Onekani Bwino Ndiponso Modzilemekeza
1. Pokonzekera msonkhano wachigawo, n’chifukwa chiyani tiyenera kusamalira maonekedwe athu?
1 “Mboni za Yehova ndi anthu abwino kwambiri! Anthu anu ndi okoma mtima ndiponso ovala bwino, ndipo ndi aulemu kwambiri.” Anatero woimira ogwira ntchito pa hotela ina ponena za abale ndi alongo pamsonkhano wina wachigawo wachaka chatha. Pamsonkhano winanso wachigawo, wogwira ntchito pa hotela ina anati: “N’zoonekeratu kuti anthu anu amavala kuti akondweretse Mulungu.” Inde, nthumwi za pamsonkhano zimaonedwa ndi anthu ena. Choncho tifunika kuvala ‘moyenerera Uthenga Wabwino’ ndipo zimenezi nthaŵi zambiri zimachititsa anthu amene si Mboni kutiyamikira komanso zimasonyezeratu kuti ndife atumiki a Mulungu. (Afil. 1:27) Pamene tikukonzekera msonkhano wachigawo, n’koyenera kuganizira pasanakhale za maonekedwe athu.
2. N’chifukwa chiyani n’kovuta kuvala ndi kudzikongoletsa bwino?
2 Wophunzira Yakobo analemba kuti: “Nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera.” (Yak. 3:17) Zingakhale zovuta kukhala oyera m’maonekedwe athu. Dziko la Satana loipali limalimbikitsa anthu kutengera masitayelo osapatsa ulemu, olimbikitsa chiwerewere, ndiponso achilendo omwe si oyenera. (1 Yoh. 2:15-17) Choncho, posankha zochita pankhani ya zovala ndi kudzikongoletsa, tifunika kutsatira langizo la m’Baibulo lakuti ‘tikane chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, tikhale ndi moyo m’dziko lino odziletsa.’ (Tito 2:12) Sitikufuna kukhumudwitsa ena mwa maonekedwe athu, kaya ndi abale athu, anthu ogwira ntchito pa lesitilanti, kapena otiona.—1 Akor. 10:32, 33.
3. Kodi ndi mafunso ati amene angatithandize kupenda maonekedwe athu?
3 Zovala Zopatsa Ulemu Ndiponso Zoyenera: Pokonzekera msonkhano wachigawo dzifunseni kuti: ‘Kodi zovala zanga n’zopatsa ulemu, kapena zimapangitsa anthu kuchita nane chidwi monyanyira? Kodi zimasonyeza kulemekeza maganizo a ena? Kodi mabulauzi anga ndi a makosi akuluakulu oonetsa pamtima kapenanso kodi mabulauziwo ndi aafupi kwambiri? Kodi madiresi anga ndi oonetsa m’kati kapena othina? Kodi zovala zanga n’zoyera ndiponso zopanda fungo loipa? Kodi panthaŵi yopuma mapulogalamu akatha, ndizikaoneka bwino ndi mwaukhondo monga momwe mtumiki amafunika kuonekera, kapena kodi zovala zanga zizikaoneka zauve, za mafashoni, zosayenerana ndi munthu wopezeka pamsonkhano wachigawo wovala baji? Kodi zovala zimene ndizikavala panthaŵi yopuma sizikandichititsa manyazi polalikira mwamwayi?’—Aroma 15:2, 3; 1 Tim. 2:9.
4. Kodi anthu ena angatithandize bwanji kuti tizioneka bwino?
4 Tingapindule mwa kumva maganizo a Akristu achikulire. Akazi okwatiwa azifunsa amuna awo mmene ena angaonere zovala zawo. Makolo oopa Mulungu angathandize ana awo achinyamata pankhani imeneyi. Ndiponso, alongo achikulire aulemu ‘angalangize akazi aang’ono . . . akhale odziletsa, odekha’ m’maonekedwe awo “kuti mawu a Mulungu angachitidwe mwano.” (Tito 2:3-5) Zofalitsa zathu zili ndi zithunzi zothandiza zosonyeza mavalidwe opatsa ulemu ndiponso oyenera.
5. Kodi tonse tingalemekeze bwanji Yehova panthaŵi yamsonkhano?
5 Lemekezani Yehova: Misonkhano yachigawo imapereka mpata wabwino wolemekeza Yehova kwa tonse, osati amene ali m’mapulogalamu okha. Ndi zoona kuti zochita ndi zolankhula zathu zachikristu zidzamulemekeza. Koma chinthu choyamba chimene otiona ambiri amaona pa ife ndi kuvala ndi kudzikongoletsa kwathu. Tonse tilemekeze Yehova mwa kuoneka bwino ndiponso modzilemekeza.—Sal. 148:12, 13.
[Bokosi patsamba 6]
Zotithandiza Kuoneka Modzilemekeza
◼ Mawu a Mulungu
◼ Kudzipenda
◼ Kumva maganizo a ena
◼ Zofalitsa zachikristu