Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/98 tsamba 7
  • Bokosi la Mafunso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bokosi la Mafunso
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Nkhani Yofanana
  • Bokosi la Mafunso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Bokosi la Mafunso
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Tizivala Ndi Kudzikongoletsa Moyenera
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kodi Muli ndi Mtima Wofewa Ngati Mnofu?
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
km 3/98 tsamba 7

Bokosi la Mafunso

◼ Kodi nchifukwa chiyani tiyenera kusamala kwambiri kavalidwe ndi kapesedwe kathu pokachezera nyumba za Sosaite ku Lilongwe ndi maofesi anthambi padziko lonse lapansi?

Akristu amayembekezeredwa kukhala ooneka bwino. Nthaŵi zonse kuvala kwathu ndi kupesa kwathu kuyenera kutisonyeza kuti ndife odekha ndi olemekezeka monga atumiki a Yehova Mulungu. Kwenikweni zizikhala choncho pomakachezera nyumba za Sosaite ku Lilongwe ndi kunthambi za padziko lonse.

Mu 1998 muno, kudzakhala misonkhano yachigawo ndi yamitundu yomwe. Abale athu zikwizikwi ochokera m’maiko ambiri adzakacheza kulikulu la Sosaite ku New York ngakhalenso kunthambi za m’maiko ena. Osati pokachezera nyumba zimenezo basi, komanso panthaŵi ina iliyonse, tifunikira ‘kumadzitsimikizira tokha monga atumiki a Mulungu mwa njira iliyonse,’ kuphatikizapo kuvala ndi kupesa bwino.—2 Akor. 6:3, 4.

Pofotokoza za kufunika kwa kuvala ndi kupesa bwino, buku la Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu, limati nkofunika kukhala aukhondo mwakuthupi kuvala mwaulemu ndi kupesa bwino poloŵa mu utumiki wakumunda ndi popita kumisonkhano yachikristu. Ndiyeno, patsamba 131, ndime 2, limati: “Zikakhalanso zomwezo powona nyumba Yabeteli ku Brooklyn kapena iliyonse ya maofesi anthambi a Sosaite. Kumbukirani, dzinalo Beteli limatanthauza ‘Nyumba ya Mulungu,’ motero kuvala kwathu, kupesa ndi khalidwe ziyenera kukhala zolingana ndi zimene zimayembekezeredwa kwa ife pofika pa misonkhano ya kulambira pa Nyumba ya Ufumu.” Ofalitsa Ufumu a chapafupi ngakhalenso ochokera kutali omwe amabwera kudzacheza ndi abanja la Beteli ndiponso pochezera nyumba zanthambi ayenera kusonyeza khalidwe labwino lofananalo.

Zovala zathu ziyenera kupangitsa ena kuzindikira kuti kulambira Yehova moona kumakhudzanso kavalidwe. Komabe, zaoneka kuti abale ndi alongo ena pomakachezera nyumba za Sosaite, amavala mosasamala kwenikweni. Kuvala koteroko sikoyenera pokachezera nyumba iliyonse ya Beteli. Pankhani imeneyi, monga zilili ndi mbali zina za moyo wathu wachikristu, tikufuna kukhala ndi mikhalidwe yabwino kwambiri imene imasiyanitsa anthu a Mulungu ndi dzikoli mwa kuchita zinthu zonse ku ulemerero wa Mulungu. (Aroma 12:2; 1 Akor. 10:31) Tingachitenso bwino kuuza ophunzira athu a Baibulo ndi enanso amene akukacheza ku Beteli kwa nthaŵi yoyamba ndi kuwakumbutsa kuti nkofunika kuvala ndi kupesa bwino.

Choncho pokachezera nyumba za Sosaite, dzifunseni kuti: ‘Kodi ndavala ndi kupesa mwaulemu?’ (Yerekezerani ndi Mika 6:8.) ‘Kodi zikulemekeza Mulungu yemwe ndimalambira? Kodi ena angamandicheukire kapena kukhumudwa ndi mmene ndikuonekera? Kodi ndikusonyeza ena chitsanzo chabwino omwe angakhale akukachezako kwa nthaŵi yoyamba?’ Tiyenitu nthaŵi zonse ‘tizikometsera chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu, Mulungu m’zinthu zonse,’ mwa kavalidwe ndi kapesedwe kathu.—Tito 2:10.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena