Kodi Tingathandize Bwanji Anthu Obwera pa Chikumbutso?
1. Kodi ndi umboni wamphamvu uti umene udzaperekedwa pa March 22, 2008?
1 Pa March 22, 2008, anthu ambirimbiri padziko lonse lapansi, adzapatsidwa umboni wamphamvu. Anthu amene adzapezeke pa Chikumbutso, adzamva za chikondi chachikulu chimene Yehova anasonyeza mwa kupereka dipo ku mtundu wa anthu. (Yoh. 3:16) Adzaphunzira za Ufumu ndi mmene Yehova adzagwiritsire ntchito Ufumuwo, pokwaniritsa chifuniro chake padziko lonse lapansi. (Mat. 6:9, 10) Adzadzionera okha chikondi ndi umodzi wa anthu a Mulungu ndiponso adzazimva kuti alandiridwa bwino.—Sal. 133:1.
2. Kodi tingathandize bwanji ophunzira Baibulo amene abwera pa Chikumbutso?
2 Ophunzira Baibulo: Ena mwa anthu odzapezeka pa Chikumbutso adzakhala anthu amene tayamba kuphunzira nawo Baibulo posachedwa. Adziwikitseni kwa abale ndi alongo. Afotokozereni za misonkhano yonse imene imachitika pa mlungu, ndipo asonyezeni malo ena ndi ena pa Nyumba ya Ufumu. Mu nkhani yake, wokamba nkhani adzalimbikitsa anthu amenewa kuti apitirize kukulitsa ubwenzi wawo ndi Yehova. Mungagwiritsire ntchito mfundo za m’nkhani yakeyo kulimbikitsa ophunzira anu.
3. Kodi tingalimbikitse bwanji ofalitsa osalalikira amene abwera pa Chikumbutso?
3 Ofalitsa Omwe Anasiya Kulalikira: Anthu ena amene adzabwere ndi amene anasiya kulalikira. Yesetsani kuwalonjera mwachikondi. Pewani kuwafunsa mafunso ndi kulankhula zinthu zimene zingawachititse manyazi. Pambuyo pa nthawi yochepa Chikumbutso chitatha, akulu angakonze zoyendera wofalitsa wosalalikira aliyense amene anabwera ku Chikumbutso. Angawayamikire chifukwa cha kuyesetsa kwawo kupezekapo, ndi kuwapempha mwachikondi kuti adzabwere ku msonkhano wa mpingo wotsatira.
4. Kodi tonsefe tingathandize bwanji alendo?
4 Alendo: Anzathu kapena achibale anthu amene tinawaitana angadzabwerenso pa mwambowu. Ena angakhale kuti anaitanidwa pa ntchito yapadera yoitanira anthu ku Chikumbutso. Mukaona anthu achilendo, yesetsani kuwalonjera ndi kuwalandira. N’kutheka kuti kameneka kangakhale koyamba kupezeka pa misonkhano yathu. Pocheza nawo mungadziwe mmene mungawapezere. Pakadutsa masiku ochepa Chikumbutso chitachitika, mungawayendere kapena kuwaimbira telefoni. Zimenezi zingathandize kuti akulitse chidwi chawo chofuna kudziwa zambiri ndipo mungawapemphe kuti muziphunzira nawo Baibulo.
5. Kodi tinganene chiyani kuti tiyambitse phunziro la Baibulo?
5 Tingagwiritsire ntchito mfundo za mu nkhani ya Chikumbutso pogawira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani pa ulendo wobwereza. Mwachitsanzo, wokamba nkhani ya Chikumbutso adzawerenga lemba la Yesaya 65:21-23. Ndiyeno pa ulendo wobwereza, mungatchule za nkhaniyo kuti: “Ndingakuonetseni madalitso ena amene dipo lingakubweretsereni?” Kenako kambiranani tsamba 4 ndi 5 m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Kapena munganene kuti, “Anthu ambiri sadziwa nthawi imene ulosi wa Yesaya umenewu udzakwaniritsidwe.” Ndipo kambiranani ndime 1 mpaka 3 m’mutu 9 wa bukuli. Njira ina imene tingayambitsire phunziro la Baibulo ndi kukambirana mfundo za m’nkhani ya Chikumbutso ndi munthuyo, kenako kumuonetsa buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndi kumusonyeza mmene timaphunzirira.
6. Kodi ndi mipata yotani imene tili nayo pamene tikumvera lamulo la Yesu lokumbukira imfa yake?
6 Tonsefe, tiyeni tifunefune mipata yothandizira ophunzira Baibulo, ofalitsa amene anasiya kulalikira, ndi alendo amene adzapezeke pa Chikumbutso. (Luka 22:19) Mosakayikira, Yehova adzadalitsa khama lathu pa ntchito ya Ufumu.