Alandireni Bwino
1. Kodi tidzakhala ndi mwayi wochitira umboni pa tsiku liti, ndipo n’chifukwa chiyani tikutero?
1 Pa Chikumbutso, timakhala ndi mwayi wabwino kwambiri wochitira umboni. Chaka chino, tikuyembekezera kuti alendo oposa 10 miliyoni adzapezeka pa Chikumbutso kuti adzamve za chikondi chachikulu kwambiri chimene Yehova ndi Yesu anasonyeza popereka dipo. (Yoh. 3:16; 15:13) Anthuwa adzaphunzira za madalitso amene angalandire chifukwa cha mphatso ya Yehova imeneyi. (Yes. 65:21-23) Komatu si wokamba nkhani yekha amene adzachitire umboni pa tsikuli. Anthu onse opezeka pa Chikumbutso adzathanso kuchitira umboni wamphamvu akamalandira bwino alendo.—Aroma 15:7.
2. Kodi tingatani posonyeza kuti tikulandira bwino alendo?
2 Mungachite bwino kulankhula ndi anthu amene akhala nanu pafupi m’malo mongokhala chete pampando n’kumadikira kuti mwambowu uyambe. Nthawi zambiri alendo amachita mantha ndiponso sadziwa zimene zichitike pa mwambowu. Choncho, iwo angakhale omasuka ngati titawamwetulira ndiponso kuwapatsa moni mwansangala. Komanso kuti tidziwe ngati munthu wina wafika pa mwambowu chifukwa choti analandira kapepala, tingachite bwino kumufunsa kuti tidziwe ngati n’koyamba kuti iye apezeke pa msonkhano wathu, kapenanso ngati akudziwa munthu aliyense wa mumpingo wathu. Mwinanso mungamupemphe kuti akhale nanu pafupi n’cholinga choti aziwerenga nawo malemba m’Baibulo lanu komanso aziona nawo buku lanu la nyimbo. Ngati mwambo wa Chikumbutso ukuchitikira pa Nyumba ya Ufumu, mungachite bwino kumuonetsa mwachidule malo osiyanasiyana panyumbayo. Nkhani ya Chikumbutso ikatha, chezani naye kuti muyankhe mafunso alionse amene iye angakhale nawo. Ngati pambuyo pa Chikumbutso mukufunika kuchoka mwamsanga n’cholinga choti mpingo winanso uchite mwambowu pamalowo, mwina munganene kuti: “Ndikufuna kumva kuti kodi mwambowu mwauona bwanji? Kodi tingadzapezane bwanji?” Kenako gwirizanani kuti mudzakumane kapena kulankhulana tsiku lina. Makamaka akulu ayenera kukhala tcheru kuti alimbikitse ofalitsa amene anasiya kulalikira, omwe adzapezeke pa mwambowu.
3. N’chifukwa chiyani ifeyo tiyenera kuyesetsa kudzalandira bwino alendo pa Chikumbutso?
3 Alendo ochuluka adzapezeka pa mwambowu, ndipo kwa ambiri, imeneyi idzakhala nthawi yawo yoyamba kulawa nawo madalitso amene Yehova amatipatsa m’paradaiso wauzimu. Iwo adzaona kuti ndife anthu osangalala, amtendere ndiponso ogwirizana. (Sal. 29:11; Yes. 11:6-9; 65:13, 14) Kodi n’chiyani chimene alendowo azidzakumbukira pambuyo pa mwambowu? Iwo angakumbukire kwambiri zimene ifeyo tinachita powalandira bwino.