Umboni Wamphamvu Udzaperekedwa
1. Kuwonjezera pa nkhani, kodi alendo amachita chidwi ndi chiyani pa Chikumbutso? Fotokozani.
1 Liti? Pa tsiku la Chikumbutso. Tachita khama kwambiri kuitana anthu kuti adzakhale nafe. Alendo amene adzabwere adzachita chidwi kwambiri ndi zimene adzamve. Komatu si zokhazo. Mayi wina amene anapita ku Chikumbutso ananena zimene anaona kumeneko. Iye ananena kuti aliyense anali wansangala. Ananenanso kuti nyumba imene anasonkhanamo, yomwe inamangidwa ndi anthu ongodzipereka, inali yokongola, yaukhondo ndi yosamalidwa bwino. Choncho kuwonjezera pa wokamba nkhani, tonsefe timapereka umboni pa mwambo wapachaka wofunika kwambiri umenewu.—Aef. 4:16.
2. Kodi aliyense angachite chiyani kuti adzapereke umboni kwa alendo?
2 Perekani Moni Mwachimwemwe kwa Alendo: Tingapereke umboni wabwino kwa alendo powamwetulira ndi kuwapatsa moni mwansangala. (Yoh. 13:35) Ngakhale kuti simungathe kulankhula ndi mlendo aliyense, mungathe kupereka moni mwansangala kwa anthu amene adzakhale nanu pafupi ndi kuwauza dzina lanu. (Aheb. 13:1, 2) Mudzakhale tcheru kuti mudzathandize alendo ooneka kuti ali okhaokha. Anthu otero ayenera kuti anapatsidwa kapepala kowaitanira ku Chikumbutso. Choncho, mungawafunse kuti: “Kodi n’koyamba kubwera kuno?” Apempheni kuti mukhale nawo pamodzi. Mungawapemphenso kuti ngati ali ndi funso lililonse angakufunseni. Ngati mpingo wanu ukufunika kuchoka mofulumira pamalopo kuti mpingo wina uchitireponso Chikumbutso, mungamufunse kuti: “Kodi mwauona bwanji mwambowu? Kodi ndingakupezeni bwanji?”
3. Kodi ofalitsa amene sabwera kumisonkhano tidzawalandire bwanji?
3 Alandireni ndi Manja Awiri Ofalitsa Amene Sabwera Kumisonkhano: Sitikukayika kuti ofalitsa amene sabwera kumisonkhano, kuphatikizapo amene amangobwera ku Chikumbutso kokha, adzafika pa Chikumbutsochi. Anthu oterewa akadzafika, mudzawalandire ndi manja awiri ndipo mudzawauze kuti mwasangalala kwambiri kuwaona. (Aroma 15:7) Pambuyo pake, akulu angapite kunyumba kwawo mwamsanga kukawalimbikitsa kuti apitirize kusonkhana ndi mpingo. Tikufunitsitsa kuti anthu ambiri amene adzabwere ku Chikumbutso, adzalimbikitsidwe ndi kutamanda Mulungu chifukwa cha zimene adzamve ndi kuona, ‘pokhala mboni zomwe zidzaone zochita zathu zabwino.’—1 Pet. 2:12.