Dziŵitsani Ena za Chiyembekezo cha Moyo Wosatha
1 Ngakhale kuti munthu wafufuza njira zochedwetsera kukalamba kuti atalikitse moyo wake, ukalamba ndi imfa nzosapeŵekabe. Tikuyamikira chotani nanga kuti Baibulo limafotokoza chifukwa chimene anthu amakalambira ndi kufa, ndiponso mmene ukalamba ndi zovuta zake zidzachotsedwera ndi mmene imfa idzathetsedwera. Choonadi chimenechi chafotokozedwa mokhutiritsa m’buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Bukulo limayankha momveka bwino mafunso ovuta onena za moyo ndi imfa, likumamsonyeza woŵerengayo nthaŵi imene Paradaiso adzabwezeretsedwa.
2 M’March muno tizigaŵira buku la Chidziŵitso ncholinga choyamba maphunziro a Baibulo apanyumba. (Mat. 28:19, 20) Ndiyeno tizibwerera kwa onse amene anachita chidwi ndi uthenga wa Ufumu. Mwakutero, tidzadziŵitsa ena za chiyembekezo cha moyo wosatha. (Tito 1:2) Kuti muthe kuchita zimenezo, mwina mungaone kuti malingaliro otsatirawa ngothandiza.
3 Paulendo woyamba, mungafunse kuti:
◼ “Kodi munadzifunsapo chifukwa chake anthu amakhumbira moyo wautali? [Yembekezerani yankho.] Abuda, Akristu, Ahindu, Asilamu, ndi ena onse amayembekezera moyo wina pambuyo pa imfa.” Tsegulani buku la Chidziŵitso pamutu 6, “Kodi Nchifukwa Ninji Timakalamba ndi Kufa?,” ndiye muŵerenge ndime 3. Kambitsiranani malemba omwe asonyezedwamowo. Potchula mafunso aŵiri ali kumapeto kwa ndimeyo, mfunseni mwini nyumbayo ngati angakonde kupeza yekha mayankho ake. Ngati akufuna zimenezo, pitirizani kukambitsirana ndime zoŵerengeka zotsatirazo. Mukatero basi phunziro layambika! Kapena ingomsiyirani bukulo pa chopereka chanthaŵi zonse kuti aziŵerenga, ndiye panganani kuti mudzabwerereko, zingakhale bwino mutatero patangopita tsiku limodzi kapena aŵiri, kuti mukakambitsirane mafunsowo.
4 Mutabwerera kumene munasiya buku la “Chidziŵitso,” munganene kuti:
◼ “Ndabweranso kuti tidzakambitsirane mafunso aja onena za imfa, omwe tinasiya osayankhidwa.” Mkumbutseni mwini nyumba mafunsowo. Ndiyeno kambitsiranani mfundo zili m’mutu 6 pa kamutu kakuti “Chiŵembu Chausatana.” Ngati mikhalidwe ikulola, mwina pitirizani phunzirolo kapena funsani funso lili kumapeto kwa ndime 7 kuti padzakhale poyambira kukambitsirana paulendo wotsatira. Tsimikizani kudzabwererako. Muitanireni kumsonkhano ndiye mlongosolereni mwachidule mmene timachitira misonkhano yampingo. Mpempheni mwaulemu kuti adzapezekepo.
5 Kaya ndi pantchito ya kukhomo ndi khomo kapena ndi umboni wamwamwaŵi, mungayambe kukambitsirana mwa kunena kuti:
◼ “Kodi munadzifunsapo kuti mtsogolomu mulinji kwa ife ndi dziko lapansili? [Yembekezerani yankho.] Baibulo limatchula mwa liwu limodzi ponena za mtsogolo—Paradaiso! Limalongosola kuti pachiyambi, Mulungu anapanga chigawo china chadziko nkukhala paradaiso wokongola m’mene anaikamo mwamuna ndi mkazi wake omwe anawalenga. Anali oti adzaze dziko lonse lapansi, nkumalisanduliza pang’onopang’ono kukhala paradaiso. Tamvani mmene mawuwa akufotokozera mmene paradaisoyo anaonekera.” Tsegulani buku la Chidziŵitso patsamba 8, ndiye ŵerengani ndime 9, pa kamutu kakuti “Moyo M’Paradaiso.” Kenaka kambitsiranani mfundo zili m’ndime 10, ndiyeno muŵerenge lemba latchulidwamolo, Yesaya 55:10, 11. Kambitsiranani za mmene moyo udzakhalira m’Paradaiso wobwezeretsedwa ndiyeno phunzirani ndime 11-16 pamodzi. Kapena mlimbikitseni munthuyo kuŵerenga yekha, ndipo panganani kuti mudzaonanenso kuti mudzakambitsirane.
6 Ngati paulendo woyamba simunathe kuyamba phunziro, mungayese kutero paulendo wobwereza mwa kunena kuti:
◼ “Monga tinakambitsirana pakucheza kwathu koyamba, cholinga cha Mulungu nchakuti dziko lonseli lidzasandulizidwe likhale paradaiso. Ndiye funso nlakuti, Kodi Paradaisoyo adzakhala wotani?” Tsegulani buku la Chidziŵitso pamutu 1, ndiye phunzirani ndime 11-16, pa kamutu kakuti “Moyo m’Paradaiso Wobwezeretsedwa.” Pambuyo pake msonyezeni chithunzi chili pamasamba 4-5, ndiye mfunseni munthuyo ngati angakonde kudzakhala m’malo okongola oterowo. Kenaka ŵerengani mzera woyamba wa ndime 17 patsamba 10. Ngati mikhalidwe ikulola, mwina pitirizani phunzirolo kapena teroni kuti paulendo wotsatira mudzafotokoza zimene zikufunika kuti munthu akhale ndi moyo m’Paradaiso wobwezeretsedwa. Fotokozaninso mwachidule mmene timachitira misonkhano yampingo, ndipo mpempheni munthuyo mwaulemu kuti adzapezeke pa Nyumba ya Ufumu.
7 Buku la Chidziŵitso ndilo chiŵiya chabwino kwambiri chogwiritsira ntchito povumbulira ena “moyo wosatha” womwe Mulungu walonjeza. Mukamachititsa maphunziro a Baibulo a panyumba mungadziŵitse anthu za chiyembekezo chachikulu chouziridwa ndi Mulungu “wosanamayo.”