Utumiki Wathu—Umboni wa Chikondi Choona
1 Mwa utumiki wathu, timasonyeza kumvera kwathu malamulo aŵiri aakulu koposa. (Mat. 22:37-39) Kukonda kwathu Yehova kumatisonkhezera kulankhula zabwino ponena za iye. Kukonda kwathu anansi athu kumatisonkhezera kuwalimbikitsa kufunafuna chidziŵitso cha chifuniro cha Mulungu ndi zifuno zake kuti, mofanana ndi ifeyo, angayambe kukonda Yehova ndi kukhala ndi mpata wolandira mphoto ya moyo wosatha. Chotero, mwa utumiki wathu, timalemekeza dzina la Yehova ndi kuuzako anansi athu za chiyembekezo chamtengo wapatali cha Ufumu. Inde, utumiki wathu ndiwo umboni wakuti timakondadi Mulungu ndi anthu anzathu.
2 Chikondi chathu chimatisonkhezera kulankhula kwa anthu a mtundu uliwonse ndiponso a mikhalidwe yosiyanasiyana. (1 Akor. 9:21-23) Mwachitsanzo: Mkristu wina, mkulu, anakhala mpando umodzi ndi wansembe wa Roma Katolika m’ndege. Mkuluyo anamasula wansembeyo kuti alankhule mwa kumfunsa mafunso mwanzeru ndiyeno nkuyamba kukambitsirana za Ufumu. Nthaŵi imene wansembeyo anali kutsika pandege, anali atalandira mabuku athu aŵiri. Ndi zotsatira zabwino chotani nanga zimene zinakhalapo chifukwa chakuti mkuluyo anasonyeza chikondi choona kwa mnansi wake!
3 Chikondi Choona Chimatisonkhezera Kulalikira: Amene amachita ntchito ya upainiya wothandiza ndi wanthaŵi zonse akusonyezadi chikondi choona kwa Mulungu ndi anansi awo. Nthaŵi zonse apainiya amawononga nthaŵi yawo ndi nyonga kuti athandize ena mwauzimu. Kodi nchiyani chimawasonkhezera kuchita zimenezo? Mpainiya wina anati: “Ndikudziŵa kuti chikondi chili chipatso cha mzimu wa Mulungu. Chotero, popanda icho sindikanakhala m’choonadi, sindikanakhoza ndi upainiya womwe. Chikondi chimandithandiza kulingalira za anthu, kuzindikira zofuna zawo, ndipo ndimadziŵa kuti anthu amakopeka nacho chikondi.” Yesu anasonyeza chikondi chotero kwa anthu. Nthaŵi ina pamene iyeyo ndi ophunzira ake otopa anali kupita kwina kwake kuti ‘akapume kamphindi,’ makamu anatsogola nayambirira kufika. Kodi Yesu anatani? ‘Atagwidwa chifundo ndi iwo,’ anaika pambali zofuna zake kuti ‘awaphunzitse zinthu zambiri.’—Marko 6:30-34.
4 Ngakhale pamene anthu akana uthenga wabwino umene timapereka, timakhala ndi chimwemwe mumtima, podziŵa kuti pokhala timasonkhezeredwa ndi chikondi, tachita zomwe tingathe kuwathandiza kuti apeze chipulumutso. Pamene tonsefe tiweruzidwa ndi Kristu pomalizira pake, tidzakhala okondwa kwambiri kuti tinasonyeza chikondi choona mwa ‘kukwaniritsa utumiki wathu.’—2 Tim. 4:5.