Ndandanda ya Mlungu wa April 18
MLUNGU WOYAMBIRA APRIL 18
Nyimbo Na. 17 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 5 ndime 16-20 ndi bokosi patsamba 55 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yobu 28-32 (Mph. 10)
Na. 1: Yobu 30:1-23 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Ngati Wina Anena Kuti: “Simumakhulupirira Yesu”—rs tsa. 433 ndime 1-3 (Mph. 5)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuganiza Kaye Tisanalankhule?—Miy. 16:23 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Pamene Ena Afunsa Chifukwa. Nkhani yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 177 ndime 3, mpaka kumapeto kwa tsamba 178. Chitani chitsanzo chosonyeza wofalitsa akufunsidwa funso ndi munthu wosakhulupirira amene amagwira naye ntchito. Funsolo likhale lokhudza zikhulupiriro zathu. Wofalitsayo azilankhula yekha akuganizira mmene angayankhire funsolo. Kenako ayankhe funsolo.
Mph. 10: Bokosi la Mafunso. Nkhani yokambirana yokambidwa ndi mkulu.
Mph. 10: Njira Zolalikirira Uthenga Wabwino: Kulalikira Nyumba Ndi Nyumba. Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Gulu, tsamba 92 ndime 3, mpaka tsamba 95 ndime 2. Funsani wofalitsa mmodzi kapena awiri amene amalalikira kunyumba ndi nyumba ngakhale kuti ali ndi mavuto ena monga matenda kapena manyazi. Kodi apindula motani chifukwa cha khama lawo?
Nyimbo Na. 26 ndi Pemphero