Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/08 tsamba 7
  • Bokosi la Mafunso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bokosi la Mafunso
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Nkhani Yofanana
  • Bokosi la Mafunso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Bokosi la Mafunso
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Tizivala Ndi Kudzikongoletsa Moyenera
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kuvala Moyenera Kumasonyeza Kuti Tikulemekeza Mulungu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
km 3/08 tsamba 7

Bokosi la Mafunso

◼ Kodi tizivala motani popita ku Nyumba za Ufumu, Malo a Misonkhano, nyumba za Beteli ndiponso ku maofesi a nthambi?

Padziko lonse lapansi, Nyumba za Ufumu, Malo a Misonkhano, nyumba za Beteli ndiponso maofesi a nthambi ndi malo apadera omwe anaperekedwa kwa Yehova kuti tizimutumikirapo. Malowa ndi oyera, aukhondo ndiponso okonzedwa bwino komanso olemekezeka. Zimenezi ndi zosiyana kwambiri ndi zimene timaona m’dongosolo la Satanali. Amene amapita ku malo amenewa ayeneranso kudziwika kuti ndi anthu a Yehova, omwe amachita chifuniro chake.

Akhristufe, ‘timadzichitira umboni mwa njira ina iliyonse kuti ndife atumiki a Mulungu,’ kuphatikizapo kuvala ndi kudzikongoletsa moyenera. (2 Akor. 6:3, 4) Timafunikiranso kupitiriza kukhala a khalidwe labwino. Nthawi zonse kuvala ndi kudzikongoletsa kwathu kuzikhala koyenera atumiki a Yehova Mulungu. Tiziteronso makamaka popita ku likulu la Mboni za Yehova ku New York, ngakhale ku maofesi a nthambi padziko lonse lapansi.

Buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova limanena kuti ukhondo, kuvala komanso kudzikongoletsa moyenera popita kukalalikira ndiponso kumisonkhano yachikhristu, ndi kofunika kwambiri. Tsamba 138, ndime 3, m’bukuli imati: “Kumbukirani kuti dzina lakuti Beteli limatanthauza ‘Nyumba ya Mulungu.’ Chotero, kavalidwe kathu, mmene tadzikongoletsera, ndiponso khalidwe lathu, zizigwirizana ndi mmene timakhalira ku Nyumba ya Ufumu tikapita kukalambira pamisonkhano.” Ofalitsa Ufumu amene akupita ku Beteli kaya akuchokera pafupi kapena kutali, ayenera kutsatira kavalidwe kapamwamba kameneka. Alendowo akamatero, amasonyeza kuyamikira ndiponso ulemu.—Sal. 29:2.

Kavalidwe kathu kazisonyeza kuti ndife anthu “amene amati amalemekeza Mulungu.” (1 Tim. 2:10) Kavalidwe ndi kaonekedwe kathu kangathandize ena kudziwa kuti timalambira Yehova moona. Komabe, kwaoneka kuti abale ndi alongo ena akamapita ku malowa amavala motayirira kwambiri, mwauve, kapena amavala zovala zoonekera m’kati. Kavalidwe kotere n’kosayenera kwa Mkhristu panthawi ina iliyonse. Pankhani imeneyi, ngakhalenso m’zochitika zonse m’moyo wathu wachikhristu, timafunika kukhalabe ndi makhalidwe apamwamba amene amasiyanitsa anthu a Mulungu ndi dzikoli. Tiyenera kuchita zonse ku ulemerero wa Mulungu.—Aroma 12:2; 1 Akor. 10:31.

Choncho, tikamapita ku likulu la Mboni za Yehova ku New York, kapena nthambi ina iliyonse, kaya ulendowo tinachita kuukonza kapena tangopezeka kumeneko patchuthi, tizidzifunsa kuti: ‘Kodi kavalidwe ndi kudzikongoletsa kwanga zikuyenerana ndi kuyera, ukhondo ndi ulemu wa kumalo kumene ndikupita? Kodi kaonekedwe kanga kakulemekeza Mulungu amene ndimamulambira? Kodi ena angakhumudwe ndi mmene ndikuonekera?’ Mwakuvala ndi kudzikongoletsa moyenera tiyeni ‘tikometsere chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu, Mulungu, m’zinthu zonse.’—Tito 2:10.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena