapoloyo kukhala mpingo wa Akristu odzozedwa ndi mzimu, monga momwe mtundu wa Israyeli unaliri mtumiki wa Mulungu nthaŵi ya Chikristu chisanakhale. (Yesaya 43:10) Inde, Yesu amapereka chakudya chauzimu kudzera m’bungwe lapadziko lonse la Akristu odzozedwa ndi mzimu, limene limapereka chakudya chauzimucho kupyolera m’mipingo ya Mboni za Yehova.

Makonzedwe a Yesu okhala ndi njira yoperekera chakudya chauzimu analongosoledwa mowonjezereka ndi mtumwi Paulo kuti: “Mmene anakwera kumwamba, anamanga ndende undende, naninkha zaufulu kwa anthu. . . . Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi; kuti akonzere oyera mtima ku ntchito ya utumiki, kumangirira thupi la Kristu; kufikira ife tonse tikafikira ku umodzi wa chikhulupiriro, ndi wa chizindikiritso cha Mwana wa Mulungu, kwa munthu wangwiro, ku muyeso wa msinkhu wa chidzalo cha Kristu.”​—Aefeso 4:8, 11-13.

Munali makamaka m’mipingo​—pamisonkhano​—pamene “zaufulu kwa anthu” zimenezi zinamangirira abale. Mwachitsanzo, mu Antiokeya, “Yuda ndi Sila, okhala eni okha aneneri, anasangalatsa abale ndi mawu ambiri, nawalimbikitsa.” (Machitidwe 15:32) Mofananamo lerolino, nkhani zokambidwa ndi amuna oyeneretsedwa mwauzimu zidzalimbitsa chikhulupiriro chathu kotero kuti sichidzafota kapena kukhala chofooka.

Zingakhale zowona kuti tapanga kupita patsogolo kwabwino chifukwa cha chithandizo chaumwini choperekedwa ndi chiŵalo cha mpingo ngakhale kuti tingakhale tisanayambe kufika pamisonkhano. Baibulo limanena kuti pali nthaŵi imene mumafunikira “kuti wina aphunzitse inu zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu; ndipo mukhala . . . ofuna mkaka, osati chakudya chotafuna.” (Ahebri 5:12) Koma munthu sangakhalire kumwa mkaka nthaŵi zonse. Misonkhano Yachikristu imapereka programu yosalekeza ya chilangizo cha Baibulo cholinganizidwira kuchititsa chikondi cha pa Mulungu ndi chikhulupiriro mwa iye kukhala chamoyo limodzinso ndi kupereka chithandizo chogwira ntchito m’kugwiritsira ntchito “uphungu wonse wa Mulungu.” (Machitidwe 20:27) Zimenezo nzoposa “mkaka.” Baibulo limawonjezera kunena kuti: “Chakudya chotafuna chili cha anthu aakulu misinkhu, amene mwa kuchita nazo anazoloŵeretsa zizindikiritso zawo kusiyanitsa chabwino ndi choipa.” (Ahebri 5:14) Pamisonkhanopo nkhani zambiri zimakambidwa zimene sizingakhale mbali ya kosi ya phunziro la Baibulo lapanyumba, monga ngati phunziro la vesi ndi vesi la maulosi ofunika a Baibulo ndi kukambitsirana kozama kwa mmene tingatsanzirire Mulungu m’miyoyo yathu.

Zokumbutsa za Yehova​—Zonga Liwu la Kumbuyo Kwanu

Kupyolera m’maphunziro ampingo oterowo, Yehova amatikumbutsa mosalekeza za mtundu wa anthu amene tiyenera kukhala. Zokumbutsa zimenezo nzofunika kwambiri. Popanda izo timakhoterera kukhala adyera, onyada, ndi aumbombo. Zokumbutsa za m’Malemba zidzatithandiza kusangalala ndi maunansi abwino ndi anthu ena ndi Mulungu mwiniyo. “Ndaganizira njira zanga, ndipo ndinabweza mapazi anga atsate mboni zanu,” anavomereza motero wolemba Salmo 119:59.

