Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/03 tsamba 5
  • Kuvala Moyenera Kumasonyeza Kuti Tikulemekeza Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuvala Moyenera Kumasonyeza Kuti Tikulemekeza Mulungu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Nkhani Yofanana
  • Valani ndi Kudzikongoletsa Bwino
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Tizivala Ndi Kudzikongoletsa Moyenera
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Bokosi la Mafunso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Onekani Bwino Ndiponso Modzilemekeza
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
km 7/03 tsamba 5

Kuvala Moyenera Kumasonyeza Kuti Tikulemekeza Mulungu

1. Kodi tingasonyeze bwanji kuyamikira msonkhano wathu wachigawo umene ukubwerawu?

1 Posachedwapa tikhala ndi mwayi wokhala alendo a Yehova pa Msonkhano Wachigawo wa 2003 wakuti “Patsani Mulungu Ulemerero.” Tikuthokoza kwambiri Yehova potiitana ku phwando lalikulu lauzimu limeneli. Tingasonyeze kumulemekeza ndi kumuyamikira chifukwa cha zinthu zauzimu zimene wapereka mwa kavalidwe ndi kudzisamalira kwathu.—Sal. 116:12, 17.

2. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala oyera ndiponso odzisamalira bwino?

2 Zoyera ndi Zadongosolo: Maonekedwe athu ayenera kusonyeza miyezo ya Mulungu wathu, yemwe ndi woyera ndiponso wadongosolo. (1 Akor. 14:33; 2 Akor. 7:1) Thupi, tsitsi, ndi zikhadabo zathu ziyenera kukhala zoyera ndiponso tiyenera kuoneka bwino. Masiku ano, anthu ambiri sadzisamalira bwino. Komabe, Mkristu sayenera kutsatira munthu wotchuka wa m’mafilimu kapena katswiri wa maseŵero amene sadzisamalira bwino. Ngati titsatira mafashoni, anthu sangathe kusiyanitsa amene akutumikira Mulungu woona ndi amene sakum’tumikira.—Mal. 3:18.

3. Kodi tingatani kuti tionetsetse kuti maonekedwe athu adzagwirizana ndi langizo limene lili pa 1 Timoteo 2:9, 10?

3 Zovala Zoyenera Atumiki Achikristu: Pamene mtumwi Paulo analembera kalata Timoteo yemwe anali woyang’anira wachikristu, analimbikitsa kuti “akazi adziveke okha ndi chovala choyenera, ndi manyazi, ndi chidziletso . . . (umo mokomera akazi akuvomereza kulemekeza Mulungu), mwa ntchito zabwino.” (1 Tim. 2:9, 10) Kuganiza mosamala n’kofunika kuti tionetsetse kuti zovala zathu n’zoyenera. Zovala ziyenera kukhala zooneka bwino, zoyera, ndiponso zabwino, osati zodzionetsera kapena zodzutsa chilakolako choipa.—1 Pet. 3:3.

4, 5. Kodi amuna ndi akazi achikristu ayenera kumvera langizo lotani?

4 Paulo anachenjezanso kuti tipeŵe kupitirira malire pankhani ya ‘kuluka tsitsi, ndi golidi kapena ngale, kapena malaya a mtengo wake wapatali.’ (1 Tim. 2:9) Kukhala osamala pogwiritsa ntchito zodzikongoletsera za mtengo wapatali ndiponso zodzikongoletsera zina n’kofunika kwambiri kwa akazi achikristu.—Miy. 11:2.

5 Mfundo za langizo limene Paulo anapereka kwa akazi achikristu zimagwiranso ntchito kwa amuna achikristu. Abale ayenera kupeŵa masitayelo amene amasonyeza maganizo a dzikoli. (1 Yoh. 2:16) Mwachitsanzo, m’mayiko ena zovala zazikulu, zopitirira saizi n’zotchuka, koma kuvala zovala zotero n’kosayenera kwa mtumiki wa Mulungu.

6. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kukhalabe ndi miyezo yapamwamba ya kavalidwe ndi kudzisamalira popita ndiponso pochokera ku msonkhano, pamsonkhanopo, ndiponso pulogalamu ya tsiku lililonse ikatha?

6 Pochita Zinthu Zina Pulogalamu Itatha: Pamene pulogalamu ili m’kati, abale ndi alongo ambiri amapereka chitsanzo chabwino pankhani ya kavalidwe ndi kudzisamalira. Komabe, malipoti akusonyeza kuti ena amatayirira akamapita kapena akamachokera ku msonkhano kapenanso akamachita zinthu zina panthaŵi yoti pulogalamu ya tsikulo yatha. Kunena zoona, maonekedwe athu, kaya pulogalamu ili m’kati kapena nthaŵi ina iliyonse, amakhudza mmene ena angaonere anthu a Mulungu. Popeza timavala mabaji athu a msonkhano, nthaŵi zonse tiyenera kuvala mokomera atumiki achikristu. Zimenezi nthaŵi zambiri zimachititsa ena kutiyamikira ndipo zimatithandiza kuwalalikira.—1 Akor. 10:31-33.

7. Kodi kavalidwe ndi kudzisamalira kwathu bwino zingakhudze bwanji ena?

7 Monga mmene kumwetulira kwaubwenzi kumakongoletsera nkhope yathu, kuvala bwino ndi kudzisamalira bwino kumalemekeza uthenga umene timalalikira ndiponso gulu limene timaliimira. Ena amene adzationa pa Msokhano Wachigawo wakuti “Patsani Mulungu Ulemerero” chaka chino angalimbikitsike kufunsa chifukwa chake ndife osiyana ndi anthu ena ndipo m’kupita kwa nthaŵi anganene kuti: “Tidzamuka nanu, pakuti tamva [ndi kuona] kuti Mulungu ali ndi inu.” (Zek. 8:23) Tiyenitu tonsefe tisonyeze kulemekeza Yehova mwa kavalidwe ndi kudzisamalira kwathu.

[Bokosi patsamba 5]

Onekani Mwaulemu

▪ Popita kapena pochokera ku msonkhano

▪ Pamsonkhanopo

▪ Pochita zinthu zina pulogalamu itatha

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena