Pezekani pa Misonkhano “Koposa”
1 Nthaŵi zonse misonkhano yakhala yofunika kwambiri kwa anthu a Yehova. Aisrayeli anali ndi kachisi ndi masunagoge awo amene anali malo a kulambira koona, maphunziro aumulungu, ndi kuyanjana kwachimwemwe. Mofananamo, Akristu oyambirira sanaleke kusonkhana pamodzi. Pamene mavuto ndi ziyeso zikuwonjezereka masiku ano otsiriza oŵaŵitsa, ifenso tifunikira chilimbikitso chauzimu chimene misonkhano yathu ya mpingo imapereka—ndipo tikuchifunikira “koposa.” (Aheb. 10:25) Taonani zifukwa zitatu zimene timapezekera pamisonkhano.
2 Kuti Tikhale ndi Mayanjano: Malemba amatilangiza ‘kuchenjezana [‘kutonthozana,’ NW], ndipo kumangirirana wina ndi mnzake.’ (1 Ates. 5:11) Mayanjano aumulungu amadzaza maganizo athu ndi malingaliro abwino ndi kutisonkhezera kuchita ntchito zabwino. Koma ngati tidzipatula ife eni, malingaliro opusa, adyera, kapena ngakhale oipa angatiloŵe.—Miy. 18:1.
3 Kuti Tilandire Malangizo: Misonkhano yachikristu imakhala ndi programu yosatha ya malangizo a Baibulo amene cholinga chake ndicho chakuti chikondi chathu pa Mulungu chikhalebe chamoyo m’mitima yathu. Imapereka chitsogozo chothandiza ponena za mmene tingagwiritsire ntchito “uphungu wonse wa Mulungu.” (Mac. 20:27) Misonkhano imatiphunzitsa luso la kulalikira ndi kuphunzitsa za uthenga wabwino, maluso ofunika koposa tsopano kuti tikhale ndi chimwemwe chosaneneka cha kupeza ndi kuthandiza aja amene amalandira choonadi cha Baibulo.
4 Kuti Tipeze Chitetezo: M’dziko lino loipa, mpingo ndiwo ngaka yeniyeni yauzimu—malo a mtendere ndi chikondi. Pamene tili pamisonkhano ya mpingo, mzimu woyera wa Mulungu umagwira ntchito pa ife mwamphamvu, kutithandiza kuonetsa chipatso cha “chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso.” (Agal. 5:22, 23) Misonkhano imatichirikiza kuti tikhale ochirimika ndi olimba m’chikhulupiriro. Imatikonzekeretsa kaamba ka mayeso amtsogolo.
5 Mwa kupezeka pamisonkhano nthaŵi zonse, timapeza zimene wamasalmo anafotokoza, zolembedwa pa Salmo 133:1, 3 kuti: “Onani, nkokoma ndi kokondweretsa ndithu kuti abale akhale pamodzi!” Paliponse lero pamene anthu a Mulungu amatumikira ndi kusonkhana pamodzi, ‘pamenepo Yehova analamulira dalitsolo, ndilo moyo womka muyaya.’