Pamene tifika pamisonkhano Yachikristu mokhazikika, timaona kugwira ntchito kwa ulosi wa Yehova kudzera mwa Yesaya, umene umati: “[Mlangizi wanu Wamkulu, NW] sadzabisikanso, koma maso ako adzaona [Mlangizi wanu Wamkulu]; ndipo makutu ako adzamva mawu kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m’menemo.” Yehova amayang’anira kupita patsogolo kwathu ndipo amatiwongolera mwachikondi ngati titenga njira yolakwika. (Yesaya 30:20, 21; Agalatiya 6:1) Ndipo amapereka chithandizo chochuluka kuposa chimenechi.

Kulandira Mzimu Woyera Kupyolera Mumpingo

Mwakufika mokhazikika pamisonkhano Yachikristu ndi Mboni za Yehova, timalimbikitsidwa ndi mzimu woyera wa Mulungu, umene umakhala pa anthu ake. (1 Petro 4:14) Ndiponso, oyang’anira Achikristu a mumpingo anaikidwa ndi mzimu woyera. (Machitidwe 20:28) Mphamvu yogwira ntchito yochokera kwa Mulungu imeneyi ili ndi chisonkhezero champhamvu pa Mkristu. Baibulo limati: “Chipatso cha mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso.” (Agalatiya 5:22, 23) Mzimu woyera, umene umagwira ntchito kupyolera m’gulu la Mulungu, udzatithandizanso kumvetsetsa bwino zimene Yehova adzapatsa amene amamkonda. Pambuyo polongosola kuti anthu otchuka a dongosolo lino la zinthu sangamvetsetse zifuno za Mulungu, Paulo analemba kuti: “Koma kwa ife Mulungu anationetsera izi mwa mzimu; pakuti mzimu [u]santhula zonse, zakuya za Mulungu zomwe.”​—1 Akorinto 2:8-10.

Kuwonjezera pa chakudya chauzimu cholimbitsa chikhulupiriro, mpingo umapereka maphunziro kwa awo amene amafuna kukhala ndi phande m’ntchito yaikulu ya mpingo. Ntchito yanji?

Maphunziro Operekedwa ndi Mpingo

Mpingo Wachikristu simalo ochezera kumene anthu amangopita kukasangalala ndi zosanguluka kapena kukalimbikitsana wina ndi mnzake kukhala ndi miyoyo yabwino kwambiri. Yesu anatuma mpingo kupereka mbiri yabwino ya Ufumu kwa awo okhala mumdima wauzimu. (Machitidwe 1:8; 1 Petro 2:9) Kuyambira patsiku limene unakhazikitsidwa, pa Pentekoste wa 33 C.E., unali gulu la alaliki. (Machitidwe 2:4) Kodi munayamba mwayesa kuuza munthu wina za zifuno za Yehova koma munalephera kumkhutiritsa? Misonkhano yampingo imapereka maphunziro aumwini m’luso la kuphunzitsa. Mwakuphunzira zitsanzo za m’Baibulo, timaphunzira mmene tingakhazikitsire maziko amodzi amene tingagwiritsire ntchito kukambitsirana, mmene tingagwiritsirire ntchito Malemba monga maziko a zigomeko zanzeru, ndi mmene tingathandizire ena kulingalira mwakugwiritsira ntchito mafunso ndi mafanizo. Maluso oterowo angakuthandizeni kukhala ndi chisangalalo chosaneneka chakuthandiza munthu wina kumvetsetsa chowonadi cha Baibulo.

M’dziko lino lodzaza ndi mikangano, ndi chisembwere, mpingo Wachikristu ulidi pothawirapo pauzimu penipeni. Ngakhale kuti ngwopangidwa ndi anthu opanda ungwiro, uli phanga la mtendere ndi chikondi. Chotero, khalani wofika pamisonkhano yake yonse wokhazikika ndi kudzionera nokha kuwona kwa mawu a wamasalmo akuti: “Onani, nkokoma ndi kokondweretsa ndithu kuti abale akhale pamodzi! . . . Yehova analamulira dalitsolo, ndilo moyo womka muyaya.”​—Salmo 133:1, 3.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